Mauthenga a Katolika pa Tsiku Lililonse

Tiyankhuleni Ambuye

Daily Catholic homilies and liturgical reflections in Chichewa — nourishing faith, one homily at a time

Watch Today's Homily Subscribe for Updates

New homily every day

667+ Homilies · Daily New Content · Chichewa Language · Free Always

Recent Homilies

Explore our collection of daily reflections

LACHISANU LAMULUNGU WA 28 PA CHAKA

Fr. Francis Lekaleka, DP

2026-10-16

MAU OYAMBA: AEFESO 1:11-14 SALIMO 33: 1-2,4-5. 12-13 MTHENGA : LUKA 12:1-7

16 OCTOBER, 2026 LACHISANU LAMULUNGU WA 28 PA CHAKA KULEMEKEZA MARGARETI MARIA ALACOQUE WOYERA MAU A MKALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO 1:11-14 Abale, Mulungu amaongolera zinthu zonse monga momwe Iye wafunira ndi m'mene watsimikizira. Iye adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale akeake. Adazikonzeratu kuti ziyenera kukhala choncho. Adafuna kuti ife, amene tinali oyamba kuyembekeza Khristu, tilemekeze ulemerero wake. Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza. Mzimu Woyerayo ndiye chikole chotsimikizira kuti tidzalandiradi madalitso onse amene Mulungu adalonjeza kupatsa anthu ake, ndipo kuti akhale ake enieni. Cholinga cha zonsezi ndi chakuti tilemekeze ulemerero wake. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 33: 1-2,4-5. 12-13 Ngwodala mtundu wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta Kondwerani mwa Chauta, inu anthu ake. Zoonadi ochita zolungama azitamanda. Tamandani Chauta ndi pangwe. Muimbireni nyimbo ndi zeze wa nsambo khumi Mau a Chauta ndi olungama, zochita zake zonse amazichita mokhulupirika. Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera. Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi. Ngwodala mtundu wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta, anthu amene Chauta waŵasankha ake ake. Chauta ali Kumwamba, amayang'ana pansi ndi kuwona anthu onse. Aleluya: Atate, mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira, nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira. Aleluya. MTHENGA WABWINO WA LUKA 12:1-7 Nthaŵi ina, chikhamu cha anthu masauzande ambiri chidasonkhana, kotero kuti anthuwo ankangopondana. Yesu adayamba kulankhula ndi ophunzira ake poyamba, adati: “Chenjerani ndi chofufumitsira buledi cha Afarisi, chimene chili chiphamaso. Kanthu kalikonse kovundikirika kadzaululika, ndipo kalikonse kobisika kadzadziŵika. Nchifukwa chake zonse zimene mwalankhula mu mdima, zidzamveka poyera, ndipo zonse zimene mwanong’oneza anthu mkati mwa nyumba, adzazilengeza pa bwalo. Ndikukuuzani inu, abwenzi anga, kuti musamaopa anthu. Iwo angathe kupha thupi lokha, koma pambuyo pake alibenso china choti angachitepo. Koma ndikuchenjezeni: amene muyenera kumuopa ndi Mulungu. Iye atalanda moyo wa munthu, ali nazonso mphamvu za kumponya mu Jehena. Ndithu ndi ameneyo amene muzimuopa. Suja amagulitsa mpheta zisanu tindalama tiŵiri? Komabe Mulungu saiŵala ndi imodzi yomwe. Ndipo tsitsi lomwe la ku mutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziopa ayi. Ndinu a mtengo woposa mpheta zambiri.” Mthenga wa Ambuye

LACHINAYI LAMULUNGU WA 28 PACHAKA

Fr. Francis Lekaleka, DP

2026-10-15

MAU OYAMBA : AEFESO 1:1-10 SALIMO 98: 1, 2-3AB, 3CD-4, 5-6 MTHENGA WABWINO : LUKA 11:47-54

15 OCTOBER, 2026 LACHINAYI LAMULUNGU WA 28 PACHAKA (II) KULEMEKEZA TEREZA WA YESU WOYERA TSIKU LOKUMBUKIRA ANAKUBALA MAU OYAMBA; MAU A MKALATA YA PAULO KWA KWA AEFESO 1:1-10 Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa kufuna kwa Mulungu. Ndikulembera anthu a Mulungu, amene ali ku Efeso, amenenso ali okhulupirika mwa Khristu Yesu. Mulungu Atate athu, ndi Ambuye Yesu Khristu, akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu, Yesu Khristu. Mwa Khristu, Iye adatipatsa madalitso onse auzimu Kumwamba. Mulungu asadalenge dziko lapansi, adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima, ndi opanda cholakwa pamaso pake. Chifukwa chotikonda, adakonzeratu kuti, mwa Yesu Khristu, atilandire ngati ana ake. Adachita zimenezi chifukwa adafuna kutero mwa kukoma mtima kwake. Adafuna kuti tizitamanda ulemu wake, chifukwa adatikomera mtima kopambana, pakutipatsa Mwana wake wokondedwa ngati mphatso yaulere. Ndi imfa ya Mwana wakeyo, Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere zimene Mulungu adatipatsa mochuluka. Mwa luntha ndi nzeru, adatiwululira chifuniro chake chimene kale chidali chobisika. Zimene adati achite mwa kukoma mtima kwake, ndi zomwe Iye Mwini adakonzeratu kale. Chimene Mulungu adalongosola kuti achite, itakwana nthaŵi, nchakuti asonkhanitse pamodzi mwa Khristu zinthu zonse za Kumwamba ndi zapansi pano. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 98: 1, 2-3AB, 3CD-4, 5-6 Chauta wadziwitsa anthu ake onse za chipulumutso chake (2a). Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, Popeza kuti wachita zodabwitsa. Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa. Chauta wadziwitsa anthu ake onse za chipulumutso chake. Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo, Waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse Kuti Iye ndi wolungama. Wakumbukira chikondi chake chosasinthika Ndi kukhulupirika kwake pa fuko la Israele. Chauta wadziwitsa anthu ake onse za chipulumutso chake. Anthu aku mathero a dziko lonse lapansi Aona chipulumutso cha Mulungu wathu. Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi. Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda. Chauta wadziwitsa anthu ake onse za chipulumutso chake. Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe, Lizani pangwe ndi nyimbo zokoma. Imbirani Chauta Mfumu, Imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete. Chauta wadziwitsa anthu ake onse za chipulumutso chake. Aleluya: (Yohane 14: 6) Ine ndine njira, ndine choona, ndiponso moyo, akutero Ambuye; palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA 11:47-54 Ambuye adati: “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo, chifukwa mumamanga ziliza za aneneri, pamene ndi makolo anu omwe akale amene adapha aneneriwo. Apo mukutsimikiza kuti mukuvomereza ntchito za makolo anuwo, popeza kuti iwowo adapha aneneriwo, inuyo nkumamanga ziliza zawo. Nchifukwa chake Nzeru ya Mulungu idati: ‘Ndidzaŵatumizira aneneri ndi Atumwi, koma anthu adzapha ena mwa iwo, nkuzunza ena.’ Motero anthu amakono adzakhala ndi mlandu chifukwa cha aneneri onse amene adaphedwa chilengedwere dziko lapansi, kuyambira kuphedwa kwa Abele, mpaka kuphedwa kwa Zakariya, amene adaphedwera m’Nyumba ya Mulungu, pakati pa guwa la nsembe ndi malo opatulika kopambana. Ndithu ndikunenetsa kuti anthu amakono adzakhaladi ndi mlandu chifukwa cha ophedwawo. Muli ndi tsoka, inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mudalanda makiyi otsekulira anthu nzeru. Inu nomwe sumudaloŵe, ndipo mudatsekereza amene ankafuna kuloŵa.” Pamene Yesu adatuluka m’nyumbamo, aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi Afarisi adayamba kumuzonda ndi kumpanikiza ndi mafunso ambiri ozunguza. Cholinga chawo chidali chofuna kumtapa mkamwa. Mthenga wa Ambuye

LACHITATU LAMULUNGU WA 28 PACHAKA

Fr. Francis Lekaleka, DP

2026-10-14

MAU OYAMBA : 5:18-25 SALIMO 1: 1-2, 3, 4 NDI 6 MTHENGA WABWINO : LUKA 11:42-46

14 OCTOBER, 2026 LACHITATU LAMULUNGU WA 28 PACHAKA (II) MAU OYAMBA; MAU A MKALATA YA PAULO KWA AGALATIYA 5:18-25 Okondedwa, ngati Mzimu Woyera akutsogolerani, ndiye kuti sindinunso akapolo a Malamulo a Mose. Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, mapokoso apa mowa, ndinso kuledzera maphwando a chipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu. Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m’moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa. Amene ali ake a Khristu Yesu, adalipachika pa mtanda khalidwe lawo lokonda zoipa, pamodzi ndi zokhumba zake ndi zilakolako zake. Ngati Mzimu Woyera adatipatsa moyo, tilolenso kuti Mzimu yemweyo azititsogolera. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 1: 1-2, 3, 4 NDI 6 Munthu wotsata Ine adzakhala nako kuŵala komutsogolera ku moyo (Yohane 8: 12). Ngodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, Wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, Wosakhala nawo m’gulu la anthu onyoza Mulungu, Koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, Nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku. Munthu wotsata Ine adzakhala nako kuŵala komutsogolera ku moyo. Munthuyo ali ngati mtengo Wobzalidwa m’mbali mwa mtsinje wa madzi, Ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, Umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino. Munthu wotsata Ine adzakhala nako kuŵala komutsogolera ku moyo. Anthu oipa sali choncho, Ali ngati mankhusu wouluzika ndi mphepo. Paja Chauta amaŵasamalira anthu ake, Koma anthu ochimwa adzaonongeka. Munthu wotsata Ine adzakhala nako kuŵala komutsogolera ku moyo. Aleluya: (Yohane 10: 27) Nkhosa zanga zimamva mawu anga. Ine ndimazidziŵa, ndipo zimanditsatira, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA 11:42-46 Ambuye adati: ”Muli ndi tsoka, inu Afarisi, chifukwa mumapereka chachikhumi cha timbewu tonunkhira, cha timbewu tokometsera chakudya, ndiponso cha mbewu za ku dimba za mtundu uliwonse. Koma simulabadako kuchita chilungamo, kapena kukonda Mulungu. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo. Muli ndi tsoka, inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yaulemu m’nyumba za mapemphero, ndiponso kuti anthu azikupatsani moni waulemu pa misika. Muli ndi tsoka, chifukwa muli ngati manda obisika, amene anthu amapondapo osadziŵa kanthu.” Apo katswiri wina wa Malamulo adati: “Aphunzitsi, mukamanena zimenezi, muli kunyozatu ndi ife tomwe.” Yesu adati: “Muli ndi tsokanso, inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mumasenzetsa anthu katundu wosautsa kunyamula, pamene inuyo simumkhudzako mpang’ono pomwe.” Mthenga wa Ambuye

LACHIWIRI LAMULUNGU WA 28 PACHAKA

Fr. Francis Lekaleka, DP

2026-10-13

MAU OYAMBA : AGALATIYA 5:1-6 SALIMO 119: 41, 43, 44, 45, 47, 48 MTHENGA WABWINO : LUKA 11:37-41

13 OCTOBER, 2026 LACHIWIRI LAMULUNGU WA 28 PACHAKA (II) MAU OYAMBA; MAU A MKALATA YA PAULO KWA AGALATIYA 5:1-6 Okondedwa, Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso mu goli la ukapolo. Ndiye mvetsani, ine, Paulo, ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ayi. Ndikufuna kubwerezanso kuuza aliyense woumbalidwa, kuti ayenera kutsata Malamulo onse a Mose. Inu amene mukuyesa kusanduka olungama pakutsata Malamulowo, mudadzipatula nokha kusiya Khristu. Pamenepo mudalekana ndi madalitso aulere a Mulungu. Koma kunena za ife, chifukwa cha kulandira Mzimu Woyera ndiponso pakukhulupirira, tikuyembekeza kuti Mulungu adzationa kuti ndife olungama pamaso pake. Pakuti pamene tili mwa Khristu Yesu, kuumbalidwa kapena kusaumbalidwa kulibe kanthu, chachikulu nchakuti munthu akhale ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 119: 41, 43, 44, 45, 47, 48 Inu Chauta, mutikonde ndi chikondi chanu chosasinthika (41a). Chauta, mundikonde ndi chikondi chanu chosasinthika, Mundipulumutse monga momwe mudalonjezera. Inu Chauta, mutikonde ndi chikondi chanu chosasinthika. Pakamwa panga musapaletse mpang’ono pomwe Kulankhula mawu anu oona, Pakuti ndimakhulupirira malangizo anu. Ndidzatsata malamulo anu kosalekeza mpaka muyaya. Inu Chauta, mutikonde ndi chikondi chanu chosasinthika. Ndidzayenda ndi ufulu, Chifukwa ndasamala malamulo anu. Inetu ndimasangalala ndi malamulo anu, amene ndimaŵakonda. Inu Chauta, mutikonde ndi chikondi chanu chosasinthika. Ndimalemekeza malamulo anu amene ndimaŵakonda, Ndipo ndimasinkhasinkha za malamulowo. Inu Chauta, mutikonde ndi chikondi chanu chosasinthika. Aleluya: (Aheberi 4: 12) Mawu a Mulungu ndi a moyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu, ndipo amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m’mitima mwawo, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA 11:37-41 Yesu atatsiriza kulankhula, wina wa m’gulu la Afarisi adamuitana kuti akadye naye. Tsono Yesu adaloŵa m’nyumba nakakhala podyera. Mfarisiyo adadabwa poona kuti Yesu wayamba kudya osatsata mwambo wawo wa kasambidwe ka m’manja. Koma Ambuye adamuuza kuti: “Inu Afarisi mumatsuka kunja kwa chikho ndi mbale, koma mkati ndinu odzaza ndi zonyenga ndi zankhanza. Ndinu anthu opusa! Kodi Mulungu amene adapanga zakunja, si yemweyo adapanganso zamkati? Popereka zachifundo kwa amphaŵi, muzipereka zimene zili mkati, ndiye pamenepo zanu zonse zidzakhala zoyera.” Mthenga wa Ambuye

LOLEMBA LAMULUNGU WA 28 PACHAKA

Fr. Francis Lekaleka, DP

2026-10-12

MAU OYAMBA : AGALATIYA 4:22-24,26-27,31-5:1 SALIMO 113: 1B-2, 3-4, 5A NDI 6-7 MTHENGA WABWINO : LUKA 11:29-32

12 OCTOBER, 2026 LOLEMBA LAMULUNGU WA 28 PACHAKA (II) MAU OYAMBA; MAU A MKALATA YA PAULO KWA AGALATIYA 4:22-24,26-27,31-5:1 Okondedwa, paja Malembo akuti: Abrahamu adali ndi ana aamuna aŵiri: wina mayi wake adali kapolo, winayo mayi wake adali mfulu. Mwana amene mayi wake adali kapolo uja, adabadwa monga momwe amabadwira ana onse. Koma mwana wina uja, amene mayi wake adali mfulu, adabadwa chifukwa cha lonjezo la Mulungu. Zimenezi zili ngati fanizo. Akazi aŵiri aja akufanizira zipangano ziŵiri. Mmodzi (Hagara uja), ndi wochokera ku phiri la Sinai, ndipo ana ake amakhala akapolo. Koma Yerusalemu wa Kumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mayi wathu. Paja Malembo akuti: “Sangalala iwe chumba, imba nthungululu, fuula mokondwera, iwe amene sudachemberepo. Ana a mkazi wosiyidwa ndi ochuluka koposa ana a mkazi amene ali naye mwamuna.” Nchifukwa chake, abale, ife sindife ana a kapolo, ndife ana a mfulu. Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso mu goli la ukapolo. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 113: 1B-2, 3-4, 5A NDI 6-7 Dzina la Chauta litamandike mpaka muyaya (2). Tamandani Chauta! Mtamandeni, inu atumiki ake, Tamandani dzina la Chauta. Yamikani Chauta kuyambira tsopano mpaka muyaya. Dzina la Chauta litamandike mpaka muyaya. Dzina la Chauta litamandike Kuyambira ku matulukiro a dzuŵa, mpaka ku maloŵero ake. Chauta akulamulira anthu a mitundu yonse, Ulemerero wake ndi waukulu kuposa wa mlengalenga. Dzina la Chauta litamandike mpaka muyaya. Ndani angalingane ndi Chauta, Mulungu wathu, Wochita kuŵeramira pansi Poyang’ana mlengalenga ndi dziko lapansi. Amakweza munthu wosauka kuchokera ku fumbi, Ndipo amatulutsa ku dzala anthu osoŵa. Dzina la Chauta litamandike mpaka muyaya. Aleluya: (Salimo 95: 8) Ambuye akuti: lero mukadamverako mawu ake! Musaumitse mitima yanu, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA 11:29-32 Pamene anthu ankachulukirachulukira, Yesu adati: “Anthu a mbadwo uno ngoipa, amafuna kuona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzachiona chizindikirocho, kupatula cha Mneneri Yona chija. Monga Yona uja adali chizindikiro kwa anthu aku Ninive, chomwechonso Mwana wa Munthu adzakhala chizindikiro kwa anthu a mbadwo uno. Pa tsiku la chiweruzo, mfumukazi ya kumwera ija idzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nidzaŵatsutsa. Paja iyo idachita kuchokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva zolankhula zanzeru za Mfumu Solomoni. Ndipotu pano pali woposa Solomoni amene. Pa tsiku la chiweruzo, anthu aku Ninive aja adzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzaŵatsutsa. Paja iwowo adatembenuka mtima, atamva malaliko a Yona. Ndipotu pano pali woposa Yona amene.” Mthenga wa Ambuye

All Homilies

Latest News

Reports and updates from the ministry

Read all news

Liturgical Calendar

Follow the rhythm of the Church's liturgical year

This Week's Schedule

Sun 11 Ordinary Time Mon 12 Ordinary Time Tue 13 Ordinary Time Wed 14 Ordinary Time Thu 15 Ordinary Time Fri 16 Ordinary Time Sat 17 Ordinary Time

Video available · Today

Never Miss a Daily Homily

Get notifications when new homilies are posted

We respect your privacy. Unsubscribe at any time.