LOLEMBA LA MULUNGU WA 10 PA CHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Gift Phiri, OFM for 8 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Gift Phiri, OFM·8 June 2026·11:44·2 views
Ordinary Time
BUKU LOYAMBA LA MAFUMU 17:1-6 SALIMO 121: 1BC-2, 3-4, 5-6, 7-8 MATEYU WOYERA 5:1-12

Mau a Mulungu a Lero

8 JUNE, 2026 LOLEMBA LA MULUNGU WA 10 PA CHAKA MAU WOYAMBA A MBUKU LOYAMBA LA MAFUMU 17:1-6 Mneneri Eliya wa ku Tisibe ku Giliyadi, adauza Ahabu kuti: “Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene ndimamtumikira, akuti: sipakhala mame kapena mvula zaka zikubwerazi, mpaka ine nditanena.” Kenaka Chauta adauza Eliyayo kuti: “Chokako kuno, upite chakuvuma, ukabisale ku mtsinje wa Keriti, kuvuma kwa Yordani. Uzikamwa mu mtsinjemo, ndipo ndalamula makwangwala kuti azikakudyetsa kumeneko.” Choncho Eliyayo adapita nakachita monga momwe Chauta adanenera. Adapita nakakhala m’mbali mwa mtsinje wa Keriti, kuvuma kwa Yordani. Tsono makwangwala ankadzampatsa buledi ndi nyama m’maŵa ndi madzulo. Ndipo ankamwa madzi ku mtsinjeko. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 121: 1BC-2, 3-4, 5-6, 7-8 Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga Kumwamba ndi dziko lapansi (2). Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, Amene adalenga Kumwamba ndi dziko lapansi. Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga Kumwamba ndi dziko lapansi. Sadzalola phazi lako kuti literereke, Iye amene amakusunga sadzaodzera. Zoonadi, amene amasunga Israele, Ndithu sadzaodzera kapena kugona. Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga Kumwamba ndi dziko lapansi. Chauta ndiye amene amakusunga, Chauta ndiye mtetezi wako, ali ku dzanja lako lamanja. Dzuŵa silidzakupweteka masana, Mwezi sudzakuvuta usiku. Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga Kumwamba ndi dziko lapansi. Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, Adzasamala moyo wako. Chauta adzakusunga kuli konse kumene udzapita, Kuyambira tsopano mpaka muyaya. Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga Kumwamba ndi dziko lapansi. Aleluya: (Mateyo 5: 11) Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunamizirani zoipa za mitundumitundu, chifukwa cha Ine. Sangalalani chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba, Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU WOYERA 5:1-12 Yesu poona chikhamu cha anthu, adakwera pa phiri. Iye atakakhala pansi, ophunzira ake adamtsatira pomwepo. Kenaka adayamba kuŵaphunzitsa, adati: “Ngodala anthu amene ali osauka mu mtima mwawo, pakuti Ufumu wa Kumwamba ndi wawo. Ngodala anthu amene akumva chisoni, pakuti Mulungu adzaŵasangalatsa. Ngodala anthu ofatsa, pakuti Mulungu adzaŵapatsa dziko la pansi pano kuti likhale lawo. Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzawakhutitsa. Ngodala anthu ochitira anzawo chifundo, pakuti iwonso Mulungu adzaŵachitira chifundo. Ngodala anthu oyera mtima, pakuti adzaona Mulungu. Ngodala anthu odzetsa mtendere, pakuti Mulungu adzaŵatcha ana ake. Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wa Kumwamba ndi wawo. Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa za mitundumitundu chifukwa cha Ine. Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m’menenso anthu ankazunzira aneneri amene adalipo kale inu musadabadwe.” Mthenga wa Ambuye