LACHITATU LAMULUNGU WA CHINAYI MU PASAKA - 29 APRIL, 2026
Chichewa Transcript
29 APRIL, 2026 Kulemekeza Katalina wa Ku Siena Woyera LACHITATU LAMULUNGU WA CHINAYI MU PASAKA MAU OYAMBA, MAU A MBUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI 12:24-13:5a Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira. Mawu a Mulungu adanka nafalikirafalikira. Tsono Barnabasi ndi Saulo atatula zachifundo zija, zimene adaŵatumira ku Yerusalemu, adabwerako. Adatengako Yohane wotchedwa Marko uja. Mu mpingo wa ku Antiyokeya mudali alaliki ndi aphunzitsi aŵa: Barnabasi, Simeoni (wotchedwa Wakuda), Lusiyo wa ku Kirene, Manayene (amene adaleredwa pamodzi ndi bwanamkubwa Herode), ndiponso Saulo. Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti: “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.” Tsono atasala zakudya ndi kupemphera, adaŵasanjika manja naŵatuma. Barnabasi ndi Saulo, otumidwa ndi Mzimu Woyera aja, adapita ku Seleukiya. Kuchokera kumeneko adayenda m‟chombo nakafika ku chilumba cha Kipro. Atafika ku mzinda wa Salami, adalalika mawu a Mulungu m‟nyumba za mapemphero za Ayuda. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 67: 2-3, 5, 6, 8 Mitundu yonse ya anthu ikutamandeni, Inu Chauta (4). Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa, Mutiunikire ndi chikondi chanu, Njira yanu idziŵike pa dziko lonse lapansi, Chipulumutso chanu chidziŵike pakati pa mitundu yonse. Mitundu yonse ya anthu ikutamandeni, Inu Chauta. Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Chauta, Mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni. Mitundu ya anthu isangalale ndi kuimba ndi chimwemwe, Chifukwa Inu mumaweruza anthu mwachilungamo, Ndi kuŵatsogolera pa dziko lapansi. Mitundu yonse ya anthu ikutamandeni, Inu Chauta. Mitundu yonse ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, Mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni. Inde, Mulungu watidalitsa, Anthu onse aku mathero a dziko lapansi apembedze Iye. Mitundu yonse ya anthu ikutamandeni, Inu Chauta. Aleluya: (Yohane 8: 12) Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse, akutero Ambuye; munthu wotsata Ine adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE 12:44-50 Ine ndine kuŵala, ndipo ndidadza pansi pano, kuti munthu aliyense wokhulupirira Ine, asamayende mu mdima. Yesu adanena mokweza mawu kuti: “Munthu wondikhulupirira, sakhulupirira Ine ndekha ayi, koma amakhulupiriranso Iye amene adandituma. Ndipo munthu woona Ine, amaonanso Iye amene adandituma. Ine ndine kuŵala, ndipo ndidadza pansi pano, kuti munthu aliyense wokhulupirira Ine, asamayende mu mdima. Munthu akamva mawu anga koma osaŵagwiritsa ntchito, Ine sindimzenga mlandu ayi. Pakuti sindidadzere kudzazenga anthu mlandu, koma kudzaŵapulumutsa. Munthu amene akana Ine, ndipo salandira mawu anga, alipo amene adzamuweruze. Adzazengedwa mlandu pa tsiku lomaliza chifukwa cha mawu omwe ndakhala ndikulankhulaŵa. Pajatu sindidalankhule zochokera mwa Ine ndekha, koma Atate amene adandituma ndiwo adandilamula zoti ndinene, ndi momwe ndilankhulire. Ndipo ndikudziŵa kuti zimene amandilamula nzolinga ku moyo wosatha. Nchifukwa chake zimene ndimalankhula, ndimalankhula monga momwe Atate amandiuzira.” Mthenga wa Ambuye