LA MULUNGU LACHAKA CHA THUPI NDI MAGAZI A KHRISTU

Watch this Catholic homily in Chichewa by Rev. Deacon Justin Malewezi Jnr for 7 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Rev. Deacon Justin Malewezi Jnr·7 June 2026·15:34·7 views
Ordinary Time
DEUTRONOMO 8:2-3,14b-16a SALIMO 147:12-13,14-15,19-20 KALATA YOYAMBA YA PAULO KWA AKORINTO 10:16-17 YOHANE 6:51-58

Mau a Mulungu a Lero

7 JUNE 2026 LA MULUNGU LACHAKA CHA THUPI NDI MAGAZI A KHRISTU Ine Ndine Chakudya Chopatsa Moyo MAU OYAMBA A MBUKU LA DEUTRONOMO 8:2-3,14b-16a [Mose adauza anthu ake kuti] “Kumbukirani m'mene Chauta, Mulungu wanu, adakutsogolerani m'chipululu, pa ulendo wa pa zaka zonse makumi anai zapitazi. Adakuvutani nakuyesani ndi zoŵaŵa, kuti adziŵe zimene zinali m'mitima mwanu, ndipo kuti aone ngati mudzamvera malamulo ake kapena ai. Adakutsitsani pokukhalitsani ndi njala, komanso adakupatsani mana kuti mudye. Inu ndi makolo anu simudadyepo ndi kale lonse chakudya chimenechi. Adachita zimenezi kuti akuphunzitseni kuti munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha ai, koma ndi mau onse otuluka m'kamwa mwa Mulungu. pamenepo musadzanyade ndi kuiŵala Chauta, Mulungu wanu, amene adakutulutsani ku Ejipito kumene mudaali akapolo. Iye adakutsogolerani, mpaka mudabzola chipululu chachikulu ndi choopsa chija, m'mene munali njoka za ululu woopsa ndi zinkhanira. Adakupatsani madzi otuluka m'thanthwe, m'dziko louma lopanda madzi lija. Adakupatsani mana oti mudye, chakudya chimene makolo anu anali asanadyepo. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 147:12-13,14-15,19-20 Tamanda Chauta iwe Yerusalemu. Tamanda Chauta, iwe Yerusalemu. Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni. Paja amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako. Amadalitsa anthu amene ali mwa iwe. Tamanda Chauta iwe Yerusalemu. Amadzetsa mtendere m'malire a dziko lako, amakudyetsa pokupatsa ufa wa tirigu wosalala. Akapereka lamulo pa dziko lapansi, mau ake amayenda mwaliŵiro. Tamanda Chauta iwe Yerusalemu. Amadziŵitsa Yakobe mau ake, amaphunzitsa Israele malamulo ake ndi malangizo ake. Sadachitepo zimenezi ndi mtundu wina uliwonse wa anthu, iwo sadziŵa malangizo ake. Tamandani Chauta! Tamanda Chauta iwe Yerusalemu. MAU A CHIWIRI A MKALATA YOYAMBA YA PAULO KWA AKORINTO 10:16-17 [Abale] Nanga chikho chimene timachidalitsa mothokoza Mulungu, kodi suja timaphatikizana ndi magazi a Khristu tikamweramo? Nanga mkate umene timaunyema, kodi suja timaphatikizana ndi thupi la Khristu tikaudya? Popeza kuti mkate ndi umodzi wokha, ife tonse, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, chifukwa tonse timagaŵana mkate umodzi womwewo. Mau a Ambuye ALELUYA Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera kumwamba. Munthu Wodya Chakudyachi Adzakhala ndi Moyo Mpaka muyaya ALELUYA MTHENGA WABWINO WA YOHANE 6:51-58 [Yesu adati] Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo chakudyacho chimene Ine ndidzapereka ndi thupi langa, limene ndikulipereka kuti anthu a pa dziko lonse lapansi akhale ndi moyo.” Pamenepo Ayuda aja adayamba kukangana okhaokha, ankatai, “Munthu ameneyu angathe bwanji kutipatsa thupi lake kuti tidye?” Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati simudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu. Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga, ali ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni, ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa iyeyo. Monga Atate amoyo adandituma, ndipo Ine ndili ndi moyo pokhala mwa Iwo, momwemonso aliyense wodya Ine, adzakhala ndi moyo pokhala mwa Ine. Chakudya chimene chidatsika kuchokera Kumwamba nchimenechi. Nchosiyana ndi mana aja amene makolo anu ankadya koma nkufabe. Wodya chakudya chimenechi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya.” Mthenga wa Ambuye