CHAKA CHA MARKO, OFALITSA MTHENGA - 25 APRIL, 2026
Fr. Horrice Mkandawire·25 April 2026
25 APRIL, 2026
CHAKA CHA MARKO, OFALITSA MTHENGA
MAU OYAMBA MAU A M’KALATA YA 1 PETRO 5:5b-14
Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza. Zimenezi zikukondweretseni, ngakhale tsopano mumve zoŵaŵa poyesedwa mosiyanasiyana pa kanthaŵi . Monga golide, ngakhale ndi wotha kuwonongeka, amayesedwa ndi moto, momwemonso chikhulupiriro chanu, chimene nchoposa golide kutali, chimayesedwa, kuti chitsimikizike kuti nchenicheni. Apo ndiye mudzalandire chiyamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka. Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu.
Aneneri amene adaneneratu za mphotho yaulere imene mudzalandireyo, ankafunafuna mofufuzafufuza za chipulumutsochi. Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo ankaneneratu za zoŵaŵa zimene Khristu adzamve, ndiponso za ulemerero umene adzakhale nawo pambuyo pake. Aneneriwo ankafunafuna kudziŵa kuti kodi zimenezi zidzachitika liti, ndiponso mwa njira yanji. Mulungu adaŵaululira kuti ntchito yaoyi sankaigwira chifukwa cha eniakewo, koma chifukwa cha inu, pamene iwo ankanena zoonazi zimene mwamva tsopano. Olalika Uthenga Wabwino adakuuzani zoonazi mwa mphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera Kumwamba. Angelo omwe amalakalaka kuwona nao zinthuzo. Nchifukwa chake mtima wanu ukhale wokonzeka. Khalani tchelu. Khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa kukoma mtima kwa Mulungu pamene Yesu Khristu adzaoneke. Muzikhala ngati ana omvera, osatsatanso zimene munkalakalaka pamene munali osadziŵa.
Mau a Ambuye
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 89: 2-3, 6-7, 16-17
Ndidzaimba za ubwino wa Chauta moyo wanga onse
Inu Chauta, ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda
chikondi chanu chosasinthika.
Ndidzalalika ndi pakamwa panga
za kukhulupirika kwanu ku mibadwo yonse.
Zakumwamba zimatamanda zodabwitsa zanu,
Inu Chauta, zimatamanda kukhulupirika kwanu mu msonkhano wa oyera mtima.
Ndidzaimba za ubwino wa Chauta moyo wanga onse
Kodi ndani mu mlengalenga angathe kulingana ndi Chauta?
Ndani pakati pa akumwamba amafanafana naye?
Mulungu ndiye amene amamuwopa mu msonkhano wa anthu oyera mtima,
wamkulu ndi wolemekezeka pakati pa onse omzungulira.
Ndidzaimba za ubwino wa Chauta moyo wanga onse
Ngodala anthu amene mumaŵaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero,
amene amayenda m'chikondi chanu, Inu Chauta.
Iwowo amakondwa masiku onse chifukwa cha Inu,
ndipo amatamanda kulungama kwanu.
Ndidzaimba za ubwino wa Chauta moyo wanga onse
Aleluya: Pitani Maiko onse kalarikeni, Ine ndili nanu nthawi zonse* Aleluya*.
MTHENGA WABWINO WA MARKO 16:15-20
Tsono adaŵauza kuti, “Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni anthu onse Uthenga Wabwino. Amene akakhulupirire ndi kubatizidwa, adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira, adzaweruzidwa kuti ngwolakwa. Okhulupirira azidzachita zozizwitsa izi: azidzatulutsa mizimu yoipa potchula dzina langa, azidzalankhula zilankhulo zachilendo, ndipo akagwira njoka kapena kumwa chakumwa chotha kuŵapha, sadzapwetekedwa. Akasanjika manja pa anthu odwala, anthuwo azidzachira.” Ambuye Yesu atalankhula nawo, adatengedwa kupita Kumwamba, nakakhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Tsono ophunzira aja adanka nalalika ponseponse. Ambuye ankagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo ankatsimikiza mau ao ndi zozizwitsa zimene ankachita.
Mthenga wa Ambuye