KULEMEKEZA BARNABAS, MPOSTOLI WOYERA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Gift Phiri, OFM for 11 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Gift Phiri, OFM·11 June 2026·16:22·3 views
Ordinary Time
NTCHITO ZA ATUMWI 11:21B-26,13:1-3 SALIMO 98: 1,2-3AB,3CD-4, 5-6, MATEYU WOYERA 10:7-13

Mau a Mulungu a Lero

11 JUNE, 2026 KULEMEKEZA BARNABAS, MPOSTOLI WOYERA MAU WOYAMBA A MBUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI 11:21B-26,13:1-3 ‭ Barnabasiyo anali munthu wolungama, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro. Ambuye ankaŵalimbikitsa, mwakuti anthu ambiri adakhulupirira natembenukira kwa Ambuye. Mpingo wa ku Yerusalemu utamva zimene zidachitikazo, udatuma Barnabasi ku Antiokeyako. Pamene iye adafika kumeneko nkuwona m'mene Mulungu adaŵadalitsira, adakondwa, nalimbikitsa onsewo kuti atsimikize mtima kukhala okhulupirika kwa Ambuye. Barnabasiyo anali munthu wolungama, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro. Choncho anthu ambirimbiri adakopeka nadzipereka kwa Ambuye. Pamenepo Barnabasi adapita ku Tariso kukafuna Saulo. Atampeza, adabwera naye ku Antiokeya. Iwo adakhala pamodzi mu mpingo umenewo chaka chathunthu, naphunzitsa anthu ambirimbiri. Ndi ku Antiokeya kumene ophunzira adayamba kutchedwa Akhristu. Mu mpingo wa ku Antiokeya munali alaliki ndi aphunzitsi aŵa: Barnabasi, Simeoni (wotchedwa Wakuda), Lusio wa ku Kirene, Manaene (amene adaaleredwa pamodzi ndi bwanamkubwa Herode), ndiponso Saulo. Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.” Tsono atasala zakudya ndi kupemphera adaŵasanjika manja naŵatuma. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 98: 1,2-3AB,3CD-4, 5-6, Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, popeza kuti wachita zodabwitsa. Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa. Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse kuti Iye ndi wolungama. Wakumbukira chikondi chake chosasinthika ndi kukhulupirika kwake pa fuko la Israele. Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu. Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi. Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda. Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe, lizani pangwe ndi nyimbo zokoma. Imbirani Chauta Mfumu, imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete. Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo Aleluya: (Mateyo 28: 19a,20b) Pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi. Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU WOYERA 10:7-13 Mwalandira mwaulere, kaperekeni mwaulere ‭Pitani, muzikalalika kuti, ‘Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake tsopano.’ Muzikachiritsa odwala, muzikaukitsa akufa, muzikachotsa khate, muzikatulutsa mizimu yoipa. Mwalandira mwaulere, kaperekeni mwaulere. Musatenge ndalama m'zikwama, kaya nzagolide, kaya nzasiliva, kaya nzakopala. Musatenge thumba lapaulendo, kapena mikanjo iŵiri, kapena nsapato, kapena ndodo. Paja wantchito ngwoyenera kulandira zosoŵa zake. “Pamene mwaloŵa mu mzinda kapena m'mudzi uliwonse, mufunsitse za munthu wofunadi kukulandirani. Mukakhale kunyumba kwake mpaka nthaŵi yochoka. Poloŵa m'nyumba, muzikanena kuti, ‘Mtendere ukhale ndi inu’. Tsono ngati anthu am'nyumbamo akulandiranidi, mtendere wanuwo ukhale nawo ndithu. Koma ngati anthu am'nyumbamo akana kukulandirani, mtendere wanuwo ubwerere kwa inu. Mthenga wa Ambuye