LACHINAI LA MULUNGU WA 11 PACHAKA
Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Charles Duncan for 18 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
18 JUNE, 2026 LACHINAI LA MULUNGU WA 11 PACHAKA MAU WOYAMBA A MBUKU LA MPHUNZITSI 48:1-14 Padabwera Eliya Mneneri wonga moto. Mawu ake ankawala ngati nsakali. Adadzetsa njala pa anthu, motero anthu ambiri adafa chifukwa cha changu chake. Potsata mawu a Ambuye, adatseka thambo la Kumwamba ndipo adatsitsa moto katatu. Iwe Eliya, ntchito zako zidali zozizwitsa kwabasi. Ndani angathe kunyadira ntchito zotere? Udaukitsa munthu wakufa m’manda ndi mawu a Mulungu wopambana zonse. Udagwetsa mafumu m’chionongeko, ndipo anthu otchuka udawagwetsa pansi kuchokera pa bedi pawo. Udamva mawu odzudzula ku Phiri la Sinai, mawu otsimikiza za chilango ku phiri la Horebu. Tsono udadzodza mafumu kuti azilipsira, ndi aneneri kuti alowe m’malo mwako. Udatengedwa kupita Kumwamba ndi kamvulumvulu wa moto wa galeta lokokedwa ndi akavalo a moto. Zidalembedwa kuti udzabwerera pa nthawi yake, kudzaziziritsa mkwiyo wa Mulungu, ukali wake usadabuke, kudzayanjanitsa bambo ndi mwana, ndi kudzakhazikitsanso mafuko a Yakobe. Ngodala amene adzakuona ndiponso amene adafa ali ndi chikondi. Ndithudi ifenso tidzakhala ndi moyo. Pamene paja Eliya adatengedwa ndi kamvulumvulu, Elisa adadzazidwa ndi nzeru zake. Pa moyo wake wonse sadachite mantha ndi mfumu ina ili yonse, ndiponso padalibe munthu wotha kumugonjetsa. Padalibe ntchito yomukanika. Ngakhale atafa, thupi lake lidatchula mawu olosa. Ali moyo adachita zinthu zozizwitsa ndipo atafa, ntchito zakenso zidakhala zodabwitsa. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 97: 1-2, 3-4, 5-6, 7 Inu anthu ake a Chauta, kondwerani mwa Iye (12a). Chauta ndiye Mfumu, Anthu apa dziko lapansi akondwere, Anthu onse a m’mbali mwa nyanja asangalale. Mitambo ndi mdima waukulu zamzinga Chauta. Amalamulira molungama; mu ufumu wake mulibe tsankho. Inu anthu ake a Chauta, kondwerani mwa Iye. Moto umapita patsogolo pake, Umapsereza adani ake omzinga kuli konse. Zing’aning’ani zake zimaŵalitsa dziko lonse lapansi, Dziko lonse limapenya nkugwedezeka. Inu anthu ake a Chauta, kondwerani mwa Iye. Mapiri amasungunuka ngati sera pamaso pa Chauta, Ndiye wolamulira dziko lonse lapansi. Za Kumwamba zimalalika za kulungama kwake, Ndipo anthu a mitundu yonse amaona ulemerero wake. Inu anthu ake a Chauta, kondwerani mwa Iye. Onse opembedza milungu yonama, Amene amanyadira mafano achabechabe, Amachititsidwa manyazi, Pakuti milungu ina yonse imagonjera Chauta. Inu anthu ake a Chauta, kondwerani mwa Iye. Aleluya: (Aroma 8: 15bc) Mzimu amene mudalandira, samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso a mantha ayi. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu, timati: “Abba! Atate!” Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU WOYERA 6:7-15 Yesu adati kwa ophunzira ake: “Pamene mukupemphera, musamangobwereza-bwereza mawu monga amachitira anthu akunja. Iwowo amayesa kuti akachulukitsa mawu choncho, ndiye pamene Mulungu aŵamvere. Inu musamatero ayi, pakuti Atate anu amadziŵa zimene mukusoŵa, inu musadapemphe. Nchifukwa chake popemphera muziti: ‘Atate athu a Kumwamba, dzina lanu lilemekezedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chonchonso pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu cha masiku onse. Mutikhululukire ife machimo athu, monga ifenso tiwakhululukira otilakwira. Ndipo musalole kuti tiyesedwe koma mutipulumutse kwa Woipa uja. Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu pa nthawi zonse. Amen.’ Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo awo, Atate anu a Kumwamba adzakukhululukirani inunso. Koma ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.” Mthenga wa Ambuye