LACHINAI LA MULUNGU WA 12 PACHAKA
Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Steven Limbani Kassim for 25 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
25 JUNE, 2026 LACHINAI LA MULUNGU WA 12 PACHAKA MAU WOYAMBA A MBUKU LACHIWIRI LA MAFUMU 24:8-17 Yehoyakini adali wa zaka 18 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira miyezi itatu ku Yerusalemu. Mayi wake adali Nehusita, mwana wa Elinati, wa ku Yerusalemu. Yehoyakini adachita zoipa pamaso pa Chauta potsata zonse zimene ankachita bambo wake. Nthaŵi imeneyo ankhondo a Nebukadineza, mfumu ya ku Babiloni, adadza ku Yerusalemu, nazinga mzindawo ndi zithando zankhondo. Ndipo Nebukadineza, mfumu ya ku Babiloni, adafika ku mzindawo pa nthaŵi imene ankhondo ake ankauzinga. Tsono Yehoyakini, mfumu ya ku Yuda, adadzipereka kwa mfumu ya ku Babiloni, pamodzi ndi mayi wake, alangizi ake, nduna zake, ndiponso akuluakulu aku nyumba kwake.Mfumu ya ku Babiloni idamugwira Yehoyakini ukapolo, pa chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake. Adatenga chuma chonse cha ku Nyumba ya Chauta, pamodzi ndi chuma chonse cha ku nyumba ya mfumu. Adaononga ziŵiya zonse zagolide za ku Nyumba ya Chauta, zimene Solomoni, mfumu ya ku Israele, adapanga. Adatenga anthu onse aku Yerusalemu, ndiye kuti nduna zonse ndi anthu onse amphamvu. Onsewo pamodzi adalipo 10,000. Adatenganso anthu onse aluso ndi amisiri osula. Sadatsalepo ndi mmodzi yemwe, kupatula anthu osauka okha a m’dzikomo. Nayenso Yehoyakini adamutenga kupita naye ku Babiloni. Adatenganso mayi wake wa mfumuyo, akazi ake, nduna zake ndiponso anthu omveka a m’dzikomo. Onsewo adaŵagwira ukapolo ku Yerusalemu kunka nawo ku Babiloni. Tsono mfumu ya ku Babiloni idagwira ukapolo anthu otchuka onse okwanira 7,000, ndiponso anthu aluso pamodzi ndi amisiri osula 1,000. Onsewo adali amphamvu odziŵa kumenya nkhondo. Kenaka mfumu ya ku Babiloni idalonga ufumu Mataniya, malume wa Yehoyakini, m’malo mwake, ndipo adasintha dzina lake kuti akhale Zedekiya. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 79: 1B-2, 3-5, 8, 9 Inu Chauta, dzina lanu likhale ndi ulemerero mpaka muyaya (9). Inu Mulungu, anthu akunja aloŵerera, m’dziko la anthu anu, Ayipitsa Nyumba yanu yoyera, asandutsa Yerusalemu bwinja. Ataya mitembo ya atumiki anu Kwa mbalame za mlengalenga, kuti ikhale chakudya chake, Ataya matupi a anthu anu oyera mtima kwa zirombo za ku thengo. Inu Chauta, dzina lanu likhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Akhetsa magazi awo ngati madzi, ponse pozungulira Yerusalemu, Ndipo palibe woti nkuika maliro awo. Ife tasanduka chinthu chonyozeka kwa anzathu, Anthu a mitundu ina amatinyodola ndi kutiseka. Mpaka liti, Inu Chauta? Kodi mudzakhalabe wokwiya mpaka muyaya? Kodi nsanje yanu idzayakabe ngati moto? Inu Chauta, dzina lanu likhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Musatilange ife chifukwa cha machimo a makolo athu. Mutichitire chifundo msanga, Chifukwa tatsitsidwa kwambiri. Inu Chauta, dzina lanu likhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Tithandizeni, Inu Mulungu, Mpulumutsi wathu, Kuti dzina lanu likhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Tipulumutseni, ndipo mutikhululukire zochimwa zathu, Kuti dzina lanu lilemekezeke. Inu Chauta, dzina lanu likhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Aleluya: (Yohane 14: 23) Ngati munthu andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate anga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye, Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU WOYERA 7:21-29 Yesu adati kwa ophunzira ake: “Si munthu aliyense wonditchula Ine kuti: ‘Ambuye! Ambuye!’ Amene adzaloŵe mu Ufumu wa Kumwamba ayi. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga a Kumwamba afuna. Pa tsiku la chiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti: ‘Ambuye! Ambuye! Kodi suja ife tinkalalika mawu a Mulungu m’dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m’dzina lanu?’ Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti: ‘Sindikudziŵani konse ayi. Chokani apa, anthu ochita zoipa!’ Munthu aliyense womva mawu angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adamanga nyumba yake pa thanthwe. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaimanga polimba.Koma aliyense wongomva mawu angaŵa, osaŵagwiritsa ntchito, ali ngati munthu wopusa amene adamanga nyumba yake pa mchenga. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo, ndipo idagwa. Kugwa kwake kudali koopsa.” Yesu atatsiriza kunena zimenezi, anthu onse aja adadabwa ndi kaphunzitsidwe kake, chifukwa ankaŵaphunzitsa monga munthu wa ulamuliro osati monga m’mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo. Mthenga wa Ambuye