LACHINAI LA MULUNGU WA 16 PACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Elizeo Nthalika, DP for 23 July 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Elizeo Nthalika, DP·23 July 2026·18:16·2 views
Ordinary Time
YEREMIYA 2:1-3.7-8.12-13 SALIMO 36:5-10 MATEYU 13:10-17

Mau a Mulungu a Lero

23 JULY, 2026 LACHINAI LA MULUNGU WA 16 PACHAKA MAU WOYAMBA A MBUKU LA MNENERI YEREMIYA 2:1-3.7-8.12-13 Chauta adandiuza kuti ndikalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu mau akuti, "Ndikukumbukira m'mene munkakhulupirikira pa unyamata wanu, m'mene poyamba paja munkandikondera monga amachitira mkwati wamkazi. Mudanditsata m'chipululu, m'dziko losabzalamo kanthu. Iwe Israele udaali wopatulika wa Chauta. Udaali ngati chipatso chake choundukula. Ndidaika zoŵaŵa ndi mavuto aakulu, pa onse amene adakuzunza, ndipo tsoka linkawagwera," akutero Chauta. "Ndidakufikitsani ku dziko lachonde kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina. Koma mutangolowa m'dzikolo, mudaliipitsa, dziko limene ndidakupatsani mudalisandutsa lonyansa. Nawonso ansembe sadafunse kuti, 'Chauta ali kuti?' Akatswiri a malamulo sadandidziwe. Olamulira adandipandukira. Aneneri ankalosa m'dzina la Baala, ndipo ankatsata milungu yachabechabe. Inu maiko akumwamba, dabwa nazoni zimenezi, njenjemerani ndi mantha, akuterotu Chauta. Anthu anga achita machimo aŵiri: andisiya lne kasupe wa madzi opatsa moyo, adzikumbira okha zitsime, zitsime zake zong'aluka, zosatha kusunga madzi. " Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 36:5-10 Kwa Inu, Chauta, kuli kasupe wamoyo. Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chimafika mpaka kumwamba, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo. Kulungama kwanu kumaonekera ngati mapiri aatali, kuweruza kwanu nkozama ngati Nyanja yakuya. Kwa Inu, Chauta, kuli kasupe wamoyo. Chikondi chanu chosasinthika ndi cha mtengo wapatali. Nchifukwa chake anthu anu amathawira m'munsi mwa mapiko anu. Mumawadyetsa zonona m'nyumba mwanu, ndipo mumawamwetsa madzi a mtsinje wa madalitso ani. Kwa lnu, Chauta, kuli kasupe wamoyo. Kwa Inu kuli kasupe wa moyodi, m'kuwala kwanu ifenso timaona kuwala. Musaleke kuwakonda ndi chikondi chanu chosasinthika anthu okudziwani, pitirizani kuwachitira zokoma anthu olungama mtima Aleluya: Tamandani Chauta, iwe Yerusalemu. Akapereka lamulo pa dziko lapansi Aleluya MTHENGA WABWINO WA MATEYU 13:10-17 Ophunzira a Yesu adadzamufunsa kuti: “Kodi bwanji anthuŵa mumalankhula nawo m’mafanizo?” Iye adati: “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wa Kumwamba. Koma enaŵa sadaŵaululire ayi. Pajatu amene ali kale ndi kanthu, adzampatsanso zina, nadzakhala ndi zochuluka. Koma amene alibe kanthu, adzamlanda ngakhale kakang’onong’ono kamene ali nako. Tsono anthuŵa ndimalankhula nawo m’mafanizo, chifukwa ngakhale amapenya, komabe saona, ndipo ngakhale amamva, komabe samva kwenikweni kapena kumvetsa. Ndi iwoŵa zikuchitikadi zimene Mneneri Yesaya adanena kuti: ‘Kumva mudzamva ndithu, koma osamvetsa, kuyang’ana mudzayang’ana ndithu, koma osapenya. Ndithu anthu ameneŵa nzeru zawo nzobuntha, adagonthetsa makutu awo, ndipo adapsinya maso awo, kuopa kuti angamapenye ndi maso awowo, angamamve ndi makutu awowo, angamamvetse ndi nzeru zawozo, ndi kutembenuka mtima, Ineyo nkuŵachiritsa.’ Koma inu ndinu odala, popeza kuti maso anu akupenya, ndipo makutu anu akumva. Kunena zoona, aneneri ambiri ndi anthu ambiri olungama, adafunitsitsa kuona zimene inu mukupenyazi, koma sadaziwone. Adafunitsitsa kumva zimene inu mukumvazi, koma sadazimve.” Mthenga wa Ambuye