LACHINAI LA MULUNGU WA 8 PACHAKA
Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Maxwell Kubalasa for 28 May 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
28 MAY, 2026 LACHINAI LA MULUNGU WA 8 PACHAKA MAU OYAMBA; MAU A MKALATA YOYAMBA YA PETRO 2:2-5,9-12 Monga makanda, obadwa chatsopano, amalirira mkaka, inunso mudzilakalaka mkaka weniweni wodyetsa mtima wanu, kuti mukule nawo ndi kupulumuka, ngati mwalawadi ndi kudzindikira kuti Ambuye ali wokoma mtima. Bwerani kwa Iye, amene ali mwala wa moyo womwe anthu adaukana, koma Mulungu adausankha ndi kuulemekeza. Inunso mukhale ngati miyala ya moyo yoti Mulungu amange nawo nyumba yake. Mmenemo mutumikire ngati ansembe opatulika, pakupereka nsembe zochokera ku mtima, zokomera Mulungu chifukwa cha Yesu Khristu. Koma inu ndinu mtundu wosankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu ake enieni. Adakusankhani kuti mukalalike zokoma za Iye, amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mu kuwala kwake kodabwitsa. Kale simudali anthu a Mulungu, koma tsopano muli anthu ake. Kale simudalandire chifundo koma tsopano mwachilandira. Ndikukupemphani, okondedwa anga, popeza ndinu alendo pansi pano, musagonjere zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo ndi moyo wanu. Samalani mayendedwe anu, pokhala pakati pa akunja, kuti ngakhale akusinjirireni kuti zochita zanu nzoipa komabe aone kuti nzabwino. Apo adzalemekeza Mulungu pa tsiku limene adzawayendere. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 100: 2, 3, 4, 5 Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa (2c). Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse. Tumikirani Chauta mosangalala. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa. Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake. Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, Pitani m’mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake! Paja Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya, Kukhulupirika kwake nkosatha. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa. Aleluya: (Yohane 8: 12) Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala nako kuŵala kotsogolera anthu ku moyo, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MARKO 10:46-52 Pamene Yesu ndi ophunzira ake, pamodzi ndi chikhamu chachikulu cha anthu, adali kutulukira mu Yeriko, padali munthu wina wa khungu, dzina lake Baratimeyo, mwana wa Timeyo. Iyeyu adali atakhala pansi pa mphepete pa msewu, namapempha kwa anthu. Pamene adamva kuti ndi Yesu wa ku Nazareti, adayamba kufuula kuti: “Inu Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.” Yesu adaima nawauza anthu kuti: “Tamuitanani.” Anthu aja adamuitana wakhunguyo, namuuza kuti: “Limba mtima, nyamuka, alikukuitana.” Iye uja adaponya pansi chofunda chake, nanyamuka mofulumira, nakafika kwa Yesu. Yesu adamufunsa kuti: “Ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Wakhunguyo adayankha kuti: “Ambuyanga, ndifuna kuti ndipenye.” Yesu adamuuza kuti: “Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Nthawi yomweyo adayamba kupenya namtsatira Yesu pa ulendowo. Mthenga wa Ambuye