LACHINAI LA MULUNGU WA 9 PACHAKA LACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Rev. Deacon Justin Malewezi Jnr for 4 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Rev. Deacon Justin Malewezi Jnr·4 June 2026·14:28·4 views
Ordinary Time
KALATA YACHIWIRI YA PAULO KWA TIMOTEO 2:8-15 SALIMO 25: 4-5AB, 8-9, 10 NDI 14 MARKO 12:28-34

Mau a Mulungu a Lero

4 JUNE, 2026 LACHINAI LA MULUNGU WA 9 PACHAKA LACHAKA MAU OYAMBA; MAU A MKALATA YACHIWIRI YA PAULO KWA TIMOTEO 2:8-15 Wokondedwa, kumbukira Yesu Khristu, amene adauka kwa akufa, ndiponso adali mmodzi mwa zidzukulu za Davide, monga umaphunzitsira Uthenga Wabwino, umene ine ndimalalika. Chifukwa cha Uthenga Wabwinowu, ndimamva zoŵaŵa, mpakanso kumangidwa m’ndende, ngati chigaŵenga. Koma mawu a Mulungu sangathe kumangidwa. Motero tsono ndimapirira zonsezi chifukwa cha anthu amene Mulungu adaŵasankha, kuti iwonso apulumutsidwe ndi Khristu Yesu, ndi kulandira ulemerero wamuyaya. Aŵa ndi mawu otsimikizika ndithu: “Ngati tidafa pamodzi naye, tidzakhala moyonso pamodzi naye. Ngati tilimbika, tidzakhala mafumu pamodzi naye. Ngati ife timkana, Iyenso adzatikana. Ngati ndife osakhulupirika, Iye amakhalabe wokhulupirika, pakuti sangathe kudzitsutsa.” Uziŵakumbutsa zimenezi anthu, ndipo uŵachenjeze kolimba pamaso pa Mulungu kuti asamakangana pa za mawu. Kutero kulibe phindu, koma kumangotayikitsa anthu amene akumva kukanganako. Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mawu a choona mwachilungamo. ‭‭Mau a Ambuye‬‬‬‬ NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 25: 4-5AB, 8-9, 10 NDI 14 Mundiphunzitse njira zanu, Inu Chauta (4). Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, Mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu. Munditsogolere m’choona chanu ndi kundilangiza, Pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga. Mundiphunzitse njira zanu, Inu Chauta. Chauta ndi wabwino ndi wolungama. Nchifukwa chake amaphunzitsa ochimwa njira zake. Amatsogolera anthu odzichepetsa kuti achite zolungama, Amaŵaphunzitsa njira zake. Mundiphunzitse njira zanu, Inu Chauta. Njira zonse za Chauta ndi za chikondi chosasinthika, Nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chake Ndi malamulo ake. Chauta amapalana ubwenzi ndi anthu omvera Iye, Ndipo amaŵadziŵitsa chipangano chake. Mundiphunzitse njira zanu, Inu Chauta. Aleluya: (2 Timoteyo 1: 10) Yesu Khristu adathetsa mphamvu za imfa, ndipo mwa Uthenga Wabwino, adaonetsera poyera moyo umene sungafe konse, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MARKO 12:28-34 Mphunzitsi wina wa Malamulo adadza pafupi, namufunsa Yesu kuti: “Kodi mwa malamulo onse, lalikulu ndi liti?” Yesu adamuyankha kuti: “Lamulo lalikulu ndi ili: ‘Tamverani, inu Aisraele, Chauta, Mulungu wathu, Iye yekha ndiye Mulungu. Motero, uzikonda Chauta, Mulungu wakoyo, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse.’ Lamulo lachiŵiri lake ndi ili: ‘Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe mwini.’ Palibe lamulo lina loposa malamulo ameneŵa.” Mphunzitsi wa Malamulo uja adati: “Ayi, mwayankha bwino, Aphunzitsi. Monga mwaneneramo, nzoonadi kuti Mulungu ndi mmodzi yekhayo, ndipo palibe winanso koma Iye yekha. Mwalondolanso ponena kuti chinthu chopambana ndicho kukonda Mulungu ndi mtima wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zonse, ndiponso kukonda mnzako monga umadzikondera iwe mwini. Kuteroko nkoposa kupereka nsembe zopsereza, ndiponso nsembe zina zonse.” Yesu adaona kuti munthuyo wayankha mwanzeru. Tsono adamuuza kuti: “Iwe suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira apo, padalibenso wina woti ayesere kumufunsa kanthu. Mthenga wa Ambuye