LACHINAYI LAMULUNGU WA 29 PACHAKA (II) - KULEMEKEZA PAPA YOHANE PAULO WACHIWIRI WOYERA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Medrick Mlava, DP for 22 October 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Medrick Mlava, DP·22 October 2026·14:08
Ordinary Time
MAU OYAMBA : AEFESO 3:14-21 SALIMO 33: 1-2, 4-5, 11-12, 18-19 MTHENGA WABWINO : LUKA 12:49-53

Mau a Mulungu a Lero

22 OCTOBER, 2026 LACHINAYI LAMULUNGU WA 29 PACHAKA (II) KULEMEKEZA PAPA YOHANE PAULO WACHIWIRI WOYERA MAU OYAMBA; MAU A MKALATA YA PAULO KWA KWA AEFESO 3:14-21 Okondedwa, nchifukwa chake tsono ndikugwadira Atate, amene banja liri lonse, Kumwamba ndi pansi pano, limatchulidwa ndi dzina lawo. Ndikupempha Mulungu kuti, kuchokera m’chuma cha ulemerero wake, akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu. Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m’mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m’chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi. Ndikupempha Mulungu kuti, pamodzi ndi anthu ake onse, muthe kuzindikira kupingasa kwake ndi kutalika kwake, kukwera kwake ndi kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. Ndithu ndikupemphera kuti mudziŵe chikondi chija cha Khristu, chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kotheratu ndi moyo wa Mulungu Mwini. Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza. Mulungu alandire ulemuwo mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibadwo yonse mpaka muyaya. Amen. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 33: 1-2, 4-5, 11-12, 18-19 Dziko lapansi ladzaza ndi ubwino wa Ambuye (5b). Kondwerani mwa Chauta, inu anthu ake. Zoonadi ochita zolungama azitamanda. Tamandani Chauta ndi pangwe. Muimbireni nyimbo ndi zeze wa nsambo khumi. Dziko lapansi ladzaza ndi ubwino wa Ambuye. Mawu a Chauta ndi olungama, Zochita zake zonse amazichita mokhulupirika. Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera. Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi. Dziko lapansi ladzaza ndi ubwino wa Ambuye. Zolinga za Chauta zimachitika nthaŵi zonse, Maganizo amu mtima mwake amakhazikika mpaka muyaya. Ngodala mtundu wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta, Anthu amene Chauta waŵasankha kuti akhale akeake. Dziko lapansi ladzaza ndi ubwino wa Ambuye. Chauta amayang’ana anthu omumvera, Ndi odalira chikondi chake chosasinthika. Iye amachita izi kuti aŵapulumutse ku imfa Ndi kuŵasungira moyo anthuwo pa nthaŵi ya njala. Dziko lapansi ladzaza ndi ubwino wa Ambuye. Aleluya: (Afilipi 3: 8-9) Zonse ndikuziona kuti nzosapindulitsa, poziyerekeza ndi phindu lopambana la kudziŵa Khristu Yesu, amene ndi Ambuye anga,Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA 12:49-53 Yesu adati kwa ophunzira ake: ”Ndidabwera kudzaponya moto pa dziko lapansi, ndipo ndikadakonda utayaka kale. Koma ndiyenera kuyamba ndaloŵa m’masautso akulu, ndipo mtima wanga sukhazikika mpaka zitachitika. Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Iyayi, kunena zoona, osati mtendere koma kugaŵikana. Kuyambira tsopano m’banja limodzi mudzakhala anthu asanu ogaŵikana, atatu adzakangana ndi aŵiri, ndipo aŵiri adzakangana ndi atatu. Bambo adzakangana ndi mwana wake wamwamuna, mwana wamwamuna adzakangana ndi bambo wake. Mayi adzakangana ndi mwana wake wamkazi, mwana wamkazi adzakangana ndi mayi wake. Apongozi adzakangana ndi mkazi wa mwana wawo, ndipo mkaziyo adzakangana ndi apongozi akewo.” Mthenga wa Ambuye