Lachisanu La Mulungu wa 10 pachaka - MTIMA WOYERA WA YESU KHRISTU

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Gift Phiri, OFM for 12 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Gift Phiri, OFM·12 June 2026·19:24·3 views
Ordinary Time
DEUTRONOMO 7:6-11 SALIMO 103: 1-2,3-4,6-7,8 ndi 10 KALATA YA YOYAMBA YA YOHANE 4:7-16 MATEYU 11:25-30

Mau a Mulungu a Lero

12 JUNE 2026 MTIMA WOYERA WA YESU KHRISTU MAU OYAMBA A MBUKU LA DEUTRONOMO 7:6-11 Inu ndinu mtundu wopatulika wa Chauta, Mulungu wanu. Mulungu adasankha inu kuti mukhale anthu ake pakati pa anthu onse a pa dziko lapansi. Mulungu pokukondani ndi kukusankhani inu, sadachitire kuti munkaposa anthu ena onse pakuchuluka. Paja mudaali ochepa ndinuyo pakati pa mitundu yonse. Koma Chauta adakukondani, ndipo adafunadi kusunga malumbiro amene adaachita ndi makolo anu. Nchifukwa chake adakupulumutsani ndi mphamvu zake, nakusandutsani mfulu, kukuchotsani m'dziko laukapolo kwa mfumu ya ku Ejipito ija. Nchifukwa chake mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye yekha Mulungu, ndipo ndi Mulungu wokhulupirika. Iye adzasungadi chipangano chake ndipo adzaonetsa chifundo chake chosasinthika kwa anthu a mibadwo zikwi zambirimbiri amene amakonda Iye namamvera malamulo ake. Koma onse amene amadana ndi Mulungu, adzaŵabwezera pakuŵaononga. Sadzamlekerera munthu wodana naye, koma adzamubwezera pakumlanga ndithu. Motero, muzimvera mosamala malangizo ndi malamulo amene ndikukulamulani leroŵa. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 103: 1-2,3-4,6-7,8 ndi 10 Chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omuopa Tamanda Chauta, iwe mzimu wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera. Tamanda Chauta, iwe Mzimu wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse. Chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omuopa Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse, ndi kuchiritsa matenda ako onse. Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda. Amakuveka chikondi chake chosasinthika ndiponso chifundo chake ngati chisoti chaufumu. Chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omuopa Chauta amaweruza mwachilungamo onse opsinjidwa amaŵachitira zolungama. Adadziŵitsa Mose njira zake, adaonetsa Aisraele ntchito zake. Chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omuopa Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga, ndipo chikondi chake chosasinthika nchachikulu. Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu. Chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omuopa Aleluya: (Yohane 13: 34) Ndakukupatsani lamulo latsopano lakuti: muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana, Aleluya. MAU A MKALATA YA YOYAMBA YA YOHANE 4:7-16 Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu. Koma munthu wopanda chikondi sadziŵa Mulungu, pakuti Mulungu ndiye chikondi chimene. Mulungu adaonetsa chikondi chake kwa ife motere: Iye nkukhala ndi Mwana mmodzi yekha, koma adamtuma pansi pano, kuti mwa Iye tikhale ndi moyo. Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu. Inu okondedwa, ngati Mulungu adatikonda kwambiri chotere, ifenso tiyenera kumakondana. Palibe munthu amene adaona Mulungu. Koma tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife. Tikudziŵa kuti timakhala mwa Mulungu, ndipo Iyenso amakhala mwa ife, chifukwa adatipatsa Mzimu wake Woyera. Ife taona, ndipo tikuchita umboni, kuti Atate adatuma Mwana wake kuti adzakhale Mpulumutsi wa anthu a pa dziko lonse lapansi. Aliyense wovomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye, ndipo iye amakhala mwa Mulungu. Motero ife timadziŵa ndipo timakhulupirira ndithu kuti Mulungu amatikonda. Mau a Ambuye ALELUYA Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wamtima wodzichepetsa ALELUYA MTHENGA WABWINO WA MATEYU 11:25-30 Pa nthaŵi imeneyo Yesu adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira, nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira. Chabwino Atate, pakuti mudafuna kutero mwa kukoma mtima kwanu. ”Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira. ”Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.” Mthenga wa Ambuye