LACHISANU LA MULUNGU WA 11 PACHAKA
Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Charles Duncan for 19 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
19 JUNE, 2026 LACHISANU LA MULUNGU WA 11 PACHAKA MAU WOYAMBA A MBUKU LACHIWIRI LA MAFUMU 11:1-4,9-18,20 Ataliya, mayi wake wa Ahaziya, ataona kuti mwana wake wafa, adanyamuka nakaononga onse a m’banja lachifumu. Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, adatenga Yowasi, mwana wa Ahaziya. Adachita momuba, kumuchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene ankati aŵaphewo. Adamuika m’chipinda china chogona cha m’Nyumba ya Chauta pamodzi ndi mlezi wake. Motero adamubisa mwanayo, kubisira Ataliya, kotero kuti sadaphedwe. Mwanayo adakhala ndi mlezi wake zaka zisanu ndi chimodzi akubisala m’Nyumba ya Chauta, pamene Ataliya ankalamulira dzikolo. Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri, wansembe Yehoyada adatumiza mawu kukaitana atsogoleri a asirikali olonda mfumu, ndipo a alonda a nyumba chifumu. Adabwera nawo kwa Yehoyada ku Nyumba ya Chauta. Tsono adapangana nawo chipangano, ndipo adaŵalumbiritsa m’Nyumba ya Chauta. Kenaka adaŵaonetsa mwana wamwamuna wa mfumu uja. Atsogoleriwo adachitadi zonse monga m’mene Wansembe Yehoyada adaŵalamulira. Aliyense adabwera ndi anthu ake amene ankadzayamba ntchito yawo pa Sabata, pamodzinso ndi anthu amene ankasiya ntchito yawo kulonda pa Sabata. Onsewo adafika kwa Yehoyada, wansembe uja. Wansembeyo adapatsa atsogoleri aja mikondo ndi zishango, zimene zidali za Mfumu Davide. Zimenezi zinkasungidwa m’Nyumba ya Chauta. Tsono adandanditsa asirikaliwo kuti aziteteza mfumu, aliyense ali ndi zida m’manja mwake, kuzungulira guwalo, ndiponso Nyumbayo. Kenaka adaŵatulutsira mwana wa mfumu, namuveka chisoti chaufumu, nkumupatsa bukhu la malamulo, ndipo adamudzoza namulonga ufumu. Anthu adamuwombera m’manja nkunena mofuula kuti: “Amfumu akhale ndi moyo wautali.” Tsono Mfumukazi Ataliya, atamva phokoso la asirikali ndi la anthu, adapita ku Nyumba ya Chauta. Atayang’ana, adaona mfumu itaima pa nsanja yake potsata mwambo wachifumu, atsogoleri ndi anthu oimba malipenga ali pafupi ndi mfumuyo. Anthu onse a m’deralo ankakondwa, namaimba malipenga. Pamenepo Ataliyayo adang’amba zovala zake, ndipo mofuula adati: “Akundiwukira! Akundiwukira!” Tsono Wansembe Yehoyada adalamula atsogoleri a gulu la nkhondo aja kuti: “Mtulutseni ameneyu pakati pa mizere mwandandayo. Ndipo aliyense amene amutsate, mumuphe ndi lupanga.” Wansembeyo adanenadi kuti: “Musamphere m’Nyumba ya Chauta ayi.” Choncho anthuwo adamugwira Ataliya uja, ndipo atafika naye ku nyumba ya mfumu, pakhomo lotchedwa la Akavalo, adamuphera pamenepo. Tsono Yehoyada adachititsa chipangano pakati pa Chauta ndi mfumu, pamodzi ndi anthu ake, kuti iwowo akhale anthu akeake a Chauta. Anthuwo adachitanso chipangano ndi mfumu. Choncho anthu onse a m’dzikomo adapita ku nyumba ya Baala nakaigwetsa. Maguwa ake ndi mafano ake adaŵaphwanyaphwanya. Kenako adapha Matani, wansembe wa Baala, patsogolo pa maguwa pomwepo. Tsono Wansembe Yehoyada adaika alonda ku Nyumba ya Chauta. Motero anthu a m’dzikomo adakondwa. Ndipo mu mzindamo mudakhala bata, Ataliya ataphedwa ku nyumba ya mfumu. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 132: 11, 12, 13-14, 17-18 Chauta wasankhula Ziyoni kuti akhale malo ake okhalamo (13). Chauta adalumbirira Davide momtsimikizira, Ndipo sadzasintha, adati: “Ndidzakhazika pa mpando wachifumu Mmodzi mwa ana ako aamuna. Chauta wasankhula Ziyoni kuti akhale malo ake okhalamo. Ngati ana ako aamuna asunga chipangano changa Ndi malamulo anga amene ndidzaŵaphunzitsa, Ana awonso adzakhala pa mpando wako wachifumu Mpaka muyaya.” Chauta wasankhula Ziyoni kuti akhale malo ake okhalamo. Chauta wasankhula Ziyoni, Akufuna kuti akhale malo ake okhalamo. Akuti: “Ameneŵa ndiwo malo anga opumuliramo mpaka muyaya. Ndidzakhala kuno chifukwa ndakufunitsitsa. Chauta wasankhula Ziyoni kuti akhale malo ake okhalamo. Davide ndidzammeretsera chiphukira kumeneko. Ndamukonzera nyale wodzozedwa wanga. Adani ake ndidzaŵaveka manyazi ngati nsalu, Koma iye yekhayo adzavala chisoti choŵala chachifumu.” Chauta wasankhula Ziyoni kuti akhale malo ake okhalamo. Aleluya: (Mateyo 5: 3) Ngodala anthu amene ali osauka mu mtima mwawo, pakuti Ufumu wa Kumwamba ndi wawo, Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU WOYERA 6:19-23 Yesu adati kwa ophunzira ake: “Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. Paja kumene kuli chuma chako, mtima wakonso umakhala komweko. Maso ndiwo nyale zounikira thupi la munthu. Ngati maso ako ali bwino, m’thupi mwako monse mumakhala kuŵala. Koma ngati maso ako sali bwino, m’thupi mwako monse mumakhala mdima. Tsono ngati kuŵala kumene kuli mwa iwe kusanduka mdima, mdima wakewo ngoopsa kopambana!” Mthenga wa Ambuye