LACHISANU LA MULUNGU WA 12 PACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Steven Limbani Kassim for 26 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Steven Limbani Kassim·26 June 2026·16:34·3 views
Ordinary Time
BUKU LACHIWIRI LA MAFUMU 25:1-12 SALIMO 137: 1-2, 3, 4-5, 6 MATEYU WOYERA 8:1-4

Mau a Mulungu a Lero

26 JUNE, 2026 LACHISANU LA MULUNGU WA 12 PACHAKA MAU WOYAMBA A MBUKU LACHIWIRI LA MAFUMU 25:1-12 ‭‬‬ Zedekiya adapandukira mfumu ya ku Babiloni. Ndiye pa chaka chachisanu ndi chinayi cha ufumu wa Zedekiyayo, mwezi wakhumi, pa tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadineza, mfumu ya ku Babiloni, adabwera ndi ankhondo ake onse, kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Adauzinga ndi zithando zankhondo ponseponse. Motero mzindawo udazingidwa ndi zithandozo mpaka chaka cha 11 cha ufumu wa Zedekiya. Tsono pa tsiku lachisanu ndi chinayi, pa mwezi wachinayi chaka chimenecho, pamene njala idali itakula kwambiri mu mzindamo, kotero kuti anthu adalibiretu chakudya m’dzikomo, malinga a mzindawo adabooledwa. Pamenepo Mfumu Zedekiya adathaŵa usiku pamodzi ndi ankhondo ake onse, kutulukira pa chipata cha pakati pa makoma aŵiri, pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababiloni adali atauzinga mzinda wonsewo. Ndipo adaloŵera cha ku Araba. Koma gulu lankhondo la ku Babiloni lidamlondola Mfumu Zedekiya nkukamugwirira m’zigwa za ku Yeriko. Ankhondo ake adabalalika namusiya.Apo aku Babiloni aja atamgwira Zedekiyayo, adapita naye kwa Nebukadineza, ku Ribula. Komweko Nebukadinezayo adagamula mlandu wa Zedekiya uja. Pompo adapha ana a Zedekiya iyeyo akupenya, ndipo adamukolowola maso Zedekiyayo, nammanga ndi maunyolo, nkupita naye ku Babiloni. Mwezi wachisanu, pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri la mwezi, chaka cha 19 cha ufumu wa Nebukadineza, mfumu ya ku Babiloni, Nebuzaradani, mkulu wa asirikali oteteza mfumu, mmodzi mwa alangizi ake, adadza ku Yerusalemu. Ndipo adatentha Nyumba ya Chauta, nyumba ya mfumu, ndi nyumba zina zonse za ku Yerusalemu. Adatentha nyumba yaikulu iliyonse. Tsono gulu lonse lankhondo la ku Babiloni limene lidali ndi mkulu wa asirikali uja, lidagumula malinga ozinga Yerusalemu.Anthu ena onse, amene adatsala mu mzindamo, ndi ena amene adathaŵa kupita kwa mfumu ya ku Babiloni, pamodzi ndi ena otsala, Nebuzaradani, mkulu wa asirikali uja, adaŵatenga kupita nawo ku Babiloni. Koma mkulu wa asirikaliyo adasiyako anthu ena osauka kwambiri a m’dzikomo, kuti azisamala minda ya mpesa ndi minda ina. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 137: 1-2, 3, 4-5, 6 Lilime langa likhale chete ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu (6ab). M’mbali mwa mitsinje ya ku Babiloni, Kumeneko tidakhala pansi Nkumalira tikakumbukira Ziyoni. Kumeneko tidapachika apangwe athu pa mitengo ya misondodzi. Lilime langa likhale chete ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu. Kumeneko anthu otigwira ukapolo adatipempha Kuti tiimbe nyimbo. Otizunza adatipempha kuti tisangalale, Iwo adati: “Tatiimbiraniko nyimbo ya ku Ziyoni.” Lilime langa likhale chete ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu. Tsono ife tidati: “Tingaimbe bwanji nyimbo ya Chauta Kuno ku dziko lachilendo?” Ndikakuiŵala iwe Yerusalemu, dzanja langa lamanja liwume. Lilime langa likhale chete ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu. Lilime langa likangamire ku mnakanaka, mkamwa mwanga, Ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu Ndi kukuona kuti ndiwe wondisangalatsa kwambiri. Lilime langa likhale chete ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu. Aleluya: (Yohane 10: 27) Nkhosa zanga zimamva mawu anga, akutero Ambuye; Ine ndimazidziŵa, ndipo zimanditsatira, Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU WOYERA 8:1-4 Yesu atatsika kuphiri kuja, anthu ambirimbiri adamutsatira. Tsono munthu wina wakhate adadzamugwadira nati: “Ambuye, mutafuna mungathe kundichiritsa.” Yesu adatambalitsa dzanja nkumukhudza, nati: “Chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha, ndipo adachiradi. Tsono Yesu adamuuza kuti: “Chenjera, usakambire wina aliyense zimenezi. Ingopita, ukadzionetse kwa wansembe, ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose zija. Umenewu ukhale umboni kwa anthu onse kuti wachiradi.” Mthenga wa Ambuye