LACHISANU LAMULUNGU WA 29 PACHAKA (II)
Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Medrick Mlava, DP for 23 October 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
23 OCTOBER, 2026 LACHISANU LAMULUNGU WA 29 PACHAKA (II) MAU OYAMBA; MAU A MKALATA YA PAULO KWA KWA AEFESO 4:1-6 Okondedwa, ine Paulo, womangidwa m’ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako. Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi, ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere. Pali thupi limodzi, ndiponso Mzimu Woyera mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene Mulungu adakuitanirani. Pali Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi. Pali Mulungu mmodzi, amene ali Atate a anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse, amagwira ntchito kudzera mwa onse, ndipo ali mwa onse. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 24: 1-2, 3-4AB, 5-6 Awa ndi anthu amene amafunitsitsa kuona nkhope yanu, Ambuye (6). Dziko lapansi ndi zonse za m’menemo ndi za Chauta, Dziko lonse lapansi Pamodzi ndi anthu onse okhalamo ndi ake. Pakuti iye ndi amene adaika dziko lapansi pa nyanja yaikulu, Adalikhazika pa mitsinje yozama. Awa ndi anthu amene amafunitsitsa kuona nkhope yanu, Ambuye. Ndani angayenere kukwera phiri la Chauta? Ndani angaime m’malo ake oyera? Ndi amene amachita zabwino ndi manja ake, Ndipo amaganiza zabwino mu mtima mwake. Ndi amene salingalira zonama. Awa ndi anthu amene amafunitsitsa kuona nkhope yanu, Ambuye. Adzalandira madalitso kwa Chauta, Ndipo Mulungu Mpulumutsi wake Adzagamula kuti alibe mlandu. Anthu otere ndiwo amene amafunitsitsa Chauta, Ndi amene amabwera kudzapembedza Mulungu wa Yakobe. Awa ndi anthu amene amafunitsitsa kuona nkhope yanu, Ambuye. Aleluya: (Mateyo 11: 25) Atate Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti mudaululira ana akhanda zinthuzi, zimene mudabisira anthu anzeru ndi ophunzira, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA 12:54-59 Yesu adauza anthu onse kuti: “Mukaona mtambo ukukwera kuzambwe, pompo mumati: ‘Mvula ikubwera!’ Ndipo imabweradi. Mphepo yakumwera ikamaomba, mumati: ‘Kutentha!’ Ndipo kumatenthadi. Inu anthu a chiphamaso, mumatha kuzindikira maonekedwe a dziko lapansi ndi a kuthambo, koma bwanji simutha kuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitika masiku omwe ano? Bwanji simutsimikiza nokha zoyenera kuchita? Monga pamene ukupita ndi mnzako wamlandu kwa woweruza, uyesetse kukonza mlanduwo mudakali pa njira, kuopa kuti angakupereke kwa woweruza, woweruzayo angakakupereke kwa msirikali, ndipo msirikaliyo angakakuponye m’ndende. Ndithu ndikunenetsa kuti sudzatulukamo mpaka utalipira zonse.” Mthenga wa Ambuye