LACHISANU LAMULUNGU WA 8 PACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Maxwell Kubalasa for 29 May 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Maxwell Kubalasa·29 May 2026·18:42·2 views
Ordinary Time
PETRO 4:7-13 SALIMO 96: 10, 11-12, 13 MARKO 11:11-26

Mau a Mulungu a Lero

29 MAY, 2026 ‭‭‬‬‬‬‬‬‬‬ LACHISANU LAMULUNGU WA PACHAKA (II) ‭‭‬‬‬‬‬‬‬‬‬‬‬‬ MAU OYAMBA, MAU A MKALATA YA PETRO 4:7-13 Abale, chimaliziro cha zonse chayandikira. Nchifukwa chake, khalani maso ndinso mukhale odziletsa, kuti muthe kupemphera. Chachikulu ndi chakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimakwirira machimo ochuluka. Poyenderana, mudzisamalirana bwino mosadandaula. Aliyense, mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitawo, ogwiritsa bwino ntchito mphatso za mitundumitundu zochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amalankhula, mawu ake akhaledi mawu ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu wampatsa, kuti pa zonse, Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Inu okondedwa, musazizwe ndi chimoto cha masautso chimene chakugwerani, kuti muyesedwe nacho. Musaganize kuti zimene zakuonekeranizo nzachilendo. Koma kondwerani, popeza kuti mulikumva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, kuti podzaoneka ulemerero wake, mudzasangalale kwakukulu. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 96: 10, 11-12, 13 Chauta akubwera kudzaweruza dziko lapansi (13b). Uzani mitundu ya anthu kuti: “Chauta ndiye Mfumu.” Dziko lonse lidakhazikitsidwa molimba, Silidzagwedezeka konse. Adzaweruza mitundu yonse ya anthu mwachilungamo. Chauta akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Za Kumwamba zisangalale, zapansi pano zikondwere, Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse za m’menemo. Minda ikondwe pamodzi ndi zonse za m’menemo. Mitengo ya m’nkhalango idzaimba mokondwa. Chauta akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Gwadani pamaso pa Chauta, Ambuye athu, Pamene zabwera kudzalamulira dziko lapansi. Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo, Adzalamulira anthu a mitundu yonse moona. Chauta akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Aleluya: (Yohane 15: 26) Sindinutu mudandisankha Ine ayi, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa, *Aleluy. MTHENGA WA AMBUYE MONGA ADALEMBERA MARKO 11:11-26 Yesu ataloŵa mu Yerusalemu, adakaloŵa m’Nyumba ya Mulungu, nayang’anayang’ana zonse. Tsono poti chisisira chidali chitagwa, adatuluka napita ku Betaniya, pamodzi ndi ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja. M’maŵa mwake, pamene iwo ankachoka ku Betaniya kuja, Yesu adamva njala. Ataona mkuyu chapatali potero, uli ndi masamba, adapitapo kuti kapena nkupezamo mkuyu. Koma atafika, sadapezemo mkuyu, koma masamba okhaokha, pakuti siidali nyengo ya mkuyu. Pamenepo adauza mtengowo kuti: “Mtengo iwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya, wina aliyense asadzadyekonso zipatso zako.” Mawu ameneŵa ophunzira ake aja adaŵamva. Iwo atafika ku Yerusalemu, Yesu adaloŵa m’Nyumba ya Mulungu, nayamba kutulutsa anthu amene ankachita malonda m’menemo. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama, ndinso mipando ya ogulitsa nkhunda. Sadalolenso kuti wina aliyense azidutsa m’mabwalo a Nyumbayo atasenza chinthu ayi. Pambuyo pake adayamba kuŵaphunzitsa, naŵauza kuti: “Paja Malembo akuti: ‘Nyumba yanga ikhale Nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.’ Koma inu mwaisandutsa phanga la lobisaliramo achifwamba.” Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo atamva zimenezi, adayamba kufunafuna njira yoti amuphere. Pakutitu ankachita naye mantha, poona kuti anthu onse ankadabwa nazo zimene Iye ankaphunzitsa. Kutayamba kuda, Yesu ndi ophunzira ake adatulukamo mu mzindamo. M’maŵa mwake, m’mamaŵa ndithu, iwo akuyenda mu msewu, adaona mkuyu uja waumiratu wonse ndi mizu yomwe. Apo Petro adakumbuka zijazi, ndipo adauza Yesu kuti: “Aphunzitsi, taonani, mkuyu uja mudautembererawu wauma.” Yesu adaŵayankha kuti: “Zoonadi, ngati mukhulupirira Mulungu, mungathe kulamula phiri ili kuti: ‘Nyamuka, kadziponye m’nyanja!’ Mutanena ndi mtima wosakayika, ndi kukhulupirira ndithu, kuti zimene mukunenazo zichitikadi, ndithu zidzachitikadi, monga momwe mwaneneramo. Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti, m’mapemphero mwanu mukapempha Mulungu chinthu chiri chonse, muzikhulupirira kuti mwalandira, ndipo mudzachilandiradi. Ndipo pamene mukuti mupemphere, muziyamba mwakhululukira mnzanu ngati muli naye kanthu. Mukatero, Atate anunso amene ali Kumwamba adzakukhululukirani machimo anu. Koma ngati inu simukhululukira anzanu, Atate anunso amene ali Kumwamba sadzakhululukira machimo anu.” Mthenga wa Ambuye