LACHISANU LAMULUNGU WA 9 PACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Rev. Deacon Justin Malewezi Jnr for 5 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Rev. Deacon Justin Malewezi Jnr·5 June 2026·12:06·5 views
Ordinary Time
TIMOTEO 3:10-17 SALIMO 119: 157, 160, 161, 165, 166, 168 MARKO 12:35-37

Mau a Mulungu a Lero

5 JUNE, 2026 ‭‭‬‬‬‬‬‬‬‬Kulemekeza Boniface Bishop ndi Mmalitri Woyera LACHISANU LAMULUNGU WA 9 PACHAKA (II) ‭‭‬‬‬‬‬‬‬‬‬‬‬‬ MAU OYAMBA, MAU A MKALATA YACHIWIRI YA PAUL KWA TIMOTEO 3:10-17 Wokondedwa, tsono iwe wakhala ukunditsatira mu zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga, mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adandigwera ku Antiyokeya, ku Ikoniyo ndi ku Lisitara kuja. Ndidazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi. Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, m’menemo anthu ochimwa ndi onama, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanamiza ena nkumanamizidwanso iwo omwe. Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira, ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa. Ukudziŵanso kuti kuyambira udakali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 119: 157, 160, 161, 165, 166, 168 Anthu okonda malamulo anu amakhala ndi mtendere waukulu (165a). Anthu ondizunza ndiponso adani anga ngochuluka, Koma sindimasiyana nawo malamulo anu. Anthu okonda malamulo anu amakhala ndi mtendere waukulu. Mawu anu ndi oona okhaokha, Malangizo anu onse olungama ngamuyaya. Anthu okonda malamulo anu amakhala ndi mtendere waukulu. Mafumu amandizunza popanda chifukwa, Koma mtima wanga umaopa mawu anu. Anthu okonda malamulo anu amakhala ndi mtendere waukulu. Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, Palibe china chotha kuŵagwetsa. Anthu okonda malamulo anu amakhala ndi mtendere waukulu. Ndimakhulupirira kuti mudzandipulumutsa, Inu Chauta, Ndipo ndimatsata malamulo anu. Anthu okonda malamulo anu amakhala ndi mtendere waukulu. Ndimatsata malamulo anu ndi malangizo anu, Pakuti makhalidwe anga onse mukuŵaona. Anthu okonda malamulo anu amakhala ndi mtendere waukulu. Aleluya: (Yohane 14: 23) Ngati munthu andikonda, adzatsata mawu anga. Atate anga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye, Aleluya. MTHENGA WA AMBUYE MONGA ADALEMBERA MARKO 12:35-37 Pamene Yesu ankaphunzitsa anthu m’Nyumba ya Mulungu, adawafunsa kuti: “Kodi bwanji aphunzitsi a Malamulo amati Mpulumutsi Wolonjezedwa uja ndi mwana wa Davide? Paja Davide, ndi nzeru zochokera kwa Mzimu Woyera, adati: ‘Chauta adauza Mbuye wanga kuti: ‘Khala ku dzanja langa lamanja, mpaka nditasandutsa adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’ Davide weniweniyo akutchula Mpulumutsi Wolonjezedwa uja kuti ‘Mbuye wake.’ Tsono angakhale mwana wakenso bwanji?” Mthenga wa Ambuye