LACHITATU LA MULUNGU WA 10 PACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Gift Phiri, OFM for 10 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Gift Phiri, OFM·10 June 2026·17:53·7 views
Ordinary Time
BUKU LOYAMBA LA MAFUMU 18:20-39 SALIMO 16: 1B-2AB, 4, 5AB NDI 8, 11 MATEYU WOYERA 5:17-19

Mau a Mulungu a Lero

10 JUNE, 2026 LACHITATU LA MULUNGU WA 10 PACHAKA MAU WOYAMBA A MBUKU LOYAMBA LA MAFUMU 18:20-39 ‭‬ Ahabu adatumiza mawu kwa onse aku Israele, ndipo adasonkhanitsa aneneri a Baala ku Phiri la Karimele. Eliya adasendera pafupi ndi anthu onsewo, naŵafunsa kuti: “Kodi mudzakhala anthu a mitima iŵiri mpaka liti? Ngati Chauta ndiye Mulungu, mtsateni. Koma ngati Baala ndiye Mulungu, tsatani iyeyo.” Anthuwo sadamuyankhe ndi liwu limodzi lomwe. Tsono Eliya adauza anthu aja kuti: “Ine ndatsala ndekha mwa aneneri a Chauta, koma aneneri a Baala alipo 450 pamodzi. Bwerani ndi ng’ombe zamphongo ziŵiri. Iwo asankhepo okha ng’ombe imodzi, ndipo aidule nthulinthuli ndi kuziika pa nkhuni nthulizo, koma asasonkhepo moto ayi. Inenso ndidula ng’ombe inayo nthulinthuli, ndi kuikanso nthulizo pa nkhuni, koma osasonkhapo moto ayi. Inu mutame dzina la mulungu wanu mopemba, inenso nditama dzina la Chauta mopemba. Tsono Mulungu amene ayankhe potumiza moto, ameneyo ndiyedi Mulungu.” Pamenepo anthu onsewo adati: “Ayi, mwanena bwino.” Tsono Eliya adauza aneneri a Baala aja kuti: “Yambani ndinu. Sankhulani ng’ombe yamphongo imodzi, muikonze, poti mwachuluka. Tsono mutame dzina la mulungu wanu mopemba, koma musasonkhe moto ayi.” Iwowo adatenga ng’ombe yamphongo imene adaŵapatsa, naipha. Tsono adatama dzina la Baala mopemba, kuyambira m’maŵa mpaka masana, ponena kuti: “Inu a Baala, tiyankheni ife.” Aneneri a Baala aja ankalumphalumpha movina, kuzungulira guwa limene adamangalo, koma sipadamveke ndi liwu lomwe, padalibe woyankha. Tsono nthaŵi yamasana ndithu Eliya adayamba kuŵaseka, naŵauza kuti: “Fuulani kwambiri, suja mukuti iyeyo ndi mulungu! Mwina mwaketu watanganidwa, kapena wapita kwina kukadzithandiza, kapena ali pa ulendo, kaya kapena ali mtulo, ndiye kamdzutsenitu.” Aneneri a Baalawo ankafuula kwambiri, nadzichekacheka ndi malupanga ndi mipeni potsata miyambo yawo, mpaka magazi chuchuchu m’mabalawo. Dzuŵa litapendeka, adakhala akufuulabe mopenga kufikira nthaŵi yoperekera nsembe idakwana. Komabe kudali ziii! Osamveka ndi liwu lomwe. Padalibe woyankha, padalibe ndi mmodzi yemwe wosamalako zimenezo. Pamenepo Eliya adauza anthu onse aja kuti: “Senderani pafupi ndi ine.” Anthu onsewo adasenderadi kwa iyeyo. Tsono Eliya adakonza guwa la Chauta, limene lidali litagwetsedwa. Adatenga miyala khumi ndi iŵiri potsata chiŵerengero cha mafuko a ana a Yakobe, amene Chauta adamuuza kuti dzina lake lidzakhala Israele. Ndi miyalayo adamangira guwa lotamandirapo Chauta. Tsono adakumba ngalande kuzungulira guwalo. Kukula kwa ngalandeyo kudali ngati moloŵa mitsuko inayi ya madzi. Adaika nkhuni zija m’malo mwake, nadula ng’ombe ija nthulinthuli, nkuika nthulizo pankhunipo. Pambuyo pake adauza anthu kuti: “Dzazani mitsuko inayi ndi madzi, muŵathire pa nyama ya nsembeyo, ndi pa nkhunizo.” Ndipo adaŵauza kuti: “Bwerezaninso kachiŵiri.” Anthu aja adathiranso madziwo kachiŵiri. Adaŵauzanso kuti: “Thiraninso kachitatu.” Iye adateronso kachitatu. Madziwo adayenderera kuzungulira guwalo, nadzaza ngalande yonse. Itakwana nthaŵi yake yopereka nsembe, Mneneri Eliya adasendera pafupi ndi guwa nati: “Inu Chauta, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Israele, lero zidziŵike kuti Inuyo ndiye Mulungu m’dziko la Israele, ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, ndiponso kuti ndachita zonsezi chifukwa mwanena ndinu. Mundiyankhe, Inu Chauta, mundiyankhe, kuti anthu aŵa adziŵe kuti Inu Chauta ndinu Mulungu, ndipo kuti atembenuke mtima.” Pomwepo moto wa Chauta udagwa, nunyeketsa nsembe yopserezayo, nkhunizo, miyala ija ndi dothi lomwe. Motowo udaphwetsa ndi madzi omwe amene adali m’ngalande aja. Tsono anthu onse ataona zimenezo, adadzigwetsa pansi nanena mokweza kuti: “Chauta ndiyedi Mulungu! Chauta ndiyedi Mulungu!” Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 16: 1B-2AB, 4, 5AB NDI 8, 11 Ndisungeni Inu, Chauta, pakuti ndinu kothawira kwanga (1b). Ndisungeni, Ambuye, nthawi zonse, Chifukwa ndinu kothawira kwanga; Ndimanena kuti: “Ndinu Mbuye wanga.” Ndisungeni Inu, Chauta, pakuti ndinu kothawira kwanga. Onse opemphera milungu ina amadziyitanira tsoka. Musapereke nsembe kwa timilungu tina Kapena kutchula maina awo pakamwa panu. Ndisungeni Inu, Chauta, pakuti ndinu kothawira kwanga. Ambuye, ndinu moyo wanga, Ndinu amene mumanditchinjiriza. Mulungu wanga ndimamuika patsogolo panga; Sindidzaopa kanthu pamene ali pafupi nane. Ndisungeni Inu, Chauta, pakuti ndinu kothawira kwanga. Mundionetse njira yopitira ku moyo wosatha, Komanso zisangalatso zimene Inu mupereka, Ndi zabwino zimene mumapatsa anthu anu. Ndisungeni Inu, Chauta, pakuti ndinu kothawira kwanga. Aleluya: (Salimo 25: 4b, 5a) Ndiphunzitseni njira zanu, Inu Chauta Mulungu wanga, ndipo munditsogolere ku choona chanu, Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU WOYERA 5:17-19 Yesu adauza ophunzira ake kuti: “Musamaganiza kuti ndidadzathetsa Malamulo a Mose ndiponso zophunzitsa za aneneri ayi. Inetu sindidadzere kudzaŵathetsa, koma kudzaŵafikitsa pachimake penipeni. Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisadathe, sipadzachoka kalemba nkakang’ono komwe, kapena kansonga ka lembo pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika. Choncho aliyense wonyozera limodzi mwa malamulo ameneŵa, ngakhale laling’ono chotani, nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamng’ono ndithu mu Ufumu wa Kumwamba. Koma aliyense amene amaŵatsata nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba.” Mthenga wa Ambuye