LACHITATU LA MULUNGU WA 11 PACHAKA
Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Charles Duncan for 17 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
17 JUNE, 2026 LACHITATU LA MULUNGU WA 11 PACHAKA MAU WOYAMBA A MBUKU LACHIWIRI LA MAFUMU 2:1,6-14 Idafika nthaŵi imene Chauta adafuna kutenga Eliya m’kamvulumvulu kunka Kumwamba. Tsiku limenelo Eliya ndi Elisa adali pa ulendo kuchokera ku Giligala. Pambuyo pake Eliya adauza Elisa kuti: “Iwe, chonde ubakhala pano, poti ine Chauta wandituma kuti ndipite ku Yordani.” Koma Elisa adauza Eliyayo kuti: “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine sindikusiyani konse.” Motero aŵiri onsewo adapitiriza ulendo wawo. Anthu makumi asanu amu gulu la aneneri aja adapita nawo, ndipo adakaimirira chapatali potero, pamene Eliya ndi Elisa adakaima pa gombe la mtsinje wa Yordani. Apo Eliya adatenga mkanjo wake naupinda, kenaka adamenya madzi ndi mkanjowo. Tsono madziwo adapatukana, ena kwina ena kwina, mpaka aneneri aŵiriwo adaoloka pouma. Ataoloka, Eliya adauza Elisa kuti: “Undipemphe choti ndikuchitire ndisadakusiye.”Elisa adati: “Ndikukupemphani kuti ndilandire chigawo chachikulu cha mphamvu zanu za uneneri.” Eliya adauza Elisayo kuti: “Wapempha chinthu chapatali. Komabe ukandipenya pa nthaŵi imene ndikukusiya, zimene wapemphazi zidzakuchitikiradi. Koma ukapanda kundipenya, sizidzachitika.” Tsono iwowo akuyendabe ndi kumakamba, adangoona galeta lamoto ndi akavalo ake a moto zikuŵasiyanitsa aŵiriwo. Ndipo Eliya adakwera Kumwamba m’kamvulumvulu. Elisa adaona zimenezi nafuula kuti: “Bambo wanga, Bambo wanga! Magaleta a Aisraele ndi anthu ake okwera pa akavalo.” Ndipo sadamuonenso Eliyayo. Tsono Elisa adagwira zovala zake nazing’amba paŵiri. Kenaka adatenga mkanjo wa Eliya umene udagwa, nabwerera nkukaima pa gombe la Yordani. Adagwira mkanjo wa Eliyawo namenya nawo madzi aja, nati: “Ali kuti Chauta, Mulungu wa Eliya?” Atamenya madziwo choncho, madzi aja adapatukana, ena kwina, ena kwina. Ndipo Elisa adaoloka. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 31: 20, 21, 24 Limbani mtima, inu anthu onse okhulupirira Chauta (25). Ndi waukulu ubwino wanu, Inu Chauta. Umene mwaŵasungira anthu okumverani, Umene mwaŵachitira anthu othaŵira kwa Inu, Aliyense waona zimenezi. Limbani mtima, inu anthu onse okhulupirira Chauta. Anthu anu mumaŵabisa pamalo pamene pali Inu, Kuti muŵateteze ku ziwembu za adani awo. Mumaŵasunga bwino ndi kuŵatchinjiriza, Kuti anthu angakangane nawo. Limbani mtima, inu anthu onse okhulupirira Chauta. Kondani Chauta, inu nonse anthu oyera mtima. Chauta amasunga anthu okhulupirika, Koma amalanga koopsa anthu odzikuza. Limbani mtima, inu anthu onse okhulupirira Chauta. Aleluya: (Yohane 14: 23) Ngati munthu andikonda Ine, adzatsata mawu anga. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye, Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU WOYERA 6:1-6,16-18 Yesu adati kwa ophunzira ake: “Chenjerani, musachite ntchito zanu zabwino pamaso pa anthu ndi cholinga choti akuoneni. Mukatero, simudzalandira mphotho kwa Atate anu amene ali Kumwamba. Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modzionetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m’nyumba za mapemphero, ndiponso m’misewu ya m’mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yawo. Koma iwe ukamapereka zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziŵe zimene dzanja lako lamanja likuchita. Ukatero, zachifundo zakozo zidzakhala zodziŵa iwe wekha. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho. Pamene mukupemphera, musachite monga anthu achiphamaso aja. Iwowo amakonda kuimirira ndi kupemphera m’nyumba za mapemphero ndi pa mphambano za miseu ya m’mizinda. Amachita zimenezi kuti anthu aŵaone. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yawo. Koma iwe, pamene ukuti upemphere, loŵa m’chipinda chako, tseka chitseko, ndipo upemphere kwa Atate ako amene ali mseri. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho. Pamene mukusala zakudya, musamaonetsa nkhope zachisoni monga amachitira anthu achiphamaso aja. Iwo amaipitsa nkhope kuti anthu aone kuti akusala zakudya. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yawo. Koma iwe, pamene ukusala zakudya, samba m’maso nkudzola mafuta kumutu, kuti anthu asadziŵe kuti ukusala zakudya. Koma Atate ako amene ali osaoneka ndiwo adziŵe. Ndipo Atate akowo, amene amaona zobisika, adzakupatsa mphotho.” Mthenga wa Ambuye