LACHITATU LA MULUNGU WA 12 PACHAKA - CHAKA CHA KUBADWA KWA YOHANE MBATIZI

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Steven Limbani Kassim for 24 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Steven Limbani Kassim·24 June 2026·19:41·2 views
Ordinary Time
BUKU LA MNENERI YESAYA 49:1-6 SALIMO 139:1-3,13-14,15 BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI 13:22-26 LUKA 1:57-66,80

Mau a Mulungu a Lero

24 JUNE, 2026 CHAKA CHA KUBADWA KWA YOHANE MBATIZI MAU OYAMBA; MAU A MBUKU LA MNENERI YESAYA 49:1-6 ‭‬‬ ‭‭‬‬‬‬‭Mverani inu anthu a ku maiko a m'mphepete mwa nyanja, tcherani khutu, inu anthu akutali. Chauta adandiitana ndisanabadwe, adanditchula dzina ndidakali m'mimba mwa amai anga. Adasandutsa pakamwa panga kuti pakhale ngati lupanga lakuthwa. Adanditchinjiriza ndi dzanja lake. Adandisula ngati muvi wakuthwa, nandibisa m'phodo mwake. Adandiwuza kuti, “Iwe Israele ndiwe mtumiki wanga. Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.” Koma ndidati, “Ndagwira ntchito yopanda phindu. Ndangoononga mphamvu zanga pachabe.” Komabe zondiyenerera zili m'manja mwa Chauta, mphotho yanga ili m'manja mwa Mulungu wanga. Chauta ndi amene adandiwumba m'mimba mwa amai anga kuti ndikhale mtumiki wake, kuti ndibweze fuko la Yakobe kwa Iye, ndipo kuti ndisonkhanitse Aisraele pafupi ndi Iye. Choncho ndimalemekezeka m'maso mwa Chauta, ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga. Chautayo akunena kuti, “Nchinthu chochepa kwambiri kuti ukhale mtumiki wanga, kuti udzutse mafuko a Yakobe ndi kuŵabweza kwao Aisraele amene adapulumuka. Ndidzakusandutsa kuŵala kounikira mitundu ina ya anthu, kuti chipulumutso changa chikafike mpaka ku mathero a dziko lapansi.” ‭‭Mau a Ambuye‬‬‬‬‬‬‬‬‬‬ NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 139:1-3,13-14,15 Ndikukutamandani, Inu amenen mudandilenga mwaluso. Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali. Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona, mumadziŵa njira zanga zonse. Ndikukutamandani, Inu amenen mudandilenga mwaluso. Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Ndikukutamandani, Inu amenen mudandilenga mwaluso. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. MAU ACHIWIRI: MAU A MBUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI 13:22-26 Pambuyo pake Mulungu adamchotsa Sauloyo, naika Davide kuti akhale mfumu yao. Za iyeyu Mulungu adanena kuti, ‘Ndapeza Davide, mwana wa Yese, ndiye munthu wanga wapamtima, amene adzachita zonse zimene Ine ndifuna.’ Mwa zidzukulu za Davideyo Mulungu adasankha Yesu kuti akhale Mpulumutsi wa Aisraele, monga momwe adaalonjezera kale. Iyeyo asanayambe ntchito, Yohane ankalalikira Aisraele onse kuti atembenuke mtima ndi kubatizidwa. Pamene Yohane anali pafupi kutsiriza ntchito yake, adafunsa anthu kuti, ‘Kodi inu mumayesa kuti ine ndine yani? Inetu sindine amene mukumuyembekezayo ai. Koma pakubwera wina pambuyo panga amene ine sindili woyenera ngakhale kumvula nsapato zake.’ “Ine abale, zidzukulu za Abrahamu, ndi ena nonse oopa Mulungu, uthenga wa chipulumutsowu Mulungu watumizira ife. Mau a Ambuye Aleluya: ‭(Lk. 1:76) [76] Tsono mwana iwe, udzatchedwa mneneri wa Mulungu Wopambanazonse, chifukwa udzatsogola pamaso pa Ambuye, kuti ukonzeretu njira zao. Aleluya.‬‬‬ MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA 1:57-66,80 ‭ Nthaŵi yakuti Elizabeti achire idakwana, ndipo adabala mwana wamwamuna. [58] Anzake ndi abale ake atamva kuti Ambuye amchitira chifundo chachikulu chotere, adakondwera naye pamodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu mwanayo atabadwa, adadza naye kuti amuumbale, nafuna kumutcha dzina la bambo wake Zakariya. Koma mai wake adakana, adati, “Iyai, koma atchedwe Yohane.” Pamenepo anthuwo adamuuza kuti, “Koma pakati pa abale anu palibe amene ali ndi dzina limeneli.” Tsono adalankhula ndi bambo wake ndi manja, namufunsa kuti, “Mukufuna kuti timutche dzina lanji?” Zakariya adapempha cholemberapo, nalembapo kuti, “Dzina lake ndi Yohane.” Anthu onsewo adazizwa. Pomwepo Zakariya adathanso kulankhula, nayamba kutamanda Mulungu. [ Anzao onse aja adagwidwa ndi mantha, ndipo mbiri ya zimenezi idawanda ku dera lonse la mapiri a ku Yudeya. Anthu onse amene ankazimva, ankazilingalira m'mitima mwao, ndi kumadzifunsa kuti, “Kodi mwana ameneyu adzakhala munthu wotani?” Pakuti zinkachita kuwonekeratu kuti Ambuye anali naye. Mwana uja Yohane ankakula nasanduka wa mkhalidwe wamphamvu. Pambuyo pake adakhala ku chipululu mpaka tsiku limene adadziwonetsa poyera pakati pa Aisraele. Mthenga wa Ambuye