LACHITATU LA MULUNGU WA 16 PACHAKA - CHAKA CHA MARIA MAGADALENA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Elizeo Nthalika, DP for 22 July 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Elizeo Nthalika, DP·22 July 2026·15:49·2 views
Ordinary Time
SOLOMONI 3:1-4AB AKORINTO5:14-17 SALIMO 63:2,2-4, 5-6,8-9 YOHANE 20:1-2,11-18

Mau a Mulungu a Lero

22 JULY, 2026 CHAKA CHA MARIA MAGADALENA MAU OYAMBA; MAU A MBUKU LA NYIMBO YA SOLOMONI 3:1-4AB Ndampeza amene mtima wanga umamkonda ‭Usiku uliwonse ndili gone pabedi panga ndinkangomufunafuna amene mtima wanga umamkonda. Ndidamufunafuna koma osampeza. Ndidamuitana, koma iye osandiyankha. Ndiye ndidati, “Ai, tsopano ndidzuka ndi kuloŵa mu mzinda, m'miseu ndi m'mabwalo. Ndimufunafuna amene mtima wanga umamkonda.” Ndidamufunafunadi, koma osampeza. Alonda adandipeza pamene ankayendera mzinda. Ndidaŵafunsa kuti, “Kodi mwandiwonerako amene mtima wanga umamkonda?” Ndidangoti iwo aja ntaŵapitirira pang'ono, ndampeza amene mtima wanga umamkonda. KAPENA MAU A MKALATA YACHIWIRI YA PAULO KWA AKORINTO5:14-17 Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano ‭Chikondi cha Khristu ndicho chimatiwongolera mokakamiza, popeza kuti tikudziŵa mosakayika konse kuti Munthu mmodzi adafera anthu onse, ndiye kuti pamenepo onse adafa. Iye adafera anthu onse, kuti amene ali ndi moyo, asakhalenso ndi moyo wofuna kungodzikondweretsa okha, koma azikondweretsa Iye amene adaŵafera, nauka kwa akufa chifukwa cha iwowo. Nchifukwa chake kuyambira tsopano ife sitiganiziranso za munthu aliyense potsata nzeru za anthu chabe. Ngakhale kale tinkaganiza za Khristu potsata nzeru za anthu chabe, koma tsopano sitiganizanso za Iye motero. Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano. ‭‭Mau a Ambuye‬‬‬‬‬‬‬‬‬‬ NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 63:2,2-4, 5-6,8-9 ‭ Inu Mulungu, Mulungu wanga, Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu ‭Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi. Inu Mulungu, Mulungu wanga, Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu Ndikukhumbira kukuwonani m'malo anu oyera ndi kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu. chikondi chanu nchabwino kupambana moyo. Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga. Inu Mulungu, Mulungu wanga, Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera. Mudzandikhutitsa ndi zonona, ndipo ndidzakutamandani ndi mau osangalala. Inu Mulungu, Mulungu wanga, Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu Inu mwakhala chithandizo changa, motero ndikuimba ndi chimwemwe pansi pa mapiko anu. Mtima wanga ukukangamira Inu, dzanja lanu lamanja likundichirikiza. Inu Mulungu, Mulungu wanga, Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu Aleluya: Mai iwe, ukuliranji? Ukufuna yani? Aleluya MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE 20:1-2,11-18 ‭Pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, m'mamaŵa ndithu kudakali kamdima, Maria wa ku Magadala adadza ku manda a Yesu. Adaona kuti chimwala chija chachotsedwa kale pa khomo la mandawo. Choncho adathamanga nakafika kwa Simoni Petro, ndi kwa wophunzira wina uja amene Yesu ankamukonda kwambiri. Adaŵauza kuti, “Aŵachotsa Ambuye m'manda muja, ndipo sitikudziŵa kumene akaŵaika.” Maria adakhalabe chilili panja pafupi ndi manda, akulira. Akulira choncho, adaŵerama kusuzumira m'mandamo,naona angelo aŵiri ovala zovala zoyera. Angelowo adaakhala pansi, wina kumutu, wina kumapazi pamalo pamene padaagona mtembo wa Yesu paja. Iwo adamufunsa kuti, “Inu mai, mukuliranji?” Iye adati, “Chifukwa aŵachotsa Ambuye anga ndipo sindikudziŵa kumene akaŵaika.” Atanena zimenezi adacheuka, naona Yesu ataimirira pomwepo, koma sadamzindikire kuti ndi Yesu. Tsono Yesu adamufunsa kuti, “Mai iwe, ukuliranji? Ukufuna yani?” Maria ankayesa kuti ndi wakumundako, motero adamuuza kuti, “Bambo, ngati mwaŵachotsa ndinu, mundiwuze kumene mwakaŵaika, kuti ndikaŵatenge.” Yesu adati, “Maria!” Iye adacheuka, nanena kuti, “Raboni!” (Ndiye kuti “Aphunzitsi” pa chihebri) Yesu adamuuza kuti, “Usandigwire, pakuti sindinakwerebe kupita kwa Atate. Koma pita kwa abale anga, ukaŵauze kuti, ‘Ndikukwera kupita kwa Atate anga, omwe ali Atate anunso, Mulungu wanga, yemwe ali Mulungu wanunso.’ Maria wa ku Magadalayo adapita, nakauza ophunzira aja kuti, “Ndaŵaona Ambuye,” ndipo adaŵakambira zimene Ambuyewo adaamtuma. Mthenga wa Ambuye