LACHITATU LA MULUNGU WA 30 PACHAKA - KULEMEKEZA SIMON NDI JUDE WOYERA
Watch this Catholic homily in Chichewa by Deacon Anthony Kavinya for 28 October 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
28 OCTOBER, 2026 KULEMEKEZA SIMON NDI JUDE WOYERA MAU A MKALATA YA PAULO KWA AEFESO 2:19-22 Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya. Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye. Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 19: 1-2, 3-4ab Mau aowo amafika mpaka ku mathero a dziko (4a). Zakumwamba zimalalika ulemerero wa Mulungu, thambo limasonyeza ntchito za manja ake. Usana umasimbira zimenezo usana unzake, usiku umadziŵitsa zimenezo usiku unzake. Mau aowo amafika mpaka ku mathero a dziko Palibe kulankhula, palibe kunena mau aliwonse. Liwu lao silimveka konse. Komabe uthenga wao umafalikira pa dziko lonse lapansi. Mau aowo amafika mpaka ku mathero a dziko. Mulungu adamangira dzuŵa nyumba m'thambomo. Mau aowo amafika mpaka ku mathero a dziko ALELUYA: Tikukutamandani, Inu Mulungu, tikukutchulani Ambuye, Gulu la Apostoli anu limayimba nyimbo zotamanda Inu ALELUYA. MTHENGA WABWINO WA LUKA 6:12-19 Masiku amenewo Yesu adapita ku phiri kukapemphera, ndipo adachezera usiku wonse akupemphera kwa Mulungu. Kutacha adaitana ophunzira ake, nasankhapo khumi ndi aŵiri. Adaŵatcha “atumwi.” Anthu ake anali aŵa: Simoni (amene Yesu adamutcha dzina loti Petro) ndi mbale wake Andrea; Yakobe ndi Yohane; Filipo ndi Bartolomeo; Mateyo ndi Tomasi; Yakobe (mwana wa Alifeyo) ndi Simoni (wa m'chipani chandale cha Azelote;) Yudasi (mwana wa Yakobe) ndiponso Yudasi Iskariote (amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.) Yesu adatsika phiri pamodzi ndi ophunzira ake, naima pa chidikha. Panali khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi anthu ena ambirimbiri ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi ku Yerusalemu, ndi ku mbali yakunyanja, ku Tiro, ndi ku Sidoni. Iwo adabwera kudzamva mau ake, ndiponso kuti Iye aŵachiritse. Anthu amene ankasautsidwa ndi mizimu yoipa, amenewonso Iye ankaŵachiritsa. Anthu onsewo ankafuna kumkhudza, chifukwa mphamvu zinkatuluka mwa Iye ndi kuŵachiritsa onse. Mthenga wa Ambuye