LACHITATU LA MULUNGU WA 8 PACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Maxwell Kubalasa for 27 May 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Maxwell Kubalasa·27 May 2026·18:42·3 views
Ordinary Time
PETRO 1:18-25 SALIMO 147: 12-13, 14-15, 19-20 MARKO 10:32-45

Mau a Mulungu a Lero

27 MAY, 2026 LACHITATU LA MULUNGU WA 8 PACHAKA MAU OYAMBA; MAU A MKALATA YOYAMBA YA PETRO 1:18-25 Ndine, Petro, mthumwi ya Yesu Khristu. Ndikulemba kalatayi kwa inu, osankhidwa ake a Mulungu, amene muli obalalika ku maiko aku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asia ndi Bitiniya. Mukudziwa bwino chimene adakuombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe, limene mudalilandira kwa makolo anu. Sadakuomboleni ndi ndalama zotha kuonongeka zija, siliva kapena golide ayi. Adakuombolani ndi magazi a mtengo wapatali a Khristu, amene adakhala ngati mwana wa nkhosa, wopanda banga kapena chilema. Iyeyo Mulungu adamusankhiratu dziko lapansi lisadalengedwe, koma wamuonetsa nthawi yotsiriza ino chifukwa cha inu. Kudzera mwa Iye, mumangokhulupirira Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa, nampatsa ulemerero. Ndipo choncho chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu, zili mwa Mulungu. Mwayeretsa mitima yanu pakumvera choona, kotero kuti mukondana ndi Akhristu anzanu moona.Nchifukwa chake muzikondana ndi mtima wonse mosafookera. Pakuti mwachita kubadwanso m’moyo wake. Siwochokera ku mbewu yotha kuonongeka, koma mbewu yosatha kuonongeka. Mbewuyi ndi mawu a Mulungu, mawu a moyo ndi wokhala mpakampaka. Paja mawu a Mulungu amanena kuti anthu onse ali ngati udzu. Ulemerero wawo uli ngati duwa la ku thengo. Udzu umauma, ndipo duwa limathothoka, koma mawu a Ambuye ngokhalapo mpaka muyaya. Mawu amenewa ndi Uthenga Wabwino umene walalikidwa kwa inu. ‭‭Mau a Ambuye‬‬ NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 147: 12-13, 14-15, 19-20 Tamanda Chauta, iwe Yerusalemu (12a). Tamanda Chauta, iwe Yerusalemu. Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni. Paja amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako. Amadalitsa anthu amene ali mwa iwe. Tamanda Chauta, iwe Yerusalemu. Amadzetsa mtendere m’malire a dziko lako, Amakudyetsa pokupatsa ufa wa tirigu wosalala. Akapereka lamulo pa dziko lapansi, Mawu ake amayenda mwaliŵiro. Tamanda Chauta, iwe Yerusalemu. Amadziŵitsa Yakobe mawu ake, Amaphunzitsa Israele malamulo ake ndi malangizo ake. Sadachitepo zimenezi ndi mtundu wina uliwonse wa anthu, Iwo sadziŵa malangizo ake. Tamanda Chauta, iwe Yerusalemu. Aleluya: (Marko 10: 45) Mwana wa Munthu adabwera, osati kuti ena adzamtumikire ayi, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu, ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MARKO 10:32-45 Pamene iwo adali pa ulendo wopita ku Yerusalemu, Yesu adali kuyenda patsogolo pa ophunzira ake. Ophunzirawo adali odabwa kwambiri. Ndipo anthu amene adali kuwatsatira adali ndi mantha. Yesu adawaitanira pambali ophunzira khumi ndi awiri aja, nayamba kuwafotokozera zimene zidali kudzamuonekera. Adati: “Tili pa ulendo wopita ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akaperekedwa kwa Akulu a Ansembe ndi Aphunzitsi a Malamulo. Akamuweruza kuti ayenera kuphedwa, ndipo akampereka m’manja mwa anthu a kunja. Iwowo akamseka, akamthira malovu, akamkwapula ndi kumupha. Koma patapita masiku atatu, adzauka.” Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeyo, adadzauza Yesu kuti: “Aphunzitsi, ife tifuna kuti chiri chonse chimene tingakupempheni, mutichitire. Yesu adawafunsa kuti: “Chimene mukufuna kuti ndikuchitireni ndi chiyani?” Iwo adati: “Mulole kuti, pamene mudzakhale mu ulemerero wanu, ife tidzakhale nanu limodzi, wina ku dzanja lamanja, wina kudzanja lamanzere.” Koma Yesu adati: “Simulikudziwa chimene muli kupemphachi. Kodi inu mungathe kumwera nawo chikho chimene ndidzamwere Ine? Kodi mungathe kulandira nawo Ubatizo umene nditi ndidzaulandire Ine?” Iwo adamuyakha kuti: “Inde, tingathe.” Apo Yesu adati: “Chabwino, chikho chimene ndidzamwere Ine, inu mudzamwera nawo. Ndipo Ubatizo umene ndidzalandire Ine, inunso mudzalandira nawo. Koma Ine ndilibe mphamvu zosankhira munthu kuti akhale ku dzanja lamanja kapena lamanzere. Mulungu ndiye adzapereke malo amenewa kwa omwe Iye Mwini adawakonzera.” Pamene ophunzira ena aja adamva zimenezi, adapsera mtima Yakobe ndi Yohane. Koma Yesu adaitana ophunzira ake aja nawauza kuti: “Mukudziwa kuti pakati pa anthu a kunja, anthu amene amati ngolamula, amamveketsadi ulamuliro wawo pa anthu awo. Ndipo akuluakulu awo amaonetsadi mphamvu zawo pa anthu awo. Koma pakati panu zisamatero ayi. Aliyense wofuna kukhala wamkulu mwa inu, akhale mtumiki wanu. Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri, akhale kapolo wa onse. Pakuti ngakhale Mwana wa Munthu yemwe sadabwere kuti ena adzamutumikire ayi. Koma adabwera kuti adzatumikire anthu, ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ambiri.” Mthenga wa Ambuye