LACHITATU LAMULUNGU WA 9 PACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Rev. Deacon Justin Malewezi Jnr for 3 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Rev. Deacon Justin Malewezi Jnr·3 June 2026·14:12·1 view
Ordinary Time
2 AMAKABEO 7:1-2, 9-14 SALIMO 124:2-3, 4-5, 7b-8 MATEYU 5:1-12

Mau a Mulungu a Lero

3 JUNE, 2026 LACHITATU LAMULUNGU WA 9 PACHAKA KULEMEKEZA CHARLES LWANGA NDI AMALITIRI ONSE A KU UGANDA MAINA AWO NAWA: 1. St Achilleus Kiwanuka (Achileo Kiwanuka or Achilles Kiwanuka) 2. St Adolphus Ludigo-Mukasa (Adolofu Mukasa Ludigo) 3. St Ambrosius Kibuuka (Ambrosio Kibuuka) 4. St Anatole Kiriggwajjo (Anatoli Kiriggwajjo) 5. St Andrew Kaggwa 6. St Antanansio Bazzekuketta (Anthanasius Bazzekuketta) 7. St Bruno Sserunkuuma 8. St Charles Lwanga (Karoli Lwanga) 9. St Denis Ssebuggwawo Wasswa (Dionysius Ssebuggwawo) 10. St Gonzaga Gonza 11. St Gyavira Musoke 12. St James Buuzaabalyaawo 13. St John Maria Muzeeyi (John Mary Kiwanuka Muzeeyi or Jean Marie Muzeyi) 14. St Joseph Mukasa (Yosefu Mukasa Balikuddembe) 15. St Kizito 16. St Lukka Baanabakintu (Luke Baanabakintu) 17. St Matiya Mulumba (Matthias Mulumba Kalemba) 18. St Mbaga Tuzinde 19. St Mugagga Lubowa 20. St Mukasa Kiriwawanvu 21. St Nowa Mawaggali (Noah Mawaggali) 22. St Ponsiano Ngondwe (Pontian Ngondwe) MAU OYAMBA: MAU A MMBUKU LA 2 AMAKABEO 7:1-2, 9-14 Adagwiranso abale asanu ndi aŵiri pamodzi ndi amai ao. Mfumu idaafuna kuŵaumiriza, pakuŵazunza ndi zikoti ndi zingwe zokwapulira, kuti adye nyama yankhumba, imene Malamulo ankaletsa. Mmodzi mwa iwowo adalankhula m'malo mwa onse, adati, “Kodi mukuyembekeza kumva chiyani pakutifunsafunsa? Ifetu tili okonzeka kufa, koma zophwanya malamulo a makolo athu ai.” Ali pafupi kufa, iye adati, “Iwe woipawe, ukutilanda moyo uno, koma Mfumu ya zolengedwa zonse idzatiwukitsa kuti itipatse moyo wosatha, ife amene tikuphedwa chifukwa chomvera Malamulo ake.” Pambuyo pake adazunza wachitatu. Ozunzawo atamulamula, pompo iye adapereka lilime lake natambalitsa manja ake mopanda mantha. Adalankhula molimba mtima kuti, “Ndidalandira ziwalozi kwa Mulungu, koma tsopano kwa ine Malamulo ake ndiye chinthu chachikulu koposa ziwalozo. Ndipo ndikukhulupirira kuti Iyeyo adzandibwezera ziwalo zangazo.” Mfumu pamodzi ndi onse amene anali naye pomwepo adadabwa ndi kulimba mtima kwa mnyamatayo, popeza kuti mazunzowo sankaŵayesa kanthu. Atafa iyeyo, adazunza wachinai ndi mazunzo a mtundu womwewo. Ali pafupi kufa iye adati, “Ngodala amene aphedwa ndi anthu, nakhulupirira Mulungu kuti adzaŵaukitsa. Koma iwe Antioko, kuuka kopatsa moyo sudzakuwona ai.” Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 124:2-3, 4-5, 7b-8 Taonjoka ngati mbalame mu msampha wa osaka, msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka Chauta akadapanda kukhala pa mbali yathu, pamene anthu adatiwukira, bwenzi atatimeza amoyo, muja mkwiyo wao udatiyakira, bwenzi chigumula chitatisesa, Taonjoka ngati mbalame mu msampha wa osaka, msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka madzi amkokomo atatikokolola, bwenzi madzi amphamvu atatimiza. Atamandike Chauta, amene sadatipereke kwa anthuwo kuti atiwononge. Taonjoka ngati mbalame mu msampha wa osaka, msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka Taonjoka ngati mbalame mu msampha wa osaka, msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka. Chithandizo chathu chimachokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi Aleluya: Ngodala osauka mu Mtima,pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU 5:1-12 Yesu poona chikhamu cha anthu, adakwera pa phiri. Iye atakakhala pansi, ophunzira ake adamtsatira pomwepo. Kenaka adayamba kuŵaphunzitsa, adati: “Ngodala anthu amene ali osauka mu mtima mwawo, pakuti Ufumu wa Kumwamba ndi wawo. Ngodala anthu amene akumva chisoni, pakuti Mulungu adzaŵasangalatsa. Ngodala anthu ofatsa, pakuti Mulungu adzaŵapatsa dziko la pansi pano kuti likhale lawo. Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzawakhutitsa. Ngodala anthu ochitira anzawo chifundo, pakuti iwonso Mulungu adzaŵachitira chifundo. Ngodala anthu oyera mtima, pakuti adzaona Mulungu. Ngodala anthu odzetsa mtendere, pakuti Mulungu adzaŵatcha ana ake. Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wa Kumwamba ndi wawo. Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa za mitundumitundu chifukwa cha Ine. Mthenga wa Ambuye