LACHIWIRI LA MULUNGU WA 11 PACHAKA
Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Charles Duncan for 16 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
16 JUNE, 2026 LACHIWIRI LA MULUNGU WA 11 PACHAKA MAU WOYAMBA A MBUKU LOYAMBA LA MAFUMU 21:17-29 Chauta adauza Eliya wa ku Tisibe kuti: ”Nyamuka, pita ukakumane ndi Ahabu, Mfumu ya ku Israele, amene akukhala ku Samariya. Iyeyu ali ku munda wa mpesa wa Naboti. Wapita kumeneko kuti akatenge mundawo kuti ukhale wake. Tsono ukamuuze kuti: Chauta akukufunsa kuti: ‘Kodi wapha, ndipo walandanso?’ Ukamuuzenso kuti: ‘Chauta akunena kuti: pa malo amene agalu ankanyambita magazi a Naboti, pomweponso agalu adzanyambita magazi ako.’” Apo Ahabu adafunsa Eliya kuti: “Kani wandipeza, iwe mdani wanga?” Eliya adayankha kuti: “Inde, ndakupezani, chifukwa inuyo mwadzigulitsa ndi kukhala ngati kapolo wa zoipa zochimwira Chauta. Tsopano Chauta akuti:‘Ndithu, ndidzakupasula. Ndidzakusesa kwathunthu, ndidzaononga mwamuna aliyense pa banja lako, kapolo kapena mfulu, m’dziko la Israele. Ndipo banja lako ndidzalisandutsa kuti likhale ngati banja la Yerobowamu, mwana wa Nebati, ndiponso ngati banja la Baasa mwana wa Ahiya. Nawenso wandikwiyitsa, chifukwa chakuti wachimwitsa anthu aku Israele.’ Tsono kunena za Yezebele, Chauta akuti agalu adzamudya Yezebele mkati mwa malinga a Yezirele. Munthu aliyense wa banja la Ahabu, amene adzafere mu mzinda, agalu adzamudya. Ndipo aliyense wa banja limenelo wodzafera ku thengo, mbalame za mlengalenga ndizo zidzamudye.”Kunena zoona, kudalibe ndi mmodzi yemwe amene adadzipereka ku zoipa kuchimwira Chauta ngati Ahabu, amene Yezebele, mkazi wake, adamukopa. Iyeyo adachita zonyansa kwambiri popembedza mafano, monga m’mene ankachitira Aamori aja, amene Chauta adaŵachotsa pamene Aisraele ankafika. Ahabu atamva mawu amenewo, adang’amba zovala zake, navala ziguduli. Adasala zakudya nagona pa zigudulizo, ndipo adayamba kuyenda modzichepetsa. Apo Chauta adauza Eliya wa ku Tisibe kuti: “Kodi waona m’mene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga? Popeza kuti wadzichepetsa pamaso panga, sindidzamlanga ndi zonse zija iyeyo ali moyo. Koma ndidzalanga banja lake, kuyambira mwana wake.” Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 51: 3-4, 5-6AB, 11, 16 Mundichitire chisoni, Inu Chauta, poti ndakuchimwirani (3a). Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, Malinga ndi chikondi chanu chosasinthika. Mufafanize machimo anga, Malinga ndi chifundo chanu chachikulu. Mundichitire chisoni, Inu Chauta, poti ndakuchimwirani. Mundisambitse kwathunthu Pochotsa kulakwa kwanga, Mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga. Mundichitire chisoni, Inu Chauta, poti ndakuchimwirani. Zolakwa zanga ndikuzidziŵa, Kuchimwa kwanga ndikukuzindikira nthaŵi zonse. Ndachimwira Inu, Inu nokha, Ndachita choipa pamaso panu. *Mundichitire chisoni, Inu Chauta, poti ndakuchimwiran*i. Musayang’ane konse machimo anga, Mufafanize zoipa zanga zonse. Mundikhululukire mlandu wanga wokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu Mpulumutsi wanga, Ndipo ndidzakweza mawu poimba za chipulumutso chanu. Ambuye, tsekulani milomo yanga, Ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu. Mundichitire chisoni, Inu Chauta, poti ndakuchimwirani. Aleluya: (Yohane 13: 34) Ndakupatsani lamulo latsopano: mukondane monga momwe Ine ndidakukonderani, akutero Ambuye, Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU WOYERA 5:43-48 Yesu adati kwa ophunzira ake: “Mudamva kuti anthu akale aja adaŵalamula kuti: ‘Ukonde mnzako, ndi kudana ndi mdani wako.’ Koma Ine ndikukuuzani kuti: muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera onse amene amakuzunzani. Mukatero mudzakhaladi ana a Atate anu amene ali Kumwamba. Paja Iwo amaŵalitsa dzuŵa lawo pa anthu abwino ndi pa anthu oipa omwe, ndipo amagwetsera mvula anthu olungama ndi osalungama omwe. Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mungalandire mphotho yanji? Kodi suja ngakhale okhometsa msonkho amachita chimodzimodzi? Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okha, mwachitapo chiyani pamenepo choposa ena? Kodi suja ngakhale akunja amachita chimodzimodzi? Nchifukwa chake monga Atate anu a Kumwamba ali oyera kotheratu, inunso mukhale oyera kotheratu.” Mthenga wa Ambuye