LACHIWIRI LA MULUNGU WA 12 PACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Steven Limbani Kassim for 23 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Steven Limbani Kassim·23 June 2026·20:10·1 view
Ordinary Time
BUKU LACHIWIRI LA MAFUMU 19:9B-11,14-21,31-35A,36 SALIMO 48: 2-3AB, 3CD-4, 10-11 MATEYU WOYERA 7:6,12-14

Mau a Mulungu a Lero

23 JUNE, 2026 LACHIWIRI LA MULUNGU WA 12 PACHAKA MAU WOYAMBA A MBUKU LACHIWIRI LA MAFUMU 19:9B-11,14-21,31-35A,36 ‭‬ Tsono pamene mfumu ya ku Asiriya idamva kuti Mfumu Tirihaka, wa ku Etiyopiya, akubwera kudzachita nayo nkhondo, idatumanso amithenga kwa Hezekiya ndi mawu onena kuti: ”Mulungu wako amene ukumkhulupirirayo asakunamize pokulonjeza kuti Yerusalemu sadzagwa m’manja mwa ine, mfumu ya ku Asiriya. Wakhala ulikumva zimene mafumu aku Asiriya adaŵachita maiko onse, kuti adaŵaononga kotheratu. Tsono iweyo ndiye nkupulumuka? Mfumu Hezekiya adalandira kalata kwa amithenga aja, naiŵerenga. Pomwepo adapita ku Nyumba ya Chauta naika kalatayo m’menemo pamaso pa Chauta. Tsono adapemphera kwa Chauta kuti: “Inu Chauta, Mulungu wa Israele, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu, pamwamba pa Akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira mafumu onse a dziko lonse lapansi. Mudalenga dziko la Kumwamba ndi dziko lapansi. Tsono Inu Chauta, tcherani khutu, kuti mumve. Inu Chauta, tsekulani maso, kuti muone. Mumve mawu onse amene Senakeribu adalankhula, onyoza Inu, Mulungu wamoyo. Inu Chauta, zoonadi mafumu aku Asiriya adaononga anthu a mitundu ina yonse, nasandutsa maiko awo chipululu. Adatentha milungu yawo imene siidali milungu konse, koma mafano a mitengo ndi a miyala opangidwa ndi anthu, nchifukwa chake adaiwononga. Ndiye Inu Chauta, Mulungu wathu, ndikukupemphani kuti mutipulumutse kwa munthu ameneyu, kuti mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziŵe kuti Inu nokha, Chauta, ndiye Mulungu.”Tsono Yesaya, mwana wa Amozi, adatumiza kwa Mfumu Hezekiya mawu omuuza kuti: “Chauta, Mulungu wa Israele, wamva pemphero lako lija lonena za Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya. Poitsutsa mfumuyo, Chauta adati: “Mzinda wa Ziyoni ukukunyoza ndi kukuseka, iwe Senakeribu. Mzinda wa Yerusalemu ukupukusa mutu kumbuyo kwako monyodola.” Poitsutsa mfumuyo, Chauta adati: “Ku Yerusalemu kudzafumira anthu otsala, ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka. Changu cha Chauta chidzachitadi zimenezi. Zimene akunena Chauta za mfumu ya ku Asiriya ndi izi, akuti: ‘Sadzaloŵa mu mzinda umenewu, sadzaponyamo muvi ndi umodzi womwe. Ankhondo ake a zishango sadzafika pafupi ndi mzinda umenewu, ndipo sadzauzinga ndi mtumbira wa nkhondo. Adzabwerera potsata njira yomwe adadzera pobwera, ndipo sadzaloŵa mu mzinda umenewu. Ine Chauta ndatero. Ine ndidzautchinjiriza ndi kuuteteza mzinda umenewu chifukwa cha ulemerero wanga, ndiponso chifukwa cha chipangano changa chimene ndidachita ndi Davide, mtumiki wanga.’“ Ndiye usiku umenewo, mnjelo wa Chauta adapita ku zithando za nkhondo za a Asiriya naphako asirikali 185,000. Tsono Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, adachoka ndi kubwerera kwawo, nakakhala ku Ninive. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 48: 2-3AB, 3CD-4, 10-11 Chauta amakhala mu mzinda wake woyera nthawi zonse (9d). Chauta ndi wamkulu, Ndi woyenera kumutamanda kwambiri. Timuyamike mu mzinda wake, pa phiri lake loyera, Mzinda wokongola wa Ziyoni pa phiri la Mulungu, Wopatsa chimwemwe ku dziko lonse lapansi. Chauta amakhala mu mzinda wake woyera nthawi zonse. Mzinda wa Ziyoni umene uli kumpotowu, Ndi mzinda wa Mfumu yathu yaikulu. Mulungu waonetsa kuti ndiye woteteza mzindawo, Pakuti Iye amakhala mkati mwa malinga ake. Chauta amakhala mu mzinda wake woyera nthawi zonse. Tikakhala m’Nyumba mwanu, Inu Mulungu, Timalingalira za chikondi chanu chosasinthika. Inu Mulungu, anthu amakutamandani ponseponse, Monga dzina lanu latchuka pa dziko lonse lapansi. Dzanja lanu lamphamvu limapambana nthaŵi zonse. Chauta amakhala mu mzinda wake woyera nthawi zonse. Aleluya: (Yohane 8: 12) Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse, akutero Ambuye; munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala nako kuŵala kotsogolera anthu ku moyo, Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU WOYERA 7:6,12-14 Yesu adati kwa ophunzira ake: “Musamapatsa agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyera nkhumba ngale za mtengo wapatali, kuopa kuti zingazipondereze, kenaka nkukutembenukirani ndi kukukhadzulani. Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa. Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.” Mthenga wa Ambuye