LACHIWIRI LA MULUNGU WA 9 PACHAKA LACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Rev. Deacon Justin Malewezi Jnr for 2 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Rev. Deacon Justin Malewezi Jnr·2 June 2026·17:04·4 views
Ordinary Time
KALATA YACHIWIRI YA PETRO 3:12-15a,17-18 SALIMO 90: 2, 3-4, 10, 14 NDI 16 MARKO 12:13-17

Mau a Mulungu a Lero

2 JUNE, 2026 LACHIWIRI LA MULUNGU WA 9 PACHAKA LACHAKA MAU OYAMBA; MAU A MKALATA YACHIWIRI YA PETRO 3:12-15a,17-18 Okondedwa, muziyembekeza tsiku la Ambuye, ndi kugwira ntchito zofulumizitsa kudza kwake. Pa tsikulo, za Kumwamba zidzayaka moto ndi kusungunuka, ndipo zinthu zonse nazonso zidzasungunukira m’motomo. Koma potsata lonjezo la Mulungu, tikudikira Kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, m’mene chilungamo chizidzakhalamo. Choncho inu, okondedwa, popeza kuti mukudikira zimenezi, muzichita changu kuti Ambuye adzakupezeni muli opanda banga kapena chilema, ndiponso muli pa mtendere ndi Ambuyewo. Zindikirani kuti Ambuye athu akukulezerani mtima kuti mupulumuke. Paulo, mbale wathu wokondedwa uja, nayenso adakulemberani za zimenezi, ndi nzeru zimene Mulungu adampatsa. Tsono inu, okondedwa, popeza kuti mwazidziŵiratu zimenezi, chenjerani kuti zolakwa za anthu ochimwa zingakusocheretseni, ndipo mungagwedezeke kenaka nkugwa. Koma mukule m’chifundo ndi m’nzeru za Yesu Khristu, Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu. Iye akhale ndi ulemerero tsopano ndi mpaka muyaya. Amen. ‭‭Mau a Ambuye‬‬‬‬ NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 90: 2, 3-4, 10, 14 NDI 16 Ambuye, ndinu kothaŵira kwanga pa mibadwo yonse (1). Mapiri asadabadwe, Ndipo musadalenge dziko lapansi ndi pokhala anthu, Ndinu Mulungu kuyambira muyaya mpaka muyaya. Ambuye, ndinu kothaŵira kwanga pa mibadwo yonse. Inu mumabwezera anthu ku fumbi, Ndipo mumati: “Bwererani, inu ana a anthu.” Pakuti zaka sauzande imodzi pamaso panu Zili ngati dzulo chabe kapena kamphindi chabe ka usiku. Ambuye, ndinu kothaŵira kwanga pa mibadwo yonse. Zaka za moyo wa munthu sizipitirira 70, Ndipo ndi 80 kwa amene ali ndi mphamvu. Koma zaka zonsezo ndi za nkhaŵa ndi mavuto. Zakazo zimatha msanga, ife nkumapita. Ambuye, ndinu kothaŵira kwanga pa mibadwo yonse. Tidzazeni m’maŵa muli monse Ndi chikondi chanu chosasinthika, Kuti tizikondwa ndi kusangalala masiku athu onse. Mulole kuti ntchito zanu zioneke kwa atumiki anu, Mphamvu zanu za ulemerero zioneke kwa ana awo. Ambuye, ndinu kothaŵira kwanga pa mibadwo yonse. Aleluya: (Aefeso 1: 17-18) Mulungu wa Ambuye athu, Yesu Khristu, akupatseni nzeru, ndikuulula Mulungu kwa inu; ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MARKO 12:13-17 Anthu ena a m’gulu la Afarisi, ndi enanso a m’chipani cha Herode, adatumidwa kuti akatape Yesu mkamwa. Atafika, adati: “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti Inu mumanena zoona, ndipo simuopa munthu aliyense. Simuchita tsankho, koma mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona. Nanga tsono, kodi Malamulo a Mulungu amalola kuti tizikhoma msonkho kwa Mfumu ya ku Roma, kapena ayi? Kodi tizikhomadi kapena tisamakhoma?” Koma Yesu podziŵa maganizo awo onyenga, adati: “Bwanji kodi mukundiyesa dala? Tandipatsirani ndalama, titaiwona.” Iwo adampatsadi ndalamayo. Tsono Iye adaŵafunsa kuti: “Kodi nkhopeyi ndi ya yani, ndipo dzinali ndi la yani?” Iwo aja adati: “Zonse ndi za Mfumu ya ku Roma.” Apo Yesu adaŵauza kuti: “Tsono perekani kwa Mfumu zake za Mfumuyo, ndiponso kwa Mulungu zake za Mulunguyo.” Atamva zimenezi, anthuwo adathedwa nzeru. Mthenga wa Ambuye