LACHIWIRI LAMULUNGU WA 10 PACHAKA (II)

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Gift Phiri, OFM for 9 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Gift Phiri, OFM·9 June 2026·13:04·2 views
Ordinary Time
BUKU LOYAMBA LA MAFUMU 17:7-16 SALIMO 4: 2-3, 4-5, 7B-8 MATEYU 5:13-16

Mau a Mulungu a Lero

9 JUNE, 2026 LACHIWIRI LAMULUNGU WA 10 PACHAKA (II) ‭‭‬‬‬‬‬ MAU OYAMBA, MAU A MBUKU LOYAMBA LA MAFUMU 17:7-16 Patangopita kanthaŵi, mtsinje umene Eliya adali kumwako udaphwa, poti kudalibe mvula m’dzikomo. Tsono Chauta adauza Eliya kuti: “Nyamuka upite ku Zarefati, mudzi wa ku Sidoni, ndipo ukakhale kumeneko. Ndalamula mayi wamasiye wa kumeneko kuti azikakudyetsa.” Choncho Eliya adanyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, adangoona mayi wamasiye akutola nkhuni. Tsono adaitana mayiyo namuuza kuti: “Patseniko madzi pang’ono, ndimwe.” Pamene mayi uja ankapita kukatunga madziwo, Eliya adamuitananso namuuza kuti: “Munditengerekonso kabuledi.” Apo mayiyo adati: “Pali Chauta, Mulungu wanu, ine sindidaphike kanthu kalikonse, koma ndili ndi ufa pang’ono m’mbiya, ndi mafuta pang’ono m’nsupa. Tsono ndikutola nkhuni zoti ndikaphikire kaufako, kuti ndikadye ine ndi mwana wanga, kenaka kufa kukhala komweko.” Koma Eliya adauza mayiyo kuti: “Musade nkhaŵa. Pitani, mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mutapeko kaufa pang’ono, mundiphikire kakeke, mubwere nako kuno. Pambuyo pake, mukaphikenso kuti mudye inuyo ndi mwana wanu. Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti: ‘Ufa umene uli m’mbiyawo sudzatha, mafutanso amene ali m’nsupawo sadzatha, mpaka tsiku limene Chauta adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’” Tsono mayiyo adapita, nakachitadi monga momwe adanenera Eliya. Mayiyo ndi Eliya ndiponso onse a pa banja la mayiyo adadya ufawo masiku ambiri. Ufa umene udali m’mbiyamo sudathe, mafuta amene adali m’nsupawo sadathenso, monga momwe Chauta adalankhulira kudzera mwa Eliya. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 4: 2-3, 4-5, 7B-8 Ambuye, nkhope yanu iwalire pa ife anthu anu (7a). Pamene ndilirira kwa Inu, mundiyankhe, Ambuye, Mundisangalatse pamene ndili m’mavuto; Mundimvere chisoni ndi kumva pemphero langa! Inu anthu otchuka, mpaka liti mudzagona tulo? Nchifukwa chiyani mudzakonda zopanda pake? Ambuye, nkhope yanu iwalire pa ife anthu anu. Dziwani kuti Chauta amachita zodabwitsa kwa anthu ake, Amamvetseranso onse amene amampemphera. Munjenjemere ndi kusiya tchimo; Pamene mugona pabedi, lingalirani za Iye. Ambuye, nkhope yanu iwalire pa ife anthu anu. Ambuye, tikufuna kuti nkhope yanu iwalire pa ife! Ndipo mubwezere chisangalalo mu mtima mwanga, Choposa chakudya ndi vinyo. Ambuye, nkhope yanu iwalire pa ife anthu anu. Aleluya: (Mateyo 5: 16) Ambuye, kuwala kwanu kuwalire anthu onse kuti aone ntchito zanu zamphamvu, ndi kutamanda Atate anu a Kumwamba, Aleluya. MTHENGA WA AMBUYE MONGA ADALEMBERA MATEYU 5:13-16 Yesu adati: “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Ulibenso ntchito mpang’ono pomwe, koma kungoutaya kunja basi, anthu nkumauponda. Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m’nyumbamo. Chomwechonso, inuyo muzionetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino, azilemekeza Atate anu a Kumwamba. Mthenga wa Ambuye