LACHIWIRI LAMULUNGU WA 19 PACHAKA

Fr. Joseph Kimu·11 August 2026
Ordinary Time
EZEKIELI 2:8-3:4 SALIMO 119: 14, 24, 72, 103, 111, 131 MATEYU 18:1-5,10,12-14

Chichewa Transcript

11 AUGUST, 2026 LACHIWIRI LAMULUNGU WA 19 PACHAKA (II) MAU OYAMBA; MAU A MBUKU LA MNENERI EZEKIELI 2:8-3:4 ‭‭‬‬ Chauta adati kwa ine: “Koma tsono iwe, mwana wa munthu, umvere bwino zimene ndikukuuza. Usakhale waupandu ngati iwowo. Tsopano yasama, udye chimene ndikupatse.” Ine poyang’ana, ndidaona dzanja litaloza ine, litagwira mpukutu wolembedwa. Adaufunyulula nandionetsa. Mpukutu wonsewo udali wolembedwa kuseli nkuseri. Mawu amene adalembedwa m’menemo adali a za madandaulo, za maliro ndi za matemberero. Pamenepo Mulungu adandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, idya chimene ndikukupatsachi. Idya mpukutuwu ndipo pita ukalankhule ndi Aisraele.” Motero ine ndidayasama, ndipo adandipatsa mpukutu kuti ndidye. Tsono adandiuza kuti: “Iwe, mwana wa munthu, idya mpukutu ndikukupatsawu, ukhute.” Choncho ndidadya, ndipo unkatsekemera ngati uchi. Kenaka adandiuza kuti: “Iwe, mwana wa munthu, pita kwa Aisraele, ukaŵauze mawu anga.” ‭‭Mau a Ambuye‬‬‬‬‬‬‬‬‬‬‬‬ NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 119: 14, 24, 72, 103, 111, 131 Inu Chauta, mawu anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa (103a). Kuyenda m’njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, Kupambana kukhala ndi chuma chiri chonse. Inu Chauta, mawu anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Malamulo anu amandikondwetsa, Ndiwo amene amandilangiza. Inu Chauta, mawu anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Malamulo a pakamwa panu amandikomera Kuposa ndalama masauzande ambiri a golide ndi a siliva. Inu Chauta, mawu anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Mawu anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Amatsekemera kuposa uchi mkamwa mwanga. Inu Chauta, mawu anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, Zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga. Inu Chauta, mawu anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Ndimapuma mwaŵefuŵefu nditatsekula pakamwa, Chifukwa ndimalakalaka malamulo anu. Inu Chauta, mawu anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Aleluya: (Mateyo 11: 29ab) Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti Ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa: mukatero mudzapeza mpumulo m’mitima mwanu, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYU 18:1-5,10,12-14 Ophunzira adafunsa Yesu kuti: “Kodi mu Ufumu wa Kumwamba, wamkulu koposa onse ndani?” Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pawo, ndipo adati: “Ndithu ndikunenetsa kuti, mukapanda kusintha ndi kusanduka ngati ana, simudzaloŵa konse mu Ufumu wa Kumwamba. Nchifukwa chake munthu wodzichepetsa, ngati mwana uyu, ameneyo ndiye wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba. Ndipo aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene. Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti anjelo awo Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga, amene ali Kumwambako nthaŵi zonse. Tsono mukuganiza bwanji? Munthu atakhala ndi nkhosa 100, imodzi nkutayikapo, kodi sangasiye 99 zina zija m’phiri, nkukafunafuna imodzi yotayikayo? Ndithu ndikunenetsa kuti ataipeza, chimwemwe chake, chokondwerera imeneyo, chimapambana chokondwerera zina zija zimene sizidatayike. Chonchonso Atate anu, amene ali Kumwamba, safuna kuti ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa atayike.” Mthenga wa Ambuye