LACHIWIRI LAMULUNGU WA 30 PACHAKA (II)
Watch this Catholic homily in Chichewa by Deacon Anthony Kavinya for 27 October 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
27 OCTOBER, 2026 LACHIWIRI LAMULUNGU WA 30 PACHAKA (II) MAU OYAMBA; MAU A MKALATA YA PAULO YOLEMBERA AEFESO 5:21-33 Okondedwa, inu amene mumaopa Khristu, muzimverana. Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga mumamvera Ambuye. Paja mwamuna ndi mutu wa mkazi wake, monga momwe Khristu ali mutu wa Mpingo, umene uli thupi lake, ndipo Iye Mwini ndi Mpulumutsi wa Mpingowo. Tsono monga Mpingo umamvera Khristu, momwemonso akazi azimvera amuna awo pa zonse. Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo. Adachita zimenezi kuti aupatule ukhale wakewake, atauyeretsa pakuutsuka ndi madzi ndiponso ndi mawu ake. Adafuna kuti akauimike pamaso pake uli wa ulemerero, wopanda banga kapena makwinya, kapena kanthu kena kalikonse kouipitsa, koma uli woyera ndi wangwiro kotheratu. Momwemonso amuna azikonda akazi awo, monga momwe eni akewo amakondera matupi awo. Amene amakonda mkazi wake, ndiye kuti amadzikonda iye yemwe. Palibiretu munthu amene amadana ndi thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamala bwino, monga momwe Khristu amachitira Mpingo wake. Amatero chifukwa Mpingowo ndi thupi lake, ndipo ife ndife ziwalo za thupi lake. Paja mawu a Mulungu akuti: “Nchifukwa chake mwamuna adzasiye atate ndi amayi ake, nakaphatikizane ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo asanduke thupi limodzi.” Mawu ameneŵa akutiwululira chinsinsi chozama, ndipo ndikuti chinsinsicho nchokhudza Khristu ndi Mpingo. Komabe akunenanso za inu, kuti mwamuna aliyense azikonda mkazi wake monga momwe amadzikondera iye mwini, ndiponso kuti mkazi aliyense azilemekeza mwamuna wake. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 128: 1-2, 3, 4-5 Ngodala munthu aliyense amene amaopa Chauta (1a). Ngodala aliyense woopa Chauta, Amene amayenda m’njira zake. Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino. Ngodala munthu aliyense amene amaopa Chauta. Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka, Mkati mwa nyumba yako. Ana ako adzakhala ngati tiziphukira ta olivi, Pozungulira tebulo lako lodyera. Ngodala munthu aliyense amene amaopa Chauta. Zoonadi, ndimo m’mene adzakhalire wodala munthu woopa Chauta. Chauta amene amakhala ku Ziyoni akudalitse. Uwone m’mene Yerusalemu zinthu zidzamuyendere bwino Masiku onse a moyo wako. Ngodala munthu aliyense amene amaopa Chauta. Aleluya: (Mateyo 11: 25) Atate, Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti mudaululira ana akhanda zinthuzi, zimene mudabisira anthu anzeru ndi ophunzira, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA 13:18-21 Yesu adati: “Kodi Ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani, ndipo ndingauyerekeze ndi chiyani? Uli ngati njere ya mbewu ya mpiru imene munthu adakaifesa m’munda mwake. Idamera nisanduka mtengo, mbalame za mlengalenga nkumabwera kudzamanga zisa pa nthambi zake.” Yesu adatinso: “Ndingayerekezenso ndi chiyani Ufumu wa Mulungu? Ulinso ngati chofufumitsira buledi, chimene mayi wina adachisakaniza ndi ufa wokwanira miyeso itatu, mpaka mtanda wonse udafufuma.” Mthenga wa Ambuye