LACHIWIRI LAMULUNGU WA PACHAKA (II) - Kulemekeza Filipi Neri Woyera, Wansembe -
Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Maxwell Kubalasa for 26 May 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
26 MAY, 2026 Kulemekeza Filipi Neri Woyera, Wansembe LACHIWIRI LAMULUNGU WA PACHAKA (II) MAU OYAMBA, MAU A MKALATA YA PETRO 1:10-16 Abale, aneneri amene adaneneratu za madalitso amene mudzawalandirewo, adafunafuna nafufuzafufuza za chipulumutsochi. Mzimu wa Khristu, wokhala mwa iwo, adali kuneneratu za zowawa zimene Khristu adzamve, ndiponso za ulemerero umene adzakhale nawo pambuyo pake. Aneneriwo adafunafuna kudziwa kuti: “Kodi izi zidzachita liti, ndiponso mwa njira yanji?” Mzimu Woyera adawaululira kuti ntchito yawoyi sadali kuigwira chifukwa cha iwo eni, koma chifukwa cha Inu. Pamene iwo adali kunena za zooonazi, zimene mwamva tsopano, olalika Uthenga Wabwino adakuuzani zoonazi, mwa mphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera Kumwamba. Anjelo nawo amalakalaka kuona zinthuzi. Nchifukwa chake mtima wanu ukhale wokonzeka. Khalani odziletsa. Khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa madalitso amene mudzawalandire, pamene Yesu Khristu adzaonekera. Mudzikhala ngati ana omvera, osatsatanso zimene mukulakalaka pamene mudali osadziwa. Koma monga momwe Iye, amene adakuitanani, ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima mu zochita zanu zonse. Pakuti paja mawu a Mulungu akuti: “Mudzikhala oyera mtima popeza kuti Ine ndine Woyera mtima.” Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 98: 1, 2-3AB, 3CD-4 Chauta waulula chipulumutso chake kwa anthu onse (2a). Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, Popeza kuti wachita zodabwitsa. Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa. Chauta waulula chipulumutso chake kwa anthu onse. Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo, Waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse Kuti Iye ndi wolungama. Wakumbukira chikondi chake chosasinthika Ndi kukhulupirika kwake pa fuko la Israele. Chauta waulula chipulumutso chake kwa anthu onse. Anthu aku mathero a dziko lonse lapansi Aona chipulumutso cha Mulungu wathu. Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, Inu dziko lonse lapansi. Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda. Chauta waulula chipulumutso chake kwa anthu onse. Aleluya: (Mateyo 11: 25) Atate, Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti mudaululira ana akhanda zinthuzi, zimene mudabisira anthu a nzeru ndi ophunzira, Aleluya. MTHENGA WA AMBUYE MONGA ADALEMBERA MARKO 10:28-31 Petro adayamba kulankhula ndi Yesu nati: “Ifetu paja tidasiya zonse kuti tikutsateni.” Yesu adati: “Zoonadi, ndikukuuzani kuti aliyense amene adachoka kwawo, nasiya abale, alongo, amayi ndi atate, ana, kapena minda, chifukwa cha Ine, ndiponso chifukwa cha Uthenga Wabwino, adzalandiranso zambirimbiri pansi pano. Adzalandiranso nyumba zambirimbiri, abale ambirimbiri, alongo ambirimbiri, amayi ambirimbiri, minda yambirimbiri, komanso mazunzo. Ndipo kutsogoloko, adzalandira moyo wosatha. Koma ambiri amene ali oyambirira adzakhala otsiriza, ndipo amene ali otsiriza adzakhala oyambirira.” Mthenga wa Ambuye