LAMULUNGU LA 11 PACHAKA
Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Gift Phiri, OFM for 14 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
14 JUNE 2026 LAMULUNGU LA 11 PACHAKA KUTUMIDWA KWA OPHUNZIRA A YESU MAU OYAMBA A MBUKU LA EKSODO (KUTULUKA) 19:2-6a Atachoka ku Refidimu adakafika ku chipululu cha Sinai, kumene adamangako mahema pafupi ndi phirilo. Mose adakwera phiri kukakumana ndi Mulungu, ndipo Mulungu adamuitana m'phirimo namuuza kuti, “Uuze zidzukulu za Yakobe, ndiye kuti mtundu wonse wa Aisraele kuti, ‘Mudaona zimene ndidaŵachita Aejipito, ndiponso muja ndidakunyamulani monga m'mene mphungu imanyamulira ana ake pa mapiko ake, ndipo ndidakufikitsani kwa Ine. Tsono mukamandimvera ndi kusunga chipangano changa, mudzakhala anthu anga pakati pa makamu onse, pakuti dziko lonse lapansi ndi langa. Ndipo inu mudzakhala anthu onditumikira Ine ngati ansembe, ndiponso ngati mtundu woyera. Tsono ukaŵauze mau ameneŵa Aisraele.’ Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 100:1-2,3,5 Ndife Anthu ake ndi nkhosa za busa lake Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse. Tumikirani Chauta mosangalala. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa Ndife Anthu ake ndi nkhosa za busa lake Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake. Ndife Anthu ake ndi nkhosa za busa lake Paja Iye ndi wabwino. Chikondi chake nchamuyaya, kukhulupirika kwake nkosatha Ndife Anthu ake ndi nkhosa za busa lake MAU ACHIWIRI A MKALATA YA PAULO KWA A ROMA 5:6-11 Pa nthaŵi imene Mulungu adaikonzeratu, pamene ife tikusoŵabe pogwira, Khristu adatifera anthu ochimwafe. Nchapatali kuti munthu afere munthu wina, ngakhale winayo akhale wolungama. Kaya kapena mwina munthu nkulimba mtima mpaka kufera munthu wabwino. Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera. Ndiye popeza kuti tsopano chifukwa cha magazi ake tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa pamenepo ku mkwiyo wa Mulungu. Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni. Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano. Mau a Ambuye Aleluya: Pitani, Kalalikeni kuti ‘Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU 9:36-10:8 Pamene adaona makamu a anthu, adaŵamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa. Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.” Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵapatsa mphamvu pa mizimu yoipitsa anthu, kuti aziitulutsa mwa anthuwo, ndiponso mphamvu zochiritsira nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi. Atumwi khumi ndi aŵiriwo maina ao ndi aŵa: Woyamba ndi Simoni, wotchedwa Petro, ndipo mbale wake Andrea; Yakobe, mwana wa Zebedeo, ndi mbale wake Yohane; Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; Simoni, wa m'chipani chandale cha Azelote; ndiponso Yudasi Iskariote, amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake. Anthu khumi ndi aŵiri ameneŵa Yesu adaŵatuma ndi malamulo akuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kukaloŵa m'mudzi uliwonse wa Asamariya ai. Koma makamaka mupite kwa Aisraele amene ali ngati nkhosa zotayika. Pitani, muzikalalika kuti, ‘Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake tsopano.’ Muzikachiritsa odwala, muzikaukitsa akufa, muzikachotsa khate, muzikatulutsa mizimu yoipa. Mwalandira mwaulere, kaperekeni mwaulere. Mthenga wa Ambuye