LAMULUNGU LA 12 PACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Charles Duncan for 21 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Charles Duncan·21 June 2026·16:22·9 views
Ordinary Time
YEREMIYA 20:10-13 SALIMO 67: 7-9,13 ndi 16,32-34 AROMA 5:12-15 MATEYU 10:26-33

Mau a Mulungu a Lero

21 JUNE 2026 LAMULUNGU LA 12 PACHAKA Chauta amathandiza Omukhulupilira MAWU A MBUKU LA MNENERI YEREMIYA 20:10-13 Ndimamva ambiri akunong'ona. Zoopsa zili pa mbali zonse! Amati, “Kamnenezeni! Tiyeni tikamneneze!” Amene adaali abwenzi anga amayembekeza kuti ndigwa pansi, amati, “Mwina mwake adzatha kunyengedwa, tsono ife tidzamgwira ndi kulipsira pa iyeyo.” Koma Chauta ali nane, ndiye wankhondo woopsa. Nchifukwa chake anthu ondizunza adzakhumudwa, ndithu sadzandipambana. Adzachita manyazi kwambiri, chifukwa cha kundilepherako, ndipo manyazi aowo sadzaiŵalika konse. Inu Chauta Wamphamvuzonse, amene mumaweruza anthu molungama, amene mumapenya zamumtima, ndikupereka mlandu wanga kwa Inu. Ndikukupemphani kuti mundilipsirire adani anga. Imbirani Chauta, mtamandeni Chauta! Ndiye amapulumutsa osauka kwa adani ao. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 67: 7-9,13 ndi 16,32-34 Mwachifundo channu Mundiyankhe, Inu Mulungu (13c). Kwa abale anga ndasanduka mlendo, kwa ana a mai wanga ndili ngati wakudza. Changu chochitira Nyumba yanu chandiphetsa, chipongwe cha anthu okunyozani chandigwera. Mwachifundo channu Mundiyankhe, Inu Mulungu (13c). Pamene ndidadzilanga posala zakudya, anthu adandinyoza. Pulumutseni kuti ndisamire m'matope, landitseni kwa adani anga ndi ku madzi ozama. Musandibisire ine mtumiki wanu nkhope yanu, fulumirani kundithandiza, pakuti ndili pa zovuta. Mwachifundo channu Mundiyankhe, Inu Mulungu (13c). Paja Chauta amamvera anthu osoŵa, sanyoza anthu ake omangidwa ndi unyolo. Kumwamba ndi pansi pano, nyanja ndi zonse zoyenda m'menemo zitamande Iye. Mulungu adzapulumutsa Ziyoni, ndipo adzamanganso mizinda ya Yuda. Anthu ake adzakhala kumeneko, ndipo lidzakhala dziko lao. Mwachifundo channu Mundiyankhe, Inu Mulungu (13c). MAU ACHIWIRI A MKALATA YA PAULO KWA AROMA 5:12-15 Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa. Uchimo udaalipo pa dziko lapansi Mulungu asanapereke Malamulo. Koma pamene palibe Malamulo, machimo a munthu saŵerengedwa ai. Komabe kuyambira nthaŵi ya Adamu kufikira nthaŵi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira Iye uja amene Mulungu adaati adzabwerayu. Koma sitingafananitse mphatso yaulere ya Mulungu ndi kuchimwa kwa Adamu ai. Pajatu anthu ambiri adafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, koma kukoma mtima kwa Mulungu, ndiponso mphatso yake yaulere, zidaposa ndithu, chifukwa zidabweretsera anthu ambiri madalitso ochuluka. Mphatso imene Mulungu adaperekayo ndiye Munthu mmodzi uja, Yesu Khristu. Mau a Ambuye Aleluya: (Yohane 15:26b-27a), mzimu wa Choona udzandichitira Umboni,akutero Ambuye; Inunso ndinu Mboni Zanga Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU 10:26-33 “Choncho inu musamaopa anthu. Kanthu kalikonse kovundikirika kadzaululuka, ndipo kalikonse kobisika kadzadziŵika. Zimene ndikukuuzirani m'chibisibisi, inu mukazilankhulire poyera, ndipo zimene mukuzimvera m'manong'onong'o, inu mukazilalikire pa madenga. Musamaŵaopa amene amapha thupi, koma mzimu sangathe kuupha. Makamaka muziwopa amene angathe kuwononga thupi ndi mzimu womwe m'Gehena. Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa. Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri. “Aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso ndidzamuvomereza pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba. Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti Ine sandidziŵa, Inenso ndidzamkana pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba kuti sindimdziŵa. Mthenga wa Ambuye