LAMULUNGU LA 30 PACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Medrick Mlava, DP for 25 October 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Medrick Mlava, DP·25 October 2026·14:21
Ordinary Time
MAU OYAMBA : EKSODO 22:21-27 SALIMO 18: 2,47 ndi 51ab MAU A CHIWILI ATESALONIKA 1:5c-10 MTHENGA WABWINO : MATEYU 22:34-40

Mau a Mulungu a Lero

25 OCTOBER, 2026 LAMULUNGU LA 30 PACHAKA MALAMULO ONSE AGONA PA CHIKONDI MAU A MBUKU LA EKSODO 22:21-27 “Musazunze mlendo kapena kumkhalitsa m'phanthi, poti paja inunso munali alendo ku dziko la Ejipito. Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye. Mukamaŵazunza, Ine ndidzaŵamva iwowo akamalira kwa Ine. Ndidzakukwiyirani, ndipo ndidzakuphani ku nkhondo. Akazi anu adzasanduka amasiye, ndipo ana anunso adzasanduka amasiye. “Mukakongoza ndalama munthu wina aliyense waumphaŵi pakati panupo, musamachita monga momwe amachitira anthu okongoza, musamuumirize kupereka chiwongoladzanja. Mukatenga mwinjiro wa munthu wina ngati chigwiriro kuti adzakulipireni, muubweze dzuŵa lisanaloŵe, poti chofunda nchokhacho, ndicho chotetezera thupi lake. Nanga adzafunda chiyani? Akalira kwa Ine iyeyu kuti ndimthandize, ndidzamuyankha chifukwa ndine wachifundo. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 18: 2,47 ndi 51ab Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, mtetezi ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa. Ndimaitana Chauta, amene ayenera kumtamanda, ndipo amandipulumutsa kwa adani anga. Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga Nthambo za imfa zidandizungulira, mitsinje yothamanga yoononga idandisefukira. Mulungu ndiye adandithandiza kuti ndilipsire, adangonjetsa anthu a mitundu ina, kuti akhale mu ulamuliro wanga. Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO KWA ATESALONIKA 1:5c-10 Mukudziŵa m’mene tinkakhalira pakati panu pofuna kuti tikuthandizeni. Inu mwakhala mukutsata chitsanzo chathu ndi cha Ambuye. Ngakhale mudapeza masautso ambiri, mudalandira mau athu mwa hifukwa chochokera kwa Mzimu Woyera. Motero nanunso mudakhala chitsanzo kwa okhulupirira onse a ku Masedoniya ndi a ku Akaiya. Inde kuchokera hifukw mau a Ambuye adakafika ku Masedoniya ndi ku Akaiya, ndipo kuwonjezera apo mbiri yakuti mudakhulupirira Mulungu idawanda ponseponse. Motero palibe chifukwa chakuti ife nkunenapo kanthu. Iwo amakamba okha za m’mene mudatilandirira, ndi za m’mene mudasiyira mafano ndi kutembenukira kwa Mulungu weniweni wamoyo, kuti muzimtumikira. Tsopano mukudikira Mwana wake kuti abwerenso kuchokera Kumwamba. Mwana wakeyo ndi Yesu, amene Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Iyeyo amatipulumutsa ku mkwiyo umene ulikudza. Mau a Ambuye ALELUYA: (Yohane 14:23) Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. ALELUYA. MTHENGA WABWINO WA MATEYU 22:34-40 Afarisi atamva kuti Yesu adatsutsa Asaduki, adasonkhana. Tsono mmodzi mwa iwo, katswiri wa Malamulo, adafunsa Yesu funso kuti amutape m'kamwa. Adati, “Aphunzitsi, kodi mwa malamulo onse a Mulungu, lalikulu ndi liti?” Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu. Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe. Malamulo onse a Mose ndiponso zonse zimene aneneri adaphunzitsa zagona pa malamulo aŵiriŵa.” Mthenga wa Ambuye