LAMULUNGU LA UTATU WOYERA - MUMAKHULUPILIRA MULUNGU WOTANI?
Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Maxwell Kubalasa for 31 May 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
31 MAY, 2026 LAMULUNGU LA UTATU WOYERA MUMAKHULUPILIRA MULUNGU WOTANI? MAU OYAMBA: MAU A MMBUKU LA EKSODO 34:4b-6,8-9 Chauta, Chauta, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima [Motero] kutacha m'maŵa, adakwera phiri la Sinai monga momwe Chauta adamlamulira. Anali atanyamula miyala iŵiri ija. Tsono Chauta adatsika mu mtambo, naimirira pomwe panali iyepo, ndipo adatchula dzina lake loti Chauta. Adayenda pamaso pa Mose nanena mokweza kuti, “Chauta, Chauta, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndiponso wokhulupirika kwa anthu ake. Pamenepo Mose adagwada pansi napembedza. Kenaka adati, “Ngati mwandikomera mtima, Inu Chauta, ndikukupemphani kuti mupite nafe. Anthuŵa ngokanika, koma Inu mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu, ndipo mutilandire ife, kuti tikhale anthu anu.” Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: DANIELE 3:52,53,54,55 ndi 56 Mulandire ulemu ndi chiyamiko mpaka Muyaya “Mutamandike Inu Ambuye, Mulungu wa makolo athu. Ndinu oyenera kukutamandani ndi kukulemekezani mpaka muyaya. Litamandike dzina lanu laulemerero ndi loyera. Ndi loyenera kulitamanda ndi kulilemekeza mpaka muyaya. Mulandire ulemu ndi chiyamiko mpaka Muyaya Mutamandike m'Nyumba yanu yoyera yoonetsa ulemerero wanu. Ndinu oyenera kukutamandani ndi kukulemekezani mpaka muyaya. Mulandire ulemu ndi chiyamiko mpaka Muyaya Mutamandike Inu okwezedwa pamwamba pa Akerubi nkumayang'ana ku mapompho. Ndinu oyenera kukutamandani ndi kukulemekezani mpaka muyaya. Mulandire ulemu ndi chiyamiko mpaka Muyaya Mutamandike pa mpando wanu waufumu. Akuimbireni nyimbo ndi kukulemekezani mpaka muyaya. Mulandire ulemu ndi chiyamiko mpaka Muyaya Mutamandike m'thambo lakumwamba. Akuimbireni nyimbo ndi kukulemekezani mpaka muyaya. Mulandire ulemu ndi chiyamiko mpaka Muyaya Aleluya: Ulemu ukhale kwa Atate ndi Kwa Mwana ndi kwa Mzimu Woyera, kwa Mulungu amene alipo, ndipo alipo ndipo alikudza Aleluya. MAU A CHIWIRI A MKALATA YA CHIWIRI YA PAULO KWA AKORINTO 13:11-13 Chaulele cha Ambuye wathu Yesu Khristu ndi chikondi cha Mulungu ndi chiyanjano cha MzimuWoyera Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu. Mupatsane moni mwa chikondi choona. Anthu onse a Mulungu akukupatsani moni. Mau a Ambuye MTHENGA WABWINO WA YOHANE 3:16-18 [Yesu adati kwa Nikodemo]: Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha. Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzaŵapulumutse. ”Munthu wokhulupirira Mwanayo, sazengedwa mlandu. Koma wosakhulupirira, wazengedwa kale, chifukwa sadakhulupirire Mwana mmodzi yekha uja wa Mulungu. Mthenga wa Ambuye