LOLEMBA LA LAMULUNGU WA 30 PA CHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Deacon Anthony Kavinya for 26 October 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Deacon Anthony Kavinya·26 October 2026·9:43
Ordinary Time
MAU OYAMBA : AEFESO 4:32-5:8 SALIMO 1:1-2.3.4 NDI 6 MTHENGA WABWINO : LUKA 13:10-17

Mau a Mulungu a Lero

26 OCTOBER, 2026 LOLEMBA LA LAMULUNGU WA 30 PA CHAKA MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO 4:32-5:8 Abale, muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso. Tsono popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira. Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu. Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu. Ndiponso musamalankhule zolaula, zopusa, kapena zopanda pake, koma muzilankhula zoyamika Mulungu. Mudziŵe ichi, kuti munthu aliyense wadama, kapena wochita zonyansa, kapena wa masiriro oipa (pakuti wa masiriro oipa ali ngati wopembedza dano) sadzalowa nao mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu. Munthu wina aliyense asakupusitseni ndi mau onyenga, pakuti zinthu zotere ndizo zimadzetsa ukali wa Mulungu pa anthu omupandukira. Nchifukwa chake musamagwirizane nawo anthu otere. Inunso kale mudaali mu mdima, koma tsopano muli m'kuwala, popeza kuti ndinu ao a Ambuye. Tsono muziyenda ngati anthu okhala m'kuwala. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 1:1-2.3.4 NDI 6 Popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira. Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu, koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mitsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino. Anthu oipa sali choncho, ali ngati mungu wouluzika ndi mphepo. Paja Chauta amawasamalira anthu ake, koma anthu ochimwa adzaonongeka Aleluya: Khalani okhulupirika mpaka imfa, ndipo ndidzakupatsani moyo ngati mphotho yanu. Aleluya. MTHENGA WABWINO WA LUKA 13:10-17 Tsiku lina la Sabata Yesu ankaphunzitsa m’nyumba ina ya mapemphero. M’menemo mudali mayi wina amene adali ndi mzimu woipa umene udamudwalitsa zaka 18. Adali ndi msana wokhota, mwakuti sankatha konse kuŵeramuka. Pamene Yesu adamuona, adamuitana namuuza kuti: “Mayi inu, mwamasuka ku matenda anu.” Adamsanjika manja, ndipo pompo mayiyo adaongoka, nayamba kutamanda Mulungu. Koma mkulu wa nyumba ya mapemphero ija adakwiya, poona kuti Yesu wachiritsa munthu pa tsiku la Sabata. Tsono mkuluyo adauza anthu onse kuti: “Pali masiku asanu ndi limodzi antchito. Muzibwera masiku ameneŵa kudzachiritsidwa, osati pa tsiku la Sabata ayi” Koma Ambuye adati: “Anthu achiphamaso inu, kodi suja nonsenu mumamasula ng’ombe zanu kapena abulu anu pa tsiku la Sabata kukaŵamwetsa madzi? Nanga mayiyu, amene ali mwana wa Abrahamu, ndipo Satana adamumanga zaka 18, kodi sikunayenera kuti amasulidwe ku nsinga imeneyi pa tsiku la Sabata?” Yesu atanena zimenezi, adani ake onse adachita manyazi. Koma anthu ena onse adakondwera chifukwa cha ntchito zodabwitsa zimene Iye ankachita. Mthenga wa Ambuye