LOLEMBA LA MULUNGU WA 11 PACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Charles Duncan for 15 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Charles Duncan·15 June 2026·18:48·4 views
Ordinary Time
BUKU LOYAMBA LA MAFUMU 21:1-16 SALIMO 5: 2-3AB, 4B-6A, 6B-7 MATEYU WOYERA 5:38-42

Mau a Mulungu a Lero

15 JUNE, 2026 LOLEMBA LA MULUNGU WA 11 PACHAKA MAU WOYAMBA A MBUKU LOYAMBA LA MAFUMU 21:1-16 ‭‬ Padali munthu wina wa ku Yezirele dzina lake Naboti. Iyeyo adali ndi munda wa mpesa ku Yezirele, pafupi ndi nyumba ya Mfumu Ahabu. Tsiku lina, Ahabu adauza Naboti kuti: “Tandipatsa munda wakowu kuti ukhale dimba langa, poti uli pafupi ndi nyumba yanga. M’malo mwake ndidzakupatsa wina wabwino koposa, kapena ngati ufuna, ndidzakupatsa ndalama pa mtengo wake wa mundawo.” Koma Naboti adauza Ahabu kuti: “Ndithu, pali Chauta, sindingakupatseni choloŵa cha makolo anga.” Apo Ahabu adakaloŵa m’nyumba mwake atakwiya, msunamo uli toloo chifukwa cha zimene Naboti wa ku Yezirele adanena, pakuti adati: “Sindingakupatseni choloŵa cha makolo anga.” Motero Ahabu adakagona pa bedi pake atapenya ku khoma, osafuna ndi kudya komwe.Koma Yezebele, mkazi wake uja, adabwera kwa iye namufunsa kuti: “Chifukwa chiyani nkhope yanu ikuoneka yosakondwa, ndipo simukufuna chakudya?” Ahabu adauza mkazi wakeyo kuti: “Chifukwa chake nchakuti ine ndidakamba ndi Naboti wa ku Yezirele, ndi kumuuza kuti andipatse munda wake wa mpesa uja kuti ndigule, kapena ngati afuna, ndidzamupatse munda wina m’malo mwake. Koma iyeyo wayankha kuti: ‘Sindidzakupatsani munda wanga wa mpesawu.’“Apo Yezebele, mkazi wakeyo, adamufunsa kuti: “Kodi mfumu ya ku Israele sindinu? Dzukani, kadyeni, mtima wanu usangalale. Ine ndidzakutengerani munda wa mpesawo kwa Naboti wa ku Yezirele.” Tsono Yezebele adalemba makalata m’dzina la Ahabu, naŵasindikiza ndi chidindo cha mfumu. Adatumiza makalatawo kwa akuluakulu ndi kwa atsogoleri amene ankakhala ndi Naboti mu mzinda mwake. M’makalatamo adalembamo kuti: “Lalikani kuti anthu asale zakudya, ndipo Naboti amuike pa malo a ulemu. Mupeze anthu aŵiri oipa mtima kuti adzamneneze ndi mawu akuti: ‘Iwe watemberera Mulungu ndiponso mfumu.’ Tsono mumtulutsire kunja, ndipo mumponye miyala kuti afe basi.” Motero anthu amu mzinda m’mene ankakhala Nabotiyo, akuluakulu ndi atsogoleri amu mzindamo, adachitadi monga momwe adaŵauzira Yezebele. Potsata mawu a m’makalata omwe mkaziyo adaŵatumizira, anthuwo adalengeza za kusala zakudya, ndipo adamuika Naboti pa malo a ulemu. Anthu aŵiri aja adaloŵa nakhala pamaso pa Nabotiyo. Adayamba akuchita umboni pakhamu pa anthu onse kuti: “Nabotiyu adatemberera Mulungu ndiponso mfumu.” Motero anthuwo adamtulutsira kunja kwa mzinda, namponya miyala mpaka kumupha.Pambuyo pake adatumiza mawu kwa Yezebele akuti: “Naboti uja takonza, moti wafa.” Yezebele atangomva zakuti Naboti amponya miyala ndipo wafa, adakauza Ahabu kuti: “Dzukani, katengeni munda wa mpesa uja umene Naboti Myezirele, ankakukanizani kugula. Nabotiyo sali moyonso ayi, wafa.” Ahabu atangomva kuti Naboti wafa, adanyamuka napita ku munda wa mpesa wa Naboti Myezirele, nautenga kuti ukhale wake. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 5: 2-3AB, 4B-6A, 6B-7 Inu Chauta, Mulungu wanga, imvani kulira kwanga (2b). Imvani mawu anga, Inu Chauta, mverani kusisima kwanga. Imvani kulira kwanga, Inu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga. Inu Chauta, Mulungu wanga, imvani kulira kwanga. M’maŵa, Inu Chauta, mumamva mawu anga. M’maŵa ndimapemphera kwa Inu, Ndi kudikira kuti mundiyankhe. Inu sindinu Mulungu wokondwerera machimo. Simufuna zoipa pamaso panu. Inu Chauta, Mulungu wanga, imvani kulira kwanga. Anthu onyada sangathe kuwonekera pamaso panu. Inu mumadana ndi anthu onse ochita zoipa. Inu mumaŵaononga anthu olankhula zonama. Inu Chauta mumanyansidwa nawo Anthu a bodza ndi opha anzawo. Inu Chauta, Mulungu wanga, imvani kulira kwanga. Aleluya: (Salimo 119: 105) Mawu anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga, Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU WOYERA 5:38-42 Yesu adati kwa ophunzira ake: “Mudamva kuti anthu akale aja adaŵalamula kuti: ‘Diso kulipa diso, dzino kulipa dzino.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti: munthu woipa osalimbana naye. Ngati munthu akumenya pa tsaya la ku dzanja lamanja, upereke linalonso. Munthu akakuzenga mlandu nafuna kukulanda malaya ako, umulole atengenso ndi mkanjo wako womwe. Munthu akakukakamiza kuyenda naye mtunda umodzi, uyende naye mitunda iŵiri. Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akafuna kubwereka kanthu kwa iwe, usamkanize.” Mthenga wa Ambuye