LOLEMBA LA MULUNGU WA 12 PACHAKA
Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Steven Limbani Kassim for 22 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
22 JUNE, 2026 Mulungu wachinai wamasalimo LOLEMBA LA MULUNGU WA 12 PACHAKA MAU OYAMBA, MAU A MBUKU LA LACHIWIRI LA MAFUMU 17:5-8,13-15a,18 Nthaŵi imeneyo, Salimanezere, mfumu ya ku Asiriya, adathira nkhondo dziko la Israele, nakafika ku Samariya, nkukauzinga mzindawo ndi zithando za nkhondo zaka zitatu. Chaka chachisanu ndi chinayi cha ufumu wa Hoseya, mfumu ya ku Asiriya idagonjetsa Samariya, ndipo idatenga Aisraele kuŵachotsa kwawo kupita nawo ku Asiriya. Idaŵakhazika ena ku mzinda wa Hala, ena kufupi ndi mtsinje wa Habori m’dera la Gozani, ndipo enanso ku mizinda ya Amedi. Zimenezo zidaoneka chifukwa Aisraele adachimwira Chauta Mulungu wawo, amene adaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, kuŵachotsa m’manja mwa Farawo, mfumu ya ku Ejipito. Aisraelewo ankapembedza milungu ina, ndipo ankayenda motsata miyambo ya anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵapirikitsa pamene ankafika Aisraele. Ankatsatanso miyambo yachilendo imene mafumu ena a Aisraele adali ataiyambitsa. Monsemo Chauta adatuma amithenga ndi aneneri ake ku Israele ndi ku Yuda, okalalika kuti: “Musinthe makhalidwe anu a uchimo, ndipo mumvere Malamulo anga amene ndidaŵapereka kwa makolo anu, kudzera mwa aneneri, atumiki anga.” Koma anthuwo sankamva, adali ouma mitu monga momwe adaliri makolo awo amene sadakhulupirire Chauta Mulungu wawo. Iwowo adanyoza malamulo a Chauta ndi chipangano cha Chauta chimene Iye adachita ndi makolo awo. Adanyozanso zochenjeza za Chauta. Nchifukwa chake Chauta adakwiya nawo kwambiri Aisraele, ndipo adaŵachotsa osafuna kuŵaonanso. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adatsalako, kupatula a fuko la Yuda okha. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 60: 3, 4-5, 12-13 Tithandizeni ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutiyankhe, Inu Ambuye (7b). Inu Mulungu, mwatitaya ife, mwatiwonongera otiteteza. Mwatikwiyira, tibwezeni mwakale. Tithandizeni ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutiyankhe, Inu Ambuye. Inu mwagwedeza dziko ndi chivomezi, Inu mwaling’amba. Konzani ming’alu yake, pakuti likugwedezeka koopsa, Inu mwalola anthu anu kuti aone mavuto aakulu. Mwatipatsa vinyo wachilango kuti timwe, Ndipo tikudzandira naye. Tithandizeni ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutiyankhe, Inu Ambuye. Si wina ayi, koma ndinu Mulungu amene mwatitaya, Ndinu Mulungu amene mwaleka kuperekeza ankhondo athu. Tithandizeni kulimbana ndi adani athuwo, Pakuti chithandizo cha munthu nchopanda pake. Tithandizeni ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutiyankhe, Inu Ambuye. Aleluya: (Aheberi 4: 12) Paja mawu a Mulungu ndi a moyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m’mitima mwawo, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYU 7:1-5 Yesu adati kwa ophunzira ake: ”Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Mmene inu mumaweruzira ena, ndi mmenenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu. Umaoneranji kachitsotso kamene kali m’maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m’maso mwako momwe? Ungamuuze bwanji mbale wako kuti: ‘Taima ntakuchotsa kachitsotso kali m’maso mwakoka!’ Pamene m’maso mwako momwe muli chimtengo? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m’maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m’maso mwa mbale wako.” Mthenga wa Ambuye