Loweluka la Mulungu wa 10 pachaka - MTIMA WOSAIPA KONSE WA MARIA
Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Gift Phiri, OFM for 13 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.
Share to WhatsAppMau a Mulungu a Lero
13 JUNE 2026 MTIMA WOSAIPA KONSE WA MARIA MAU OYAMBA A MBUKU LA MNENERI YESAYA 61:9-11 Ana ao adzakhala odziŵika pakati pa anthu a mitundu ina, zidzukulu zaonso zidzakhala zotchuka pakati pa anthu onse. Aliyense woŵaona adzazindikira kuti ndi anthu amene Ine Chauta ndidaŵadalitsa.”Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali. Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: 1 SAMUELI 2:1,4-5,6-7,8abcd Mtima wanga ukutamanda Ambuye Mpulumutsi wanga “Mtima wanga ukukondwa chifukwa cha zimene Chauta wandichitira, Ndikuyenda ndi mdidi chifukwa cha Chauta. Pakamwa panga pakula nkuseka adani anga monyodola. Ndakondwa kwambiri chifukwa mwandipulumutsa. Mtima wanga ukutamanda Ambuye Mpulumutsi wanga Ankhondo amphamvu mauta ao athyoka, koma anthu ofooka avala dzilimbe. Anthu amene kale adaali okhuta, tsopano akusuma, koma amene kale adaali ndi njala, tsopano akukhuta. Chumba chabala ana asanu ndi aŵiri, koma wobereka ana ambiri watsala yekha. Mtima wanga ukutamanda Ambuye Mpulumutsi wanga Chauta amadzetsa imfa ndipo amabwezeranso moyo, amatsitsira ku manda, ndipo amaŵatulutsakonso. Chauta amasaukitsa ndipo amalemeretsa, amatsitsa ndipo amakweza. Mtima wanga ukutamanda Ambuye Mpulumutsi wanga Amakweza osauka kuŵachotsa pa fumbi, amachotsa anthu osoŵa pa dzala, amaŵakhazika pamodzi ndi akalonga, amaŵapatsa mpando waulemu. Mtima wanga ukutamanda Ambuye Mpulumutsi wanga Aleluya: (Luka 2: 19) Ndinu wodala, Pakuti madasunga zonsezo namazilingalira mumtima mwanu. Aleluya. MTHENGA WABWINO WA LUKA 2:41-51 Makolo a Yesu ankapita ku Yerusalemu chaka ndi chaka ku chikondwerero cha Paska. Pamene Yesu anali ndi zaka khumi ndi ziŵiri, iwo adapita kumeneko monga adaazoloŵera. Masiku a chikondwererocho atatha, adanyamuka kumabwerera kwao, mnyamata uja Yesu nkutsalira ku Yerusalemu, makolo ake osadziŵa. Iwo ankayesa kuti ali pamodzi ndi anzao aulendo, choncho adayenda ulendo wa tsiku limodzi. Tsono adayamba kumufunafuna pakati pa abale ao ndi abwenzi ao. Ataona kuti sakumpeza, adabwerera ku Yerusalemu akumufunafuna ndithu.Patapita masiku atatu, adampeza m'Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera mau ao, ndi kumaŵafunsa mafunso. Onse amene ankamva mau ake, ankadabwa ndi mayankho ake anzeru. Pamene makolo ake adamuwona, adadabwa, ndipo mai wake adamufunsa kuti, “Mwana iwe, watisautsiranji chotere? Ine ndi bambo wako tavutika nkukufunafuna.” Koma Yesu adati, “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kani simumadziŵa kuti ndiyenera kupezeka m'nyumba ya Atate anga?” Koma iwo sadamvetse zimene adaŵayankhazo. Tsono Yesu adabwerera nawo pamodzi, nafika ku Nazarete, ndipo ankaŵamvera. Mai wake ankasunga zonsezi mumtima mwake. Mthenga wa Ambuye