LOWERUKA LA MULUNGU WA 11 PACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Charles Duncan for 20 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Charles Duncan·20 June 2026·17:38·2 views
Ordinary Time
BUKU LACHIWIRI LA MBIRI 24:17-25 SALIMO 89: 4-5, 29-30, 31-32, 33-34 MATEYU WOYERA 6:24-34

Mau a Mulungu a Lero

20 JUNE, 2026 LOWERUKA LA MULUNGU WA 11 PACHAKA MAU WOYAMBA A MBUKU LACHIWIRI LA MBIRI 24:17-25 ‭‬ Yehoyada atamwalira, akalonga aku Yuda adabwera kudzalambira mfumu, ndipo mfumu idaŵamvera. Anthu adasiya Nyumba ya Chauta, Mulungu wa makolo awo, namatumikira mafano. Tsono mkwiyo wa Mulungu udagwera anthu aku Yuda ndi amu Yerusalemu, chifukwa cha tchimo lawoli. Komabe Mulungu adatuma aneneri pakati pawo kuti anthuwo aŵabwezere kwa Chauta. Koma aneneriwo ataŵadzudzula, anthuwo sadasamaleko ayi. Tsono mzimu wa Mulungu udaloŵa mwa Zekariya, mwana wa wansembe, Yehoyada. Iye adaimirira pakati pa anthu naŵauza kuti: “Chauta akufunsa kuti: ‘Chifukwa chiyani mukuchimwira malamulo a Chauta? Ndithu simudzapindula kanthu?’“ Koma anthuwo adamuchita chiwembu, ndipo mfumu italamula, adamponya miyala m’bwalo la Nyumba ya Chauta. Motero Mfumu Yowasi sadakumbukire zabwino zimene Yehoyada, bambo wake wa Zekariya, adamuchitira, koma adapha mwana wake. Ndipo pamene ankafa, mwanayo adati: “Chauta apenye, ndipo abwezere chilango.” Pa kutha kwa chaka, gulu la nkhondo la ku Siriya lidadzamenyana ndi Yowasi. Adabwera ku Yuda ndi ku Yerusalemu, napha akazembe onse a anthu pakati pa anthuwo. Ndipo adatumiza zofunkha zawo zonse kwa mfumu ya ku Damasiko. Ngakhale gulu la nkhondo la ku Siriya lidadza ndi anthu ochepa, Chauta adapereka m’manja mwawo gulu lalikulu kwambiri la ankhondo, chifukwa chakuti anthuwo adali atasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao. Umu ndimo m’mene anthu aku Siriya adalangira Yowasi. Asiriya aja atamusiya wovulazidwa kwambiri, anyamata ake adamuchita chiwembu, chifukwa cha magazi a mwana wa Yehoyada, wansembe uja, ndipo adamphera pabedi pake. Motero iyeyo adafa. Ndipo adamuika m’manda mu mzinda wa Davide, koma sadamuike m’manda a mafumu. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 89: 4-5, 29-30, 31-32, 33-34 Ndidzamkonda mtumiki wanga nthaŵi zonse ndi chikondi chosasinthika (29a). Ndachita chipangano ndi wosankhidwa wanga, Ndalumbira kwa Davide, mtumiki wanga, kuti: ‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya, Ndidzasungira mibadwo yonse mpando wako wa chifumu.’ Ndidzamkonda mtumiki wanga nthaŵi zonse ndi chikondi chosasinthika. Ndidzamkonda nthaŵi zonse ndi chikondi changa chosasinthika, Chipangano changa ndi iye sichidzaphwanyika. Ndidzakhazikitsa zidzukulu zake pa mpando wachifumu, Mpaka muyaya, ndipo ufumu wake Udzakhala waukulu ngati mlengalenga. Ndidzamkonda mtumiki wanga nthaŵi zonse ndi chikondi chosasinthika. Koma ngati ana ake asiya lamulo langa, Ndipo satsata malangizo anga, ngati aphwanya malamulo anga, Ndipo sasunga malangizo anga, Ndidzaŵalanga ndi ndodo, chifukwa cha zolakwa zawo. Ndidzamkonda mtumiki wanga nthaŵi zonse ndi chikondi chosasinthika. Ndidzaŵakwapula ndi zikoti chifukwa cha machimo awo. Koma Davide sindidzamchotsera chikondi changa chosasinthika, Sindidzakhala wosakhulupirika kwa iye. Ndidzamkonda mtumiki wanga nthaŵi zonse ndi chikondi chosasinthika. Aleluya: (2 Akorinto 8: 9) Mukudziŵa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale adali wolemera, adakhala mphaŵi chifukwa cha inu, kuti ndi umphaŵi wakewo, inu mukhale olemera, Aleluya. MTHENGA WABWINO WA MATEYU WOYERA 6:24-34 Yesu adati kwa ophunzira ake: “Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi, nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma. Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadya chiyani, kapena mudzamwa chiyani, kapena thupi lanu, kuti mudzavala chiyani. Kodi suja moyo umaposa chakudya? Kodi suja thupi limaposa zovala? Onani mbalame za mlengalenga. Izo sizifesa kapena kukolola, kapena kututira mu nkhokwe ayi. Komabe Atate anu a Kumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu a mtengo wapatali kuposa mbalame? Ndani mwa inu, ndi maganizo a nkhaŵa, angathe kuwonjezera ngakhale tsiku limodzi pa moyo wake? Ndipo mumaderanji nkhaŵa ndi zovala? Onani maluŵa aku thengo m’mene amakulira. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu ayi. Komatu kunena zoona, ngakhale Mfumu Solomoni yemwe, mu ulemerero wake wonse, sadavale zokongola kulingana ndi limodzi lomwe mwa maluŵa ameneŵa. Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wa ku thengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu? Nchifukwa chake musamade nkhaŵa nkumanena kuti: ‘Tidzadya chiyani? Tidzamwa chiyani? Tidzavala chiyani?’ Paja zimenezi amazifunafuna ndi anthu akunja. Atate anu a Kumwamba amadziŵa kuti mukuzisoŵa zonsezi. Koma inu, yambani mwafunafuna Ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso. Motero musadere nkhaŵa za maŵa. Za maŵa nzamaŵa. Tsiku liri lonse liri ndi zovuta zake zokwanira.” Mthenga wa Ambuye