LOWERUKA LA MULUNGU WA 8 PACHAKA

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Maxwell Kubalasa for 30 May 2026. Liturgical reflection: YUDA 17,20b-25.

Share to WhatsApp
Fr. Maxwell Kubalasa·30 May 2026·16:39·4 views
Ordinary Time
YUDA 17,20b-25 SALIMO 63: 2, 3-4, 5-6 MARKO 11:27-33

Mau a Mulungu a Lero

30 MAY, 2026 LOWERUKA LA MULUNGU WA 8 PACHAKA MAU OYAMBA; MAU A MKALATA YA YUDA 17,20b-25 Inu okondedwa, muzikumbukira mawu amene Atumwi a Ambuye athu, Yesu Khristu, adaneneratu. Koma inu okondedwa, muzithandizana kuti uzikulirakulira moyo wanu, umene udakhazikika pa maziko a chikhulupiriro chanu changwiro. Muzipemphera ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Khalani m’chikondi cha Mulungu, podikira moyo wosatha, umene Ambuye athu, Yesu Khristu, adzakupatseni mwa chifundo chake. Pali ena amene ali okayika, amenewo muziŵachitira chifundo. Koma ena muŵapulumutse pakuŵalanditsa ku moto. Enanso muŵachitire chifundo, koma mwamantha, muzidana ngakhale ndi chovala chawo chomwe choipitsidwa ndi machimo. Akhale ndi ulemerero Iye amene angathe kukusungani, kuti mungagwe m’machimo, amene angathenso kukufikitsani pamaso pa ulemerero wake, muli okondwa ndi opanda chilema konse. Mulungu, amene Iye yekha ndiye Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Khristu Ambuye athu, akhale ndi ulemerero, ukulu, mphamvu ndi ulamuliro, isadayambe konse nthaŵi tsopano, ndi mpaka muyaya. Amen. ‭‭Mau a Ambuye‬‬‬‬ NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 63: 2, 3-4, 5-6 Mtima wanga uli ndi ludzu lofunafuna Inu, Ambuye (2b). Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, Thupi langa likulakalaka Inu Ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi. Mtima wanga uli ndi ludzu lofunafuna Inu, Ambuye. Ndikukhumbira kukuonani m’malo anu oyera Ndi kuona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu. Ndidzakutamandani, Chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo. Mtima wanga uli ndi ludzu lofunafuna Inu, Ambuye. Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga. Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera. Mudzandikhutitsa ndi zonona, Ndipo ndidzakutamandani ndi mawu osangalala. Mtima wanga uli ndi ludzu lofunafuna Inu, Ambuye. Aleluya: (Akolose 3: 16a, 17c) Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu m’mitima mwanu; chiri chonse chimene mungachite, muchichite m’dzina la Ambuye Yesu, ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye, Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MARKO 11:27-33 Yesu adafika ku Yerusalemu. Tsono pamene Iye ankangodziyendera m’Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo, pamodzi ndi akulu a Ayuda adadzamufunsa kuti: “Kodi ulamuliro woti uzichitira zimenezi udauzitenga kuti? Ndani adakupatsa mphamvu zimenezi?” Yesu adati: “Nanenso ntakufunsani funso limodzi. Mukandiyankha, ndiye ndikuuzani kumene ndidatenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi. Kodi Yohane kuti azibatiza, mphamvu zake adazitenga kwa yani, kwa Mulungu kapena kwa anthu? Tandiyankhani.” Iwo aja adayamba kutsutsana nkumati: “Tikati adazitenga kwa Mulungu, Iyeyu anena kuti: ‘Nanga bwanji tsono simudamkhulupirire?’ Komanso tikati adazitenga kwa anthu, apo ndiye ayinso.” Adatero chifukwa choopa anthu, pakuti anthu onse ankati Yohane adalidi mneneri weniweni. Ndiye adangomuyankha Yesuyo kuti: “Khaya, ife sitikudziŵa.” Apo Iye adati: “Nanenso tsono sindikuuzani kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.” Mthenga wa Ambuye