LOWERUKA LAMULUNGU WA 29 PACHAKA (II)

Watch this Catholic homily in Chichewa by Fr. Medrick Mlava, DP for 24 October 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Fr. Medrick Mlava, DP·24 October 2026·13:51
Ordinary Time
MAU OYAMBA : AEFESO 4:7-16 SALIMO 122: 1-2, 3-4AB, 4CD-5 MTHENGA WABWINO : LUKA 13:1-9

Mau a Mulungu a Lero

24 OCTOBER, 2026 LOWERUKA LAMULUNGU WA 29 PACHAKA (II) MAU OYAMBA; MAU A MKALATA YA PAULO KWA KWA AEFESO 4:7-16 Okondedwa, aliyense wa ife adalandira mphatso yakeyake yaulere, molingana ndi m’mene Khristu amaperekera mphatso zake. Paja mawu a Mulungu akuti: “Pamene adakwera Kumwamba, adatenga chigulu cha am’ndende, ndipo adagaŵira anthu mphatso.” Tsono mawu akuti adakwera tanthauzo lake nchiyani? Ndiye kuti poyamba adatsikira pansi penipeni pa dziko. Iye amene adatsika, ndi yemweyo amene adakwera, nabzyola Kumwamba konse, kuti zinthu zonse zikhale zodzaza ndi Iye. Iyeyu ndiye amene adapereka mphatso kwa anthu. Mphatso zake zidali zakuti, ena akhale Atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yawo idali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu, kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu. Motero potsiriza, tonse tidzafika ku umodzi umene umapezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo tidzakhwima ndithu, ndi kufika pa msinkhu wathunthu wa Khristu. Sitidzakhalanso ngati ana akhanda ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, ndiponso otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya zophunzitsa za anthu onyenga, amene amasocheretsa anthu ndi kuchenjera kwawo. Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu, umene umalamula thupi lonse, ndi kulilumikiza pamodzi ndi mfundo zake zonse. Motero chiwalo chiri chonse chimagwira ntchito yake moyenera, ndipo thupi lonse limakula ndi kudzilimbitsa ndi chikondi. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 122: 1-2, 3-4AB, 4CD-5 Tiyeni tipite mokondwera ku Nyumba ya Chauta (1). Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti: “Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.” Mapazi athu akhala akuima mkati mwa zipata zako, Iwe Yerusalemu. Tiyeni tipite mokondwera ku Nyumba ya Chauta. Yerusalemu adamangidwa bwino, Zigawo zake zonse nzogwirizana pamodzi. Kumeneko kumapita mafuko onse, anthu ake a Chauta. Tiyeni tipite mokondwera ku Nyumba ya Chauta. Monga momwe adalamulira Israele Kuti akayamike dzina la Chauta. Kumeneko adaikako mipando yaufumu yoweruzira, Mipando yake ya banja la Davide. Tiyeni tipite mokondwera ku Nyumba ya Chauta. Aleluya: (Ezara 33: 11) Ambuye Chauta akuti: Ine ndemwe, sindikondwa ndikaona munthu woipa alikufa: ndikadakonda kuti aleke kuchimwako kuti akhale ndi moyo, _Aleluya. MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA 13:1-9 Anthu ena adadza kwa Yesu, nayamba kumusimbira za Agalileya amene Pilato adalamula kuti aphedwe, pamene iwo ankapereka nsembe zawo kwa Mulungu. Tsono Yesu adaŵafunsa kuti: “Kodi mukuyesa kuti Agalileyawo adali ochimwa koposa Agalileya ena onse, popeza kuti adaphedwa motere? Iyayi, koma mukapanda kutembenuka mtima, inunso mudzaonongedwa ngati iwo aja. Nanga anthu aja 18, amene nyumba yosanja idaŵagwera ku Silowamu nkuŵapha? Kodi mukuyesa kuti iwowo adali ophwanya malamulo koposa anthu ena onse okhala m’Yerusalemu? Iyayi, koma mukapanda kutembenuka mtima, inunso mudzaonongedwa ngati iwo aja.” Yesu adaŵaphera fanizo, adati: “Munthu wina adali ndi mkuyu wobzalidwa m’munda wake wa mpesa. Adakafunamo zipatso, koma osazipeza. Tsono adauza wosamala mundawo kuti: ‘Papita zaka zitatu tsopano ndikufuna zipatso mu mkuyu uwu, koma osazipeza. Udule tsono. Ukugugitsiranji nthaka?’ Koma iye adati: ‘Ambuye, baulekani chaka chino chokha. Ndiukumbira pa tsinde nkuuthira manyowa. Ukadzabala zipatso chaka chamaŵa, zidzakhala bwino. Koma ukakapanda kubala, apo mudzaudule.’ Mthenga wa Ambuye