LOWERUKA LAMULUNGU WA 9 PACHAKA (II)

Watch this Catholic homily in Chichewa by Rev. Deacon Justin Malewezi Jnr for 6 June 2026. Liturgical reflection: Ordinary Time.

Share to WhatsApp
Rev. Deacon Justin Malewezi Jnr·6 June 2026·13:21·4 views
Ordinary Time
KALATA YACHIWIRI YA PAUL KWA TIMOTEO 4:1-8 SALIMO 71: 8-9, 14-15AB, 16-17, 22 MARKO 12:38-44

Mau a Mulungu a Lero

6 JUNE, 2026 LOWERUKA LAMULUNGU WA 9 PACHAKA (II) ‭‭‬‬‬‬‬ MAU OYAMBA, MAU A MKALATA YACHIWIRI YA PAUL KWA TIMOTEO 4:1-8 Wokondedwa, pamaso pa Mulungu, ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza anthu onse, amoyo ndi akufa omwe, ndipo potamanda kubwera kwake ndi ufumu wake wa Khristuyo, ndikukulamula ndithu kuti uzilalika mawu a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sali kuŵafuna. Utsutse anthu zolakwa zawo, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni. Paja nthaŵi idzafika pamene anthu adzakana chiphunzitso choona. M’malo mwake, chifukwa cholakalaka kumva zoŵakomera zokha, adzadzisankhira aphunzitsi ochuluka omaŵauza zimene iwo akufuna. Adzafulatira choona, osafunanso kuchimva, ndipo adzangotsata nthano chabe. Koma iwe, uzikhala maso pa zonse, pirira pa zoŵaŵa, gwira ntchito yolalika Uthenga Wabwino. Kwaniritsa udindo wako mosamala. Kunena za ine, moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthaŵi yafika kuti ndinyamuke ulendo wanga wochoka m’moyo uno. Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liŵiro, ndasunga chikhulupiriro. Chonditsalira tsopano ndi chakuti ndikalandire mphotho imene ikundidikira. Mphothoyo ndi yakuti Ambuye, amene ali Woweruza molungama, adzandilungamitsa pa tsiku la chiweruzo. Ndipo mphotho imeneyi sadzangopatsa ine ndekha ayi, komanso ena onse amene mwachikondi akudikira kuti Ambuyewo adzabwerenso. Mau a Ambuye NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 71: 8-9, 14-15AB, 16-17, 22 Inu Chauta, pakamwa panga padzaimba za chipulumutso chanu (15ab). Pakamwa panga pakutamanda Inu, Pakulalika ulemerero wanu tsiku lonse. Musanditaye nthaŵi ya ukalamba wanga, Musandisiye ndekha pamene mphamvu zanga zatha. Inu Chauta, pakamwa panga padzaimba za chipulumutso chanu. Koma ine ndidzakhulupirira Inu nthaŵi zonse, Ndipo ndidzapitirizabe kukutamandani. Pakamwa panga padzalankhula tsiku lonse Za ntchito zanu zolungama ndi za chipulumutso chanu. Inu Chauta, pakamwa panga padzaimba za chipulumutso chanu. Ndidzabwera ndi uthenga Wofotokoza za ntchito zamphamvu za Chauta. Ndidzatamanda chilungamo chanu chokha. Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga, Ndipo ndikulalikabe ntchito zanu zodabwitsa. Inu Chauta, pakamwa panga padzaimba za chipulumutso chanu. Ndidzakutamandaninso ndi zeze, Inu Mulungu wanga, Chifukwa cha kukhulupirika kwanu. Ndidzaimba nyimbo zoyamika Inu ndi pangwe, Inu Woyera wa Israele. Inu Chauta, pakamwa panga padzaimba za chipulumutso chanu. Aleluya: (Mateyo 5: 3) Ngodala anthu amene ali osauka mu mtima mwawo, pakuti Ufumu wa Kumwamba ndi wawo, Aleluya. MTHENGA WA AMBUYE MONGA ADALEMBERA MARKO 12:38-44 Pamene Yesu ankaphunzitsa, adati: “Chenjera nawoni aphunzitsi a Malamulo. Amakonda kuyenda atavala mikanjo yaitali, namafuna kuti anthu aziŵapatsa moni pa misika. Amakonda mipando yaulemu kwambiri m’nyumba za mapemphero. Akapita ku maphwando, amakakhala pa malo a ulemu. Koma amaŵadyera chuma chawo amayi amasiye, nkumapemphera mapemphero ataliatali monyengezera. Ndithu anthu ameneŵa adzalangidwa koposa.” Tsiku lina Yesu adakhala pansi kuyang’anana ndi bokosi loponyamo ndalama zopereka ku Nyumba ya Mulungu. Ankayang’anitsitsa m’mene anthu ankaponyera ndalama zawo. Anthu ambiri a chuma ankaponyamo ndalama zambiri. Koma padafika mayi wina wamasiye, wosauka. Iyeyu adangoponyamo tindalama tiŵiri. Tsono Yesu adaitana ophunzira ake naŵauza kuti: “Ndithu ndikunenetsa kuti mayi wamasiye wosaukayu waponyamo koposa anthu ena onseŵa, amene aponya ndalama m’bokosimu. Chifukwa ena onseŵa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma mayiyu, mwa umphaŵi wake, waponyamo zonse zimene adali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.” Mthenga wa Ambuye